ZBS Malawi

ZBS Malawi This is zbs malawi page and This pages is for only news

*6 DAYS MISSING. HELP [ kuchokera Ku inbox πŸ“₯ ]*Tithandidzeni kusaka mwanawathu yemwe Ali Ndi dzaka 16. Dzina lake ndi Li...
23/10/2025

*6 DAYS MISSING. HELP [ kuchokera Ku inbox πŸ“₯ ]*

Tithandidzeni kusaka mwanawathu yemwe Ali Ndi dzaka 16. Dzina lake ndi Lidia Malemia ndipo amaphunzira pa sukulu ya High Profile ku Zomba.
Ataweruka ku sukulu Lachisanu adangosiya makope nkuchoka osanena komwe akupita ndipo sadabwelere mpaka tsiku lalero.

*Amene angamuwone chonde atiyimbire phone pa number iyi 0998542900*

*ONLINE BREAKING NEWS REPORTING*πŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌChifukwa cha kugwa kwa Nertwork pano Bungwe la MDF ndilomwe li...
18/09/2025

*ONLINE BREAKING NEWS REPORTING*

πŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡Ό

Chifukwa cha kugwa kwa Nertwork pano Bungwe la MDF ndilomwe likuyang'anila MACRA Osati zomwe akukamba enawo..

Chifukwa chakusuzga kwa Nertwork pasono Wupu wa MDF ndiwo ukudangilila bungwe la MACRA.

*Wakulemba Admin Alick Ndhlovu wa Online Breaking News*βœοΈβœοΈβœοΈβœοΈπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡Ό

* *πŸ‘¨β€πŸ’»βœοΈπŸ‡²πŸ‡Όβš–οΈπŸŒ½πŸ§’ Mneneli wa chipani cha Democratic Progressive (DPP) a Shadreck Namalomba auza nthambi za chitetezo monga ...
18/09/2025

* *πŸ‘¨β€πŸ’»βœοΈπŸ‡²πŸ‡Όβš–οΈπŸŒ½πŸ§’

Mneneli wa chipani cha Democratic Progressive (DPP) a Shadreck Namalomba auza nthambi za chitetezo monga apolisi ndi Army kuti agwire ndi kumanga anthu onse omwe avala zovala za makaka achipani cha DPP ngati angapezeke akuchita chisokonezo kapena ziwawa.

A Namalomba ayankhula izi patsamba lawo la mchezo la Facebook.

"Musavale zovala zamakaka a chipani Cha Dpp mpaka MEC italengeza zosatira" atero anamalomba.

Iwo ati amaliongo ena akufuna kubweretsa chisokonezo ndipo aziti ndi Dpp.

*πŸ’« #(1) ZBS ZIKACHITIKA MUMVERA PANO [email protected]*
πŸ‘¨β€πŸ’»βœοΈπŸ‡²πŸ‡Όβš–οΈπŸ“πŸ“»πŸ“‘πŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡Ό

14/08/2025

*SALIMA*πŸ‘¨β€πŸ’»βœοΈπŸ‡²πŸ‡Όβš–οΈ

Gerald Kapiseni Phiri yemwe akupikisana nawo ngati phungu mdela lapakati pa boma la Salima pansi pa chipani cha MCP wati sakutekeseka ndi anthu ena ponena kuti zitukuko zomwe wapanga zikumupatsa mphavu ndi chikhulupiliro kuti apambanaso.

Iye amayankhula izi atapeleka midada yomwe wamanga pa sukulu ya Primary ya Chingombe mbomali.

Phiri wati wachita zitukuko zomwe, anthu akusangalala nazo ndipo kuti pa 16 September apitilila ndikupekeka zituko kwa anthu adelari.

Mfumu yayikulu Kalonga yati Gerald Kapiseni Phiri ndi mmodzi mwa aphungu omwe achita bwino kwambiri mbomali ndipo kuti ali ndi chikhulupiliro kuti anthu adelari amusankhaso mwezi wa mawa.

Pakadali pano Kapiseni wati mawa ali ndi ulendo omwe ayende ndi anthu omutsatila mderali kuchoka pa ofesi ya chipani cha MCP mbomali kuzungulila delari lonse lapakati pa boma la Salima.

*πŸ’« #(1) ZBS ZIKACHITIKA MUMVERA PANO [email protected]*
πŸ‘¨β€πŸ’»βœοΈπŸ‡²πŸ‡Όβš–οΈπŸ“πŸ“»πŸ“‘πŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡Ό

03/08/2025

500 flowers please

23/07/2025

* *

πŸ‡²πŸ‡ΌβœŠβ€ΌοΈβš’οΈBwalo la Senior Resident Magistrate ku Lilongwe lavomereza pempho la boma losungabe mchitokosi a Felix Magaleta ndi a Adam Tsoka, omwe akuwaganizira milandu ya kuba ndi kupha anthu ku Area 25 ku Lilongwe, kwa masiku asanu ndi awiri pomwe akufuna kuti atsirize kafukufuku.

Utalowa mlanduwu mubwaloli, mbali ya boma inati awiriwa, pa 31 May chaka chino, anaba lamya za m'manja ziwiri za ndalama yokwana K450,000 ku Area 25 munzindawu.

Oyimira mbali ya boma anati Oganiziridwawa anavomera kulondolera apolisi komwe katundu yemwe anaba ali, ndipo iwo afuna nthawi yowonjezera kuti achite zofufuza.

Apa, Senior Resident Magistrate Wanangwa Nyirenda, wati mlandu wakuba lamyazi udzabweraso kubwaloli pa 30 July chaka chino.

Tsopano Oganiziridwawa apita nawo ku bwalo la Principal Resident Magistrate komwe kukhaleso gawo lina la milandu yomwe akuwaganizira.

*πŸ”ΊοΈπŸ”ΊοΈπŸ”ΊοΈπŸ”ΊοΈJ.JπŸ”ΊοΈπŸ”ΊοΈπŸ”ΊοΈπŸ”ΊοΈπŸ”ΉπŸ”ΉπŸ”ΉπŸ”ΉπŸ”ΉπŸ”ΉπŸ”ΉπŸ”ΉπŸ”Ή*
*πŸ”ΉοΈπŸ”ΉPOMPOPOMPOπŸ”Ή*
*βš‘βš‘πŸ“24HRS⚑⚑*
*βš‘βš‘πŸ“NEWS⚑⚑*
*βš‘βš‘πŸ“UPDATE⚑⚑*
*FOLLOW US FOR MORE NEWS*πŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡Όβž–βž–βž–βž–βž–βž–βž–βž–βž–βž–βž–βž–βž–

23/07/2025

*NKHANI*

Katswiri pandale wati mgwilizano womwe apanga achipani cha DPP ndi gulu lomwe likuzitcha kuti (Northern Block) momwe muli zipani zomwe zilibe ngakhale khasala ngopanda pake.

Pulofesa John phiri wati chipani cha DPP chisadalire kuti chingapeze mavoti m'chigawo chaku mpoto chifukwa cha mgwilizano omwe apanga dzulo.

Katswiri anamaliza nkunena kuti mbiri ya DPP chigawo chaku mpoto idada kale kamba koti nthawi yomwe imalamulira palibe chomwe adapanga m'chigawochi.

Phunzitsi wa sukulu ya ukachenjedwe wati anthu aku mpoto adathana nayo DPP kale kale kamba ka monga izi.kuphedwa kwa anthu 21,komaso kubweretsa quoter system yomwe cholinga chake chidale kuthetsa maphunziro mchigawochi.

πŸ“NEWS UPDATE

21/07/2025

*HELLO ALL,*
*NDALANDILA UTHENGA KUCHOKA KU LUMBADZI CLINIC,*
*MUNTHU UYUYU WAGUNDIDWA , KOMA DRIVER WATHAWA ( HIT AND RUN) WAVULALA MMUTU, KOMA SAKUYANKHULA.*

*NGOZI INACHITIKA PA FEMAC , NDIPO GALIMOTO INAMUGUNDAYO YAGWETSA NUMBER PLATE MUKUYIWONAYO.*

*AMENE TIKUMUDZIWA , KAPENA NGATI PALI ACHIBALE AKE UTHENGA NDI UMENEWO.*
*PONYANI MMA GROUP ENA , AROUND LUMBADZI*

21/07/2025

*DOWA*πŸ‘¨β€πŸ’»βœοΈπŸ‡²πŸ‡Όβš–οΈ

Wofalitsa nkhani za polisi m'boma la Dowa Sub Inspector Alice Sitima wati lamulo ligwira ntchito kwa amene apezeke kuti akukhudzidwa ndi ku wotchedwa kwa msika wa Mvera m'bomali.

A Sitima ayankhula izi anthu ena omwe akuganizilidwa kuti ndi asilikali a MDF awotcha msikawu ngati kubwezera pa imfa ya nzawo, Chiswansangu Nyirongo yemwe adamwalira atabayidwa ndi chida chakuthwa ndi mnyamata yemwe wamangidwa poganizilidwa kuti adachita izi, Pemphero Puleti wa zaka 24.

Iwo ati pakadali pano palibe umboni uliwonse wosonyeza kuti asilikali ndi omwe achita izi.

A Sitima ati, pa nthawi yomwe anapita ku msikawu atalandira lipoti, sanawoneko munthu yemwe amawonetsa ndikupereka maganizo kuti ndiye wa wotcha msikawu koma ati kafukufuku ali mkati wokhudza nkhaniyi ndipo wina akepeza akayankha mulandu pa khoti.

*πŸ’« #(1) ZBS ZIKACHITIKA MUMVERA PANO [email protected]*
πŸ‘¨β€πŸ’»βœοΈπŸ‡²πŸ‡Όβš–οΈπŸ“‘πŸ“πŸ“»πŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡Ό

Gmail is email that’s intuitive, efficient, and useful. 15 GB of storage, less spam, and mobile access.

21/07/2025

*ZAUMOYO*πŸ‘¨β€πŸ’»βœοΈπŸ‡²πŸ‡Όβš–οΈ

Akuluakulu pachipatala cha Mponela ku Dowa, ati odwala pachipatalachi akudya kamodzi patsiku, kaamba ka kuvuta kwa zinthu.

Namwino wa pachipatalachi, a Felix Mtuwana, wati anthu omwe ali ndi kuthekera awathandize ndi zofunikira kuti odwala adzikwanitsa kudya katatu ngati momwe zimayenera kukhalira nthawi zonse.

Iwo apereka pempholi pomwe nzika ya m'boma la Dowa, yomwe pano imakhala m'dziko la United States of America, a Phillipina Phiri Msiska, anapereka katundu osiyana siyana mzipinda zonse za odwala pachipatalachi, za ndalama zoposa K1 million.

A Susan Phiri Kondowe, womwe anakapereka katunduyo m'malo mwa nzikayi, anati thandizolo lomwe mkuphatikizapo shuga, sopo komanso m'chere, linadza pozindikira kuti odwala ena amasowekera zambiri pomwe ali m'chipatala, kaamba ka umphawi.

M'modzi mwa odwala pachipatalachi, a a Chrissy Chabwera, am'dera la mfumu yayikulu Dzoole m'bomali, wati akuvutika kuti apeze zofunika pa moyo wawo watsiku ndi tsiku, choncho lathindizolo lichepetsa ena mwa mavutowo.

*πŸ’« #(1) ZBS ZIKACHITIKA MUMVERA PANO [email protected]*
πŸ‘¨β€πŸ’»βœοΈπŸ‡²πŸ‡Όβš–οΈπŸ“‘πŸ“»πŸ“πŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ‡²πŸ‡Ό

Address

Mangochi

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when ZBS Malawi posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share