31/07/2025
SIMUZANDIMVA NDIKUNYOZA KAPENA KUTUKWANA ANZANGA OMWE NDIKUPIKISANA NAWO — DOSSA
M'modzi mwa anthu omwe akupikisana nawo pa udindo wa Mphungu Wanyumba ya Malamulo kudera la Balaka Bwaila, wa chipani cha UTM, Mercy Dossa, wati satenga nawo gawo pa kunyoza kapena kutukwana anzake omwe akupikisana nawo pa chisankhochi.
Dossa wanena izi Lachitatu pa 30 July, 2025, pa msonkhano wokopa anthu omwe anachititsa pa bwalo la masewero la Mbera, pomwe amafotokozera anthu zina mwa ndondomeko zomwe akufuna kuchita m'deralo ngati atapatsidwa mwayi woti akawatumikile ku Nyumba ya Malamulo.
“Simuzandimva ndikunyoza kapena kutukwana anzanga omwe ndikupikisana nawo. Tikuyenera kukhala ndi kampeni yoyenera komanso yolemekezana chifukwa cholinga chathu tonse ndichimodzi, kutukula dera lino,” adatero Dossa.
Asanapange msonkhanowu, Dossa anakapereka kalata zake ku bungwe loyendetsa zisankho la MEC pa Mbera TDC, ngati gawo lofunikira kuti avomerezedwe kutenga nawo mbali pa chisankho chomwe chikhalepo pa 16 Seputembala chaka chino.
Wolemba: Francis Maonjera_ Balaka
(July,31,2025)