29/04/2025
MBIRI YA HASTINGS KAMUZU BANDA WENIWENI
( Muzithunzizo uyo wa diso la mng'alayo ndiye yemwe anali Kamuzu weniweni wathu🇲🇼, winayo wavala ma garasiyo dzina lake lenileni linali Richard Armstrong ochokera ku dziko la Ghana 🇬🇠ndipo analamulila dziko la Malawi ngati Kamuzu kwa dzaka 31, ma buku a history ak*telo)
PART 1
Akimu Kankhwala Banda, mwana wa mayi Akupingama Phiri ndi Bambo Mphonongo Banda, a m'mudzi mwa nyakwawa chiwengo, mfumu yaikulu chilowamatambe, m'boma la Kasungu, anali ndi Diso la ng'ala lakumazele.
Ndipo Dzina loti Kamuzu linachokera pa muzu, kapena k*ti mankhwala a zitsamba, omwe mayi ake Akupingama Phiri, anakatenga kwa Sing'anga, kamba koti anali ndi vuto la uchembere.
Mayi Akupingama Phiri, anapatsidwa Kamuzu kamodzi kakang'ono komwe anauzidwa k*ti akanyike m'madzi ndipo adzimwa madziwo k*ti apeze mphatso ya mwana.
Ndipo pambuyo pogwilitsa ntchito mankhwalawo, Mwana anabadwa, ndipo anamutchura Dzina k*ti Akimu Kankhwala Banda.
Akimu ali m'nyamata, anachotsa dzina loti Kankhwala ndikuyikapo Kamuzu, ka mankhwala aja amene mayi ake Akupingama Phiri anapatsidwa ndi Sing'anga, ndipo iye anapita limodzi ndi amalume ake a Hannoch Msokera Phiri, ku Dziko la Zimbabwe.
Akimu akupitiliza maphunziro ake, anasinthanso dzina lake, pochotsa Dzina loti Akimu, ndikukhala Hastings Kamuzu Banda.
Ameneyu ndiye anali Hastings Kamuzu Banda, nzika ya Dziko lathu la Malawi, osati zina zija ayi, mchewa weni weni anali ameneyu.
Mukafufuza kwambiri mbiri ya Kamuzu Banda, mumapeza Anthu awiri, ali pachithunzipa ndi Richard Armstrong waku Ghana uja.
Mbiriyo imapitiliza kufotokoza k*ti, Hastings Kamuzu Banda, wa Diso la ng'ala, ankaphunzira limodzi ndi Richard Armstrong, mayi ake aku Ghana, Bambo ake aku America.
Ndipo Hastings Kamuzu Banda ndi Richard Armstrong, ankagwilizana kwambiri ndipo zonse ku sukulu ankapangira limodzi.
Koma chilichonse chomwe ankachita kapena kuyankhulana ndi Abale ake, Hastings Kamuzu Banda, ankammufotokozera nzake Richard.