07/06/2026
Kampani ya H.Adam Wholesalers yati ngakhale nyengo yazachuma sili bwino iwo ayetsetsabe kupitilidza kuthandidza masewero a mpira wamiyendo ku chigawo chakummawa,Mkulu owona za Malonda ku kampani yi Oster Banda ndi amene wanena izi loweruka pa 6 June 2026 pa bwalo la Vision ku Ntaja m'boma la Machinga pa masewero otsekulira ligi ya Durata Batteries Eastern Region Football Association.
"Tikufuna kuti ikhale ligi yopambana ngati pangakhale kusamvetsetsana,mbali zonse zikhalirane pansi kuti mpira upindure" Anatero Banda.
Mawu ake wapampando wa Bungwe la Eastern Region Football Association Issah Brahim anati zotsamwitsa zonse zomwe anali nazo chaka chatha azikonza ndipo chaka chino ligiyi ikhale yapamwamba. Brahim anathokonzanso kampani ya H.Adam kamba kobweranso chaka chino kuzathandiza ligi yi zomwe zawapatsa chilimbikitso.
Daud ntanthiko yemwe anaimilira Bungwe la FAM anati,ngati bungwe iwo ndi othokoza Kampani ya H.Adam ndipo wapempha Kampaniyi kuti ithandizenso ligi yachiwiri ya mchigawochi.
Masewero omwe anali pa tsikuli anakomera anyamata a Ntaja Rangers omwe anagonjetsa Nselema United ndi zigoli zitatu kwa chimodzi.
Kampani ya H.Adam Wholesalers ikuthandiza ligi ya mchigawo chakumawa ndi ndalama zokwana 36 million kwacha .
Wolemba: Williams Chande (07/06/2026)
.8Mhz