
07/08/2025
Timu ya Mighty Wanderers Fc yalowa mgwirizano wachaka chimodzi ndi theka ndi kampani ya Island Beverages yomwe imapanga madzi a Kasupe.
Mgwirizanowu ndi wandalama zokwana K25 million ndipo kampaniyi idzipereka madzi kumatimu onse komanso iziloledwa kuchita malonda ake ogulisa madzi pomwe timuyi ikusewera masewero ake.
Poyankhula ndi Unenesko Fm, mkulu oyendesa zintchito ku timuyi Panganeni Ndovi ,wati mgwirizanowu ndofunikira kwambiri ndipo wabweranso mu nthawi yake pomwe timuyi ikhale ikutenga nawonso mbali mumpikisano wa CAF Confederation Cup.
Mawu ake mkulu wa kampani ya Island Beverages Christopher Malani wati kulowa mumgwirizano ndi timuyi kuthandiziranso kupitisa patsogolo ntchito zamalonda za kampaniyi.