31/08/2026
Katswiri odziwa kukankha chikopa wa m'dziko la Argentina, Lionel Messi walengeza kuti tsopano wasiya kusewerera timuyi atasewera kwa zaka makumi awiri ndi chimodzi (21).
Malingana ndi nyumba yofalitsa nkhani ya Reuters, Messi wanena izi kudzera pa tsamba lake la mchezo la Instagram ponena kuti ngakhale chili chiganizo chowawa komabe nthawi yake yakwana kuti asiye kutumikila timuyi.
Messi anayamba kusewera ku timu ya Argentina Ali ndi zaka 18 ndipo wasewera masewero pafupifupi 207 omwe ndi kuphatikizapo akanali wachisodzera.
Mwa zikho zina zomwe katswiri yu wapambana ndi kuphatikizapo chikho Cha mpira wamiyendo padziko lonse lapansi cha FIFA World Cup m'chaka cha 2022, chikho cha maiko akumwera kwa America (Copa America) komaso chikho cha padziko lonse lapansi cha ana achisodzera osadutsa zaka 20.
Iye wasewerapo masewero a mu ndime yotsiliza ya FiFa World Cup maulendo atatu (2014, 2022, 2026) ndipo masewera ake otsiliza ndi timuyi anali pomwe anagonja ndi timu ya Spain.
Olemba Frank Mkanalumo.