05/06/2026
Swalaah ya Janazah ndi imodzi mwa Swalaah zomwe anthu ambili sitimaswali.
Koma ine ntaonetsetsa nnaona kuti chifukwa choti ambili sitidziwa mapangidwe ake.
Mix maliro amachitika patali patali nde timaona ngati basi titha kumakhala olo osadziwa Swalaah yi.
Akachitika maliro basi mkumangodekha.
Poyamba ndimene kuti Swalaah ya Janazah ndi yofunikira kwambili kuyidziwa.
Izi zili choncho chifukwa Swalaah ija ndiyabwino kumbali zonse ziwili.
a. Ndiyabwino kwa ife amoyo omwe tikuyiswali.
b.Komaso ndiyabwino kwa munthu amene wamwalira uja
Pamemepo ndichedwe pang'ono
👇
*Ubwino wa Swalaah ya Janazah kwa amoyo*
Mtumiki ﷺ ananeneratu za malipiro amene munthu umawapeza ukaswali nawo Swalaah imeneyi.
Iye anati:-
👇
مَنْ شَهِدَ الْجَنَازَةَ حَتَّى يُصَلِّيَ عَلَيْهَا فَلَهُ قِيرَاطٌ، وَمَنْ شَهِدَ حَتَّى تُدْفَنَ كَانَ لَهُ قِيرَاطَانِ
*Amene angakhale nawo pa maliro mpakana kuswalira nawo, amapeza Qirat, ndipo amene akhalepo mpakana kuyika amakhala ndi ma Qirat awili*
Mtumiki ﷺ atafusidwa kuti ma Qirat awili ndi chani? Anati:-
مِثْلُ الْجَبَلَيْنِ الْعَظِيمَيْنِ
*(Malipiro akulu) Ngati mapiri awili akuluakulu*
Imeneyi ili mu Swaheeh Bukhari
Moti amzathu akamaswalira maliro aja amakhala akupeza nawo zimenezi.
Ife omwe tangokhala pansi paja osaswali nawo zimenezi *Ubwino wa Swalaah ya Janazah kwa wakufa*
Kumbali ya m'bale wathu otisiya uja, Swalaah ya Janazah iliso ndi ubwino.
Ma chance a munthu oti akalowe ku Jannah amachuluka ndi Swalaah imene ija.
Mtumiki ﷺ ananena kuti:-
👇
مَا مِنْ رَجُلٍ مُسْلِمٍ يَمُوتُ فَيَقُومُ عَلَى جَنَازَتِهِ أَرْبَعُونَ رَجُلاً لاَ يُشْرِكُونَ بِاللَّهِ شَيْئًا إِلاَّ شَفَّعَهُمُ اللَّهُ فِيهِ
*Msilamu aliyense amene wamwalira pamaliro pake ndikuyima anthu 40 osapanga Shirk (kumuswalira), Allah ﷻ amamukhululukira iye ndi Maduwa awo.*
Swaheeh Muslim
Taganizani munthu uja akanakhala amationa ndipo akudziwa kuti akayima anthu 40 apa Allah ﷻ andikhululukira, bwezi akukulimbikitsani chotani kuti muswali nawo?
Nanga taganizani omwalirawo mutakhala Inu?
Nthawi imene ija m'bale wathu amakhala akufuna thandizo lathu nde tisamamutaye ayi.
Nthawi ya Swalaah ya Janazah ikafika, monga Swalaah iliyonse, tiyeni tionetsetse kuti tapanga Wudhu wathu bwino bwino.
Malingana ndi ma Ulama ambiri, imene ija ndi Swalaah ndithu nde imafunika Twaharah yokwanira.
Mtumiki ﷺ amayiswali Swalaah imene ija pagulu nthawi zonse. Nde ifeso tiziyiswali pa gulu.
Unless ngati ilipo wekha nde utha kuswali wekha.
Pakakhala amuna ndi akazi, akazi atha kuyima kumbuyo kwa amuna nkuswali nawo ngati muja tichitira Swalaah zonse.
Kapena after kuswalira amuna Janazah ija itha kuoititsidwa Malo omwe Pali akazi kuti akaswalireso.
Zonsezo ndi zotheka.
Ngati zatheka titha kupanga mizere itatu. Ngakhale kuti zilibe vuto kweni kweni chifukwa ma Hadeeth omwe abwela pa zimenezi si amphanvu kwambili.
*Akamwalira wa mmuna*
Jeneza izayikidwa patsogolo ndipo Imaam azayima cha kumutu kwa maliro aja.
*Akamwalira wa Nkazi*
Imaam azayima cha pakati pa maliro aja.
*Likamwalira Gulu*
Swalaat imodzi imakhala yokwanila kwa gulu lonse. Apo ndekuti maliro a chimuna azayikidwa kutsogolo kwa Imaam ndipo achikazi kumbuyo kwake.
Then anthu azabwela mmbuyomo.
Maswalidwe.
Swalaat ya Janazah ndi yophweka chifukwa siyayitali komaso ilibe zochita zambiri.
Ilibe Rukui kapena Sajdah. Koma imakhala ndi ma Takbeerah angapo ngati muja imakhalira Swalaah ya Eid.
👇
Ma Takbeerah atha kukhala 4, 5, 6, 7 or 9.
Pali ma Hadeeth osiyana siyana amene abwela okamba zoti ma Takbeerah atha kukhala choncho.
However zomwe zili common pakati pa anthu ndi za ma Takbeerah 4. Nde let's go with that.
Koma mukazaona ena aonjezera musazadabwe. Zilipo ndithu.
Akamachitila ma Takbeerah wa titha kumakweza manja. Kapena titha kungokweza pa Takbeerah yoyamba yokha palibe vuto
Takbeerah yoyamba*
Apa manja azakwezedwa kenako azamangidwa, kuyika lamanja pa mwamba pa lamanzere muja timapangira Swalaah Zina muja.
Tikatero timawelenga Surah Fatiha. Ndizothekaso after Fatiha kuwelenga Surah Ina.
Koma kuwelengako kumakhala kotsitsa mawu. Osati mokweza.
*Takbeerah yachiwili*
Apa munthu azapanga Aswalatu ala Nnabiy.
Kumufunira zabwino mtumiki ﷺ. Ngati timanenera tikamaliza after Tashahhu pa Swalaah
👇
اللَّهُمَّ صَلِّ عَلَى مُحَمَّدٍ، وَعَلَى آلِ مُحَمَّدٍ، كَمَا صَلَّيْتَ عَلَى إِبْرَاهِيمَ وَعَلَى آلِ إِبْرَاهِيمَ، إِنَّكَ حَمِيدٌ مَجِيدٌ، اللَّهُمَّ بَارِكْ عَلَى مُحَمَّدٍ، وَعَلَى آلِ مُحَمَّدٍ، كَمَا بَارَكْتَ عَلَى إِبْرَاهِيمَ، وَعَلَى آلِ إِبْرَاهِيمَ، إِنَّكَ حَمِيدٌ مَجِيدٌ
*Takbeerah yachitatu ndi yachinayi*
Kuchokano pa Takbeerah ya chitatu komaso ya chinayi kaya kumapita uko, imeneyi imakhala nthawi yomupangira ma Duwah wakufa uja, komaso achibale ake komaso asilamu.
Ndipo ma Duwah alipo ambiri omwe tingamupangire.
Koma ma Duwah abwino ndi omwe mtumiki ﷺ amapanga monga awa
👇
اللَّهُمَّ اغْفِرْ لَهُ وَارْحَمْهُ وَعَافِهِ وَاعْفُ عَنْهُ وَأَكْرِمْ نُزُلَهُ وَوَسِّعْ مُدْخَلَهُ وَاغْسِلْهُ بِالْمَاءِ وَالثَّلْجِ وَالْبَرَدِ وَنَقِّهِ مِنَ الْخَطَايَا كَمَا نَقَّيْتَ الثَّوْبَ الأَبْيَضَ مِنَ الدَّنَسِ وَأَبْدِلْهُ دَارًا خَيْرًا مِنْ دَارِهِ وَأَهْلاً خَيْرًا مِنْ أَهْلِهِ وَزَوْجًا خَيْرًا مِنْ زَوْجِهِ وَأَدْخِلْهُ الْجَنَّةَ وَأَعِذْهُ مِنْ عَذَابِ الْقَبْرِ أَوْ مِنْ عَذَابِ النَّارِ
اللَّهُمَّ اغْفِرْ لَهُ وَارْحَمْهُ وَعَافِهِ وَاعْفُ عَنْهُ وَأَكْرِمْ نُزُلَهُ وَأَوْسِعْ مُدْخَلَهُ وَاغْسِلْهُ بِالْمَاءِ وَالثَّلْجِ وَالْبَرَدِ وَنَقِّهِ مِنَ الْخَطَايَا كَمَا يُنَقَّى الثَّوْبُ الأَبْيَضُ مِنَ الدَّنَسِ
اللَّهُمَّ إِنَّهُ عَبْدُكَ وَابْنُ عَبْدِكَ وَابْنُ أَمَتِكَ كَانَ يَشْهَدُ أَنْ لاَ إِلَهَ إِلاَّ أَنْتَ وَأَنَّ مُحَمَّدًا عَبْدُكَ وَرَسُولُكَ وَأَنْتَ أَعْلَمُ بِهِ اللَّهُمَّ إِنْ كَانَ مُحْسِنًا فَزِدْ فِي إِحْسَانِهِ وَإِنْ كَانَ مُسِيئًا فَتَجَاوَزْ عَنْ سَيِّئَاتِهِ اللَّهُمَّ لاَ تَحْرِمْنَا أَجْرَهُ وَلاَ تَفْتِنَّا بَعْدَهُ .
اللَّهُمَّ اغْفِرْ لِحَيِّنَا وَمَيِّتِنَا وَشَاهِدِنَا وَغَائِبِنَا وَصَغِيرِنَا وَكَبِيرِنَا وَذَكَرِنَا وَأُنْثَانَا. اللَّهُمَّ مَنْ أَحْيَيْتَهُ مِنَّا فَأَحْيِهِ عَلَى الْإِسْلَامِ وَمَنْ تَوَفَّيْتَهُ مِنَّا فَتَوَفَّهُ عَلَى الْإِيمَانِ. اللَّهُمَّ لَا تَحْرِمْنَا أَجْرَهُ وَلَا تَفْتِنَّا بَعْدَهُ
Ma Duwah ena ndakamba apa Ali mu ma Athar oti anakamba ndi ma swahaba pomwe yoyamba ndi yachiwili ndiza mtumiki ﷺ directly.
Kupeleka salaam
Timaliza Takbeerah ya 4 ndikunena ma Duwah ake timapeleka salaam.
Salaam timapanga ngati ya Swalaah za normal ija.
Kuyamba kumanja then kumazere tikulunjika nkhope yathu kumanja then kumazere
Ndizothekaso kupanga salaam imodzi yakumanja kokha. Pali m Hadeeth omwe amaloreza zimenezo.
Mukazaziona osazadabwa.
Ndikhulupilira tatolapo picture mmene timaswalira Swalaah yi.
Maduwawo lowezani ladies and gentlemen.
Mmaloweza zinthu Inu ma Duwah awawa si nkhani bola kukhala ndi chidwi, kaya si lero or mawa koma lowezani