OMAH Publications

OMAH Publications Let's Grow Together As World And As Family πŸŒπŸŒŽπŸŒπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡Ό

26/07/2025
UDF NOMINATIONS PAPER UPDATE  LILONGWE Lero pa 26 July chaka cha 2025 wolemekezeka a Atupele Muluzi lero pamodzi ndi aku...
26/07/2025

UDF NOMINATIONS PAPER UPDATE LILONGWE

Lero pa 26 July chaka cha 2025 wolemekezeka a Atupele Muluzi lero pamodzi ndi akulu akulu komanso otsatira chipani cha UDF ali ku BICC mu mzinda wa Lilongwe komwe akuyembekezeka kukapeleka zikalata zawo ku bungwe loyendetsa Chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) zowasonyeza kuti akufuna kudzapikisana nawo pa mpando wa utsogoleri wa dziko pa 16 September chaka chino

aMuluzi akuyembekezekaso kudziwitsa mtundu wa aMalawi pamodzi ndi otsatira chipani cha UDF za yemwe amusankha kukhala wachiwiri wawo mu ulendo wawo

Ili ndi gawo loyamba lomwe Malawi Electoral Commission imalandira zikalata za omwe akufuna kupikisana nawo pa mpando wa utsogoleri wa dziko ndikuziunika ngati zili ndi zoziyeneleza

Omah Alick
26/07/2025

Zathapo apano DPP yatulutsano Wachiwiri wawo zomwe anthu ambiri amadikira kuti amve, Ndipo wachiwiriyo ndi Dr Jane Ansa ...
25/07/2025

Zathapo apano DPP yatulutsano Wachiwiri wawo zomwe anthu ambiri amadikira kuti amve, Ndipo wachiwiriyo ndi Dr Jane Ansa

Ngakhale anthu ena akunyinyilika kuti sakugwilizana nazo komabe ena ali ndi chimwemwe ndi chisangalaro kuti Professor Arthur Peter Mutharika wasankha munthu oyenera kuthandizana naye kuyendetsa naye boma

25/07/2025
Omah Alick

Anthu ali ku BICC mu mzinda wa Lilongwe komwe mtsogoleri wa chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) Professor Art...
25/07/2025

Anthu ali ku BICC mu mzinda wa Lilongwe komwe mtsogoleri wa chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) Professor Arthur Peter Mutharika akukapeleka ma pepala osonyeza kuti apikisana nawo pa Chisankho cha Patatu ngati mtsogoleri wa dziko komanso komwe akadziwitse aMalawi munthu yemwe akuyenera kukhala wachiwiri wawo pambuyo pamgwirizano wawo ndi chipani cha Afford

25/07/2025
Omah Alick

Ku Lilongwe pa Manda a Area 36 kuseli kwa nsewu wa M1 Pafupi ndi mtawa Lodge kwapezeka abambo awiri ataotchedwa,  koma o...
19/08/2024

Ku Lilongwe pa Manda a Area 36 kuseli kwa nsewu wa M1 Pafupi ndi mtawa Lodge kwapezeka abambo awiri ataotchedwa, koma omwe achita izi sakudziwika. Komanso anthu omwalirawa sakudziwika kuti ndi akuti

Source : (Omah Alick)

02/05/2024

Mtsogoleri wa chipan chimene changobadwa kumene cha Peoples Development Party (PDP) a Kondwan Nankhumwa wafotokoza chifukwa chomwe wasankhira mbalame ya chiomba nkhanga kukhala chizindikiro cha chipani chake

A Nankhumwa ati anasankha chiomba nkhanga kukhala chizindikiro cha chipanichi pa zifukwa zingapo

A Nankhumwa ati mbalame ya chiomba nkhanga ndi mbalame imene imadya chakudya kapena nyama yoti yapha yokha osati kudikira wina aiphere komaso ati mbalameyi ndi imodzi mwa mbalame zimene zimauluka mmwamba kwambiri kuposa mbalame zina

Anankhumwa ayankhula izi pamene amakhanzikitsa chipani chawo chomwe changobadwa kumene cha PDP ku Golden Peacock mu mzinda wa Blantyre

Wolemba (Omah Alick 02/05/24)

02/05/2024

Anthu ochuluka asonkhana ku golden peacock mu mzinda wa Blantyre komwe akukachitira umboni kukhazikitsidwa kwa chipan cha Peoples Development Party (PDP) chomwenso mtsogoleri wake ndi ndi membala wakale wa chipan cha Democratic Progressive Party (DPP) a Kondwan Nankhumwa

Wolemba (Omah Alick 02/05/24)

Zithunzi :MIJ Online

02/05/2024

Mtsogoleri wa dziko lino Dr. Lazarus Chakwera akonza mphwando lomwe adye limodzi ndi atolankhani a Mdziko muno ku nyumba ya chifumu mu mzinda wa Lilongwe mmawa wa lero pa 02 April, 2024 lomwenso Lori tsiku lokumbukira atolankhani pachingelezi limatchedwa (World Press Day)

Wolemba:( Omah Alick 02/05/24)

Rest in Peace star πŸ’”πŸ’”πŸ‡²πŸ‡Ό
02/05/2024

Rest in Peace star πŸ’”πŸ’”πŸ‡²πŸ‡Ό

Wolemekezeka Dr. Kondwan Nankhumwa akhala akuyankhula ku mtundu wa aMalawi lero mmawa uno kuyambira nthawi ya 9 O'clock ...
02/05/2024

Wolemekezeka Dr. Kondwan Nankhumwa akhala akuyankhula ku mtundu wa aMalawi lero mmawa uno kuyambira nthawi ya 9 O'clock kudzera pa wailesi za mphepo, pa kanema komanso pa masamba a mchezo a Zodiak Online. Tiyen tisunge nthawi kuti tisaphonyane nazo

Wolemba(Omah Alick 02/05/24)

Source : Zodiak page

01/05/2024

BERMUDA TRIANGLE
Bermuda ndi chilumba, chimene chili mu Atlantic ocean, pomwe Bermuda triangle ndi kadera kamene kali mkatikati mwa madzi mu Atlantic ocean komwe kadagundikizana ndi chilumba chotchedwa Bermuda, ndipo Bermuda triangle imaoneka mwa ngodya zitatu, malowa ali Kumadzulo cha mkatikati mwa nyanja yaikulu yotchedwa *Atlantic ocean* koma ku mpoto pang'ono kwa nyanjayi, Kuchokera ku Bermuda kukafika ku florida kukhota kukafika ku Poert Rico. moyandikiranako ndithu pang'ono ndi ku Florida.
Bermuda triangle ndi Bermuda island ndi malo awiri osiyana, koma triangle yi idalandira dzina loti Bermuda kuchokera ku anthu omwe amakhala ku Bermuda Island kapena kuti ku chilumba cha Bermuda. potengera kuti malowa ndioyandikana, Malowa amatchedwanso kuti *Hurricane triangle*, komanso amatchedwanso kuti *Devil's Triangle*

Mchifukwa chiyani Malowa amatchedwanso kuti *Devil's triangle*??
Dzina loti *Devils triangle* linaperekedwa ku malowa kamba ka zinthu zoopsa zomwe zakhala zikuchitikirapo.
Malowa pakhala pakumachitika zinthu zowopsa kwambiri. Nyanja ya Atlantic Ocean idatenga gawo lalikulu kwambiri la dziko lapansi, pachifukwa cha ichi nyanjayi pamadutsa ma boat, ma sitima, ngakhale mmalengalenga mwake ndege nazoso zimadutsamo. *Bermuda triangle* pokhala mkatikati mwanyanjayi pakhala pakuchitikira zinthu zodabwitsa ndipo pakhala pakusowa ndege, sitima komanso maboti.
Simbari yonse yanyanjayi pomwe pamachitika zowopsazi ayi, koma kachigawo kochepa chabe kanyanjayi ndipomwe pamachitika zimenezi. Malo amenewo anthu akumeneko anawapasa dzina lokuti Bermuda Triangle Adawapasa dzinalo chifukwa chokuti pamaoneka mwa triangle choncho. Kamalo ka
PakatiKati pa madera atatu a Florida, Bermuda ndi Poert Rico ndipo pamene pamatchedwa kuti pa Bermuda Triangle. Ndege ndi Sitima zakhala zikusowa mosadziwika bwino kuyambira kale kale mpakana Lero lino zimasowabe.
Kodi ndege ndi sitimazi zimasowa mwanjira yanji?
Ndege ikamawuluka m'malengalenga, ikangolowa mbari yaku Bermuda Triangle,

Address

Mangochi

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when OMAH Publications posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share

Category