Nsanje tips

Nsanje tips News updates✓Nsanje & across The warm � of Africa MW.

 *MAI WAMWALIRA PA MKANGANO WAKU CHIGAYO*Apolisi ku Chikwawa amanga a Nales Stephano adzaka 45, ochokera m'mudzi wa Cham...
22/06/2026



*MAI WAMWALIRA PA MKANGANO WAKU CHIGAYO*

Apolisi ku Chikwawa amanga a Nales Stephano adzaka 45, ochokera m'mudzi wa Chambuluka m'bomali kamba kowaganizira kuti apha a Patricia Yosefe kutsatira mkangano womwe unabuka pa mzera wa anthu omwe amadikira kugaya chimanga pa malo a malonda a Bereu.

Malinga ndi mneneri wa polisi ya Chikwawa a Dickson Matemba, mdzukulu wa malemuyo anakangana ndi mayiyu pa nkhani yokhudza amene anayenera kutsogola pa mzera wogayira chimanga.

Malemu Patricia Yosefe omwe anali a zaka 83, atalowererapo pofuna kuthetsa mkanganowo, akuti mayiyo anamukankha mwamphamvu ndipo anagwa pansi.

Kutsatira kugwaku a Patricia Yosefe anakomoka ndipo anthu amene anali pafupi anawatengera ku chipatala kuti akalandire chithandizo.

Koma atafika kuchipatala, madotolo anatsindika kuti amwalira kamba kovulala kwambiri m'mutu.

Pakadali pano, apolisi akupitiliza kufufuza nkhaniyi ndipo ati mayiyu adzaonekera ku khoti kafukufuku akadzatha.

Kuwonjezera apo Iwo alimbikitsanso anthu kuti azithetsa mikangano mwa mtendere komanso kukambirana, m'malo mochita ziwawa zomwe zingabweretse mavuto aakulu kuphatikizapo imfa.

18/05/2026



Munthu m'modzi akuganizilidwa kuti wafa pomwe ena angapo avulala pa ngozi ya galimoto yomwe yachitika mphindi zingapo zapitazo pa Nyaikha, kwa Ngabu m’boma la Chikwawa, pomwe galimoto yomwe imachokera ku Chikwawa kupita kwa Sorgin yagubuduka.

M'modzi mwa anthu amene anali m’galimotomo, Aggie Viano, wati galimoto ya matani atatuyo inali itanyamula matumba a nyemba, katundu wina, komanso anthu ndipo ovulala atengeledwa kuchipatala cha Ngabu kuti akalandire thandizo.

Apolisi akuyembekezeka kulankhulapo.

14/05/2026

Nkuyankhula kwa Mfumu yaikulu Ngabu yati pakufunika kuunikiranso malamulo adziko lino. Iwo apempha deputy commissioner wa police kuti chilango Cha anthu omwe apha nzawo ndichopepuka kwambiri, choncho iwo ati adakakonda kuti okupha nzake nayenso aziphedwa, kuti zichepetse kapena kuti kuthetseratu mchitidwe ophana dziko muno.

Izi ayankhula pa nsonkhano omwe likulu la chitetezo lakhazikitsa ku Ngabu, m'boma la chikwawa ozindikiritsa anthu za nchitidwe onyatsa omwe ukuchitika kuchigwa cha nsinje wa shire.

 Nthawi Ina iliyonse masewero a pakati pa ma team a Ngabu select ndi Blue Eagles akhale akuyamba pa Ngabu community Grou...
14/05/2026



Nthawi Ina iliyonse masewero a pakati pa ma team a Ngabu select ndi Blue Eagles akhale akuyamba pa Ngabu community Ground, mboma la Chikwawa.

Awa ndi masewero omwe akonzedwa ndi cholinga chozindikiritsa anthu za nkhani zomwe zakhala ziyenda masiku anayi apiyawa pa nkhani zopanda umboni zomwe zadzetsa chipwirikiti pakati pa anthu am'maboma a Chikwawa ndi Nsanje.

Pamalowa pabwera alendo osiyanasiyana monga aDeputy commissioner of police, atsogoleri osiyanasiyana amipingo komanso mafumu.

13/05/2026

Ulendo wa ndawala ulimkati mu boma la Nsanje .Ndipo ulendowu wandawala wayamba pa Bangula kupita ku Nsanje Boma.

Uku apolisi nyimbo zilimkati .
mutu wamyimbo wawo ukuti " Asakunamize sisowa '

 First Grade Magistrate Annie Chinkhadzula m'boma la Chikwawa alamula kuti anthu 28 omwe akuganiziridwa kuti adapha anth...
11/05/2026



First Grade Magistrate Annie Chinkhadzula m'boma la Chikwawa alamula kuti anthu 28 omwe akuganiziridwa kuti adapha anthu asanu masiku apitawa powaganizira kuti amasowetsa ziwalo zobisika za anthu m'matsenga ku Nsanje ndi Chikwawa kuti abakasungidwebe ku ndende ya Chichiri podikirira kupita ku bwalo la milandu lalikulu ku Blantyre.

Bwalo linamva kuchokera kwa woyimila boma pa milandu, a Enerst Mangweru kuti anthuwa achita zosemphana ndi gawo 209 la lamulo oyendetsera dziko lino ndipo akuyenera kudzayankha mlandu wakupha ku bwalo lalikululi masiku akubwelewa.

Apa Magistrate Chikhadzula waperekanso mwayi woti anthuwa atha kukasaka loya ndipo akalephera boma lidzawapezera loya pakhaniyi kuti adzawaimilire.

Police in Chikwawa apolisi akhwimitsa chitetezo potsatila zakuphedwa kwa anthu ena atatu mdelari powaganizila kuti asowe...
10/05/2026

Police in Chikwawa
apolisi akhwimitsa chitetezo potsatila zakuphedwa kwa anthu ena atatu mdelari powaganizila kuti asowetsa maliseche. Akuti Malowa ndi malo womwe bambo wina a Baza Sande aawotchedwa powaganizila nkhani za bodza zoti akukhuzidwa pa mchitidwe wosowetsa ziwalo zobisika za anthu.

Apolisi amanga anthu atatu powaganizira kuti apha komanso kubweretsa chisokonezo pa mphekesera zokhudza kusowa kwa malo ...
10/05/2026

Apolisi amanga anthu atatu powaganizira kuti apha komanso kubweretsa chisokonezo pa mphekesera zokhudza kusowa kwa malo obisika m'boma la Chikwawa.

Malingana ndi mneneri wa polisi, Lael Chimtembo, oganiziridwawa ndi Thomas Moses, Montford Tembenuka onse ochokera m'mudzi mwa Nyaekha m'boma la Chikwawa.

Chimtembo wati awiriwa akuganiziridwa kuti anapha Baza Sande wa zaka 34 dzulo m'mawa.

Oganiziridwa wina ndi Hudson Thomas wazaka 26, amene akumuganizira kuti amauza anthu kuti malo ake obisika asowa, atafufuzidwa anapeza kuti palibe chosintha chili chonse.

Mneneriyu wati, oganiziridwawa akhala akutengeredwa ku bwalo lamilandu pamene apolisi akanafufuza za anthu ena omwe anatenga nawo mbali pokupha anthu atatu m'bomali pa nkhani yokhudza kusowa kwa malo obisika.

10/05/2026
09/05/2026



Anthu okwiya atentha Yobe Ng'oma limodzi ndi mkazi wake Migiresi M***a a midzi ya Phanda ndi Milore kwa mfumu yaikulu Masache ku Chikwawa powaganizira kuti anasowetsa maliseche a munthu wina mmatsenga.

Awiriwa atenthedwa mmudzi wa Simbi komwe anali nawo ku mwambo wa maliro ndipo zachitika pomwe Ng'oma amapempha madzi pa khomo lina.

Dickson Matemba, wofalitsa nkhani za Apolisi ku Chikwawa wati ali kumeneko munthu wina anakuwa kuti maliseche ake asowa zomwe zinakwiyitsa anthu ndipo analoza zala Ng'oma kuti ndiye wachita za mtopolazi ndipo anayamba kumumenya.

Matemba wati mkazi wake wa Ng'oma atamva izi anathamangira komweko kuti akapulumutse mwamuna wake koma anthu okwiyawa anawatengera limodzi pa thengo lina komwe anawatentha ndi moto.

Zotsatira za chipatala cha Ngabu zawonetsa kuti awiriwa afa kamba ka ululu wa mabala opsa ndi moto.

Address

BOX 101 NDAMERA
Ndamera

Opening Hours

00:00 - 17:00

Telephone

+265884439723

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Nsanje tips posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Business

Send a message to Nsanje tips:

Shortcuts

Share