
08/08/2025
MaKhonsolo a maboma a Mwanza ndi Neno lachiinayi sabata ino asainirana mapangano a m'gwilizano ndi wayilesi ya Neno kuti wayilesiyi iziulutsa mapulogalamu amaphunziro akupulayimale amumabomawa.
A Fredrick Kaphuka Malango omwe ndi m'modzi mwa akuluakulu oona zamaphunziro m'boma la Mwanza ati cholinga chawo ndikupititsa patsogolo maphunziro a mma'boma awiliwa kaamba koti zaka zingapo mabomawa samachita bwino kumbali ya chiwerengero cha ana okhoza mayeso a maphunziro awo.
A Malango ati ophunzirawa aziphunzila kudzera pawayilesi pogwilitsa ntchito mafoni akompyuta yammanja (tablet fon) omwe anawapeleka kale musukulu zamabomawa.
Iwo pempha makolo kuti atenge udindo ophunzitsa ana awo akakhala pakhomo ndicholinga choti mapulogalamuwa abale zipatso.
Mmau ake mkulu oyang'anira ntchito za wayilesi ya Neno a Jane Chinkwita ati mgwilizanowu ndiothandiza kwambiri kaamba koti makolo azitha kutsatira maphunzirowa kudzera pawayilesi ndi kupeza luntha la momwe angaphunzitsile ana awo akakhala pakhomo.
Iwo ati aonetsetsa kuti akugwira ntchitoyi modzipeleka komanso mwa ukadaulo ndicholinga choti mabomawa atukuke.
Wayilesi ya Neno imamveka mmaboma a Blantye, Mwanza, Ntcheu ndi maboma ena ozungulira.
Wolemba Chifundo Masauli 08/08/2025