19/08/2025
Ikhani Chikhulupiliro Mwa Mulungu Ekha
Maliro 3:25 Yehova ndi wabwino kwa amene amayembekezera Iye, kwa munthu amene amafunafuna Iyeyo.
Chinsinsi chokhala ndi mtendere mu dziko losautsali, dziko lokhumudwitsa komanso dziko lodzala ndi zofooketsa komanso uchimo ndi kukhala ndi Mulungu basi!
Osaika chikhulululo chanu mwa anthu chifukwa, akhoza kukukhumudwitsa.
Osaika chikhulululo chanu mwa ndalama/bank account yanu chifukwa, zikhoza kutaika.
Osaika chikhulululo chanu mwa nyengo chifukwa, zimatha kusintha.
Osaika chikhulululo chanu mu zinthu zadziko lapansi chifukwa, sizokhalitsa-
Kumbukirani malonjezo a Mulungu amene ndi Inde komanso Amen.
Mulungu amene anakhala Okhulupilika nthawi yambuyo, adzakhala wabwinonso lero mpaka kalekale.