23/05/2025
*FLAMES IDZAYAMBA KUKUMANA NDI LESOTHO KU COSAFA.*
```
◼️Timu yampira wamiyendo yadziko lino ya Flames idzakumana ndi Lesotho pa 05 June m'masewero ake oyamba a mugulu B mumpikisano wa chaka chino wa COSAFA m'dziko la South Africa.
Izi ndikutsatira mndandanda wa masewero omwe bungwe la Council of Southern Africa Football Associations (COSAFA) latulutsa.
Malingana ndi mndandandawu, Flames idzasewera masewero ake achiwiri pa 08 June pomwe idzakumane ndi Namibia pabwalo la Toyota isanasewere masewero ake otsiriza mugululi ndi Angola pa 10 June pabwalo lomweli la Toyota.
Ndipo kenako, amene atsirize pamwamba mugululi [B] adzakumana ndi opambana mugulu C momwe muli matimu monga Morocco, Madagascar ndi Eswatini.
Malawi inapita kotsiriza kumpikisano wa COSAFA mchaka cha 2023 komwe inafika ndime ya Semifainolo koma inagonja ndi Lesotho kudzera pamapenate isanagonjenso pamapenate ndi South Africa m'masewero ofuna kupeza timu yomalizira panambala yachitatu.
Chaka chatha, timu yadziko linoli sinapite kukatenga nawo mbali mumpikisanowu kutsatira imfa ya yemwe anali wachiwiri kwa Mtsogoleri wa dziko lino Dr. Saulos Klaus Chilima.
```
*JACK MA ONLINE 📖✍️😎*