Lipenga la Neno

  • Home
  • Lipenga la Neno

Lipenga la Neno Takulandilani ku Lipenga la Neno...the purpose of this page is to give you news and activities that matter to you without fear or favour
(1)

Chiwerengero cha anthu omwe akufuna mpando wa Phungu dera la Neno East sopano chafika pa anthu 13 kusatira kulengeza kwa...
13/07/2025

Chiwerengero cha anthu omwe akufuna mpando wa Phungu dera la Neno East sopano chafika pa anthu 13 kusatira kulengeza kwa ntolankhani Luke Chimwanza kuti wakatenga zikalata zake ku bungwe la MEC ndipo apikitsana nao ngati phungu oima paekha.

A Chimwanza omwe ndi mtsogoleri wa a ntolankhani chigawo cha ku mwera-Blantyre press Club ndiye kuti akhala ntolankhani wachiwiri kuimira ku dera la Neno East pambuyo pa a Patrick Kamkwatira omwe nao anatula pansi ntchito ku wailesi ya Times.

A Chimwanza amachokera m'mudzi mwa Tchenga ku Matope

Dera la Neno East ndi latsopano ku Neno, ndipo likukuta dera lonse lomwe liri pansi pa mfumu yaikulu Symon komwe kuli madera a Zalewa, Lisungwi, Matope ndi Kasamba kungotchulapo ochepa chabe

02/07/2025
Phungu wa dera la Neno North a Thoko Tembo ati ndizodandaulitsa kuti ngakhale khonsolo ya Neno ndiyo yakhala nambala wan...
02/07/2025

Phungu wa dera la Neno North a Thoko Tembo ati ndizodandaulitsa kuti ngakhale khonsolo ya Neno ndiyo yakhala nambala wani pa ma nkhosolo onse mdziko muno mu kauniuni wa LAPA yapasidwa ndalama yochepa kuyerekeza ndi makhonsolo ena omwe sanachite bwino.

Phunguyi wanena izi pa tsamba lake la nchezo pomwe anati ochita bwino amayenera kulandira mphoto yopotsa omwe sanachite bwino zomwe ati ndizosiyana ndi momwe pulojeketi ya Enable Service Delivery ikuyendesera zinthu zake.

Komabe iye anati sikuti ali ndi mkhwizi kapena jelasi ndi makhonsolo ena omwe apasidwa ndalama zochuluka kuposa Neno, koma anati pamafunika omwe akuchita bwino kuwapatsa mphoto zowalimbikitsa kuti achite bwino kuposa pomwe afikira.

Khonsolo ya Neno yalandira pafupifupi 556 Million kwacha pomwe makhonsolo ngati Balaka, Thyolo ndi Mulanje kungotchulapo ochepa chabe alandira ndalama zoposera 1 Biliyoni.

Ndalamazi ndi za Governance to Enable Service Delivery Project imene amayendatsa ndi makhonsolowa

Pulojekiti yi ndi ya boma la Malawi kudzera ku bungwe la Boma la ukadaulo pa Chuma la National Local Government Finance Committee

Amapereka thandizo la chuma ndi A banki yayikulu padziko lonse lapansi ya World Bank

Ndalama zonse zimene za pita ku Makhonsolo ndi 57billiion Kwacha kuphatikizapo za RCRP2 project imene akuthandizanso ndi A World Bank.

Khonsolo ya boma la Neno yakhala  nambala 1 pa makhonsolo 28 omwe achita bwino pogwiritsa ntchito ndalama zachitukuko za...
01/07/2025

Khonsolo ya boma la Neno yakhala nambala 1 pa makhonsolo 28 omwe achita bwino pogwiritsa ntchito ndalama zachitukuko za m'thumba la Performance Based Grant (PBG) pansi pa ntchito za Governance to Enable Service Delivery (GESD) mu chaka 2023-2024.

Izi ndi malinga ndi kawuniwuni yemwe bungwe la National Local Government Finance Committe (NLGFC) wa Loacal Authorities Performance Assessment (LAPA) 2024 linachita pofuna kuona momwe makhonsolowa akugwiritsira ntchito ndalama zachitukukozi.

Powulutsa zotsatira za kawuniwuniyu lero m'boma la Salima nduna ya maboma ang'ono a Richard Chimwendo Banda yati ndalama zomwe makhonsolowa amalandira cholinga chake ndi kutukula miyoyo ya anthu kumidzi, osati kulemeretsa kagulu kena ka anthu.

Mu chaka cha 2023 khonsolo ya Neno inali nambala 25
https://www.tiktok.com/.la.neno?_r=1&_d=ejb5dd09gdmcj7&sec_uid=MS4wLjABAAAAL9o2RwTgxfIbUGy_RxNK-_-i_YJCulDD4MJTTyryaX4tO5OP2p3RrqAnOP7JXxZG&share_author_id=7490153556830749704&sharer_language=en&source=h5_m&u_code=eji2i9kleh360d×tamp=1751380663&user_id=7490153556830749704&sec_user_id=MS4wLjABAAAAL9o2RwTgxfIbUGy_RxNK-_-i_YJCulDD4MJTTyryaX4tO5OP2p3RrqAnOP7JXxZG&utm_source=copy&utm_campaign=client_share&utm_medium=android&share_iid=7510570078049060664&share_link_id=073f8aad-5fb0-4300-bf42-977d7c5e7343&share_app_id=1233&ugbiz_name=ACCOUNT&ug_btm=b8727%2Cb4907&social_share_type=5&enable_checksum=1

Ndiyetu ku Mwanza West kumeneko kusatira infa ya emwe anali phungu wa delari mayi Joyce Chitsulo sopano anthu akumeneko ...
28/06/2025

Ndiyetu ku Mwanza West kumeneko kusatira infa ya emwe anali phungu wa delari mayi Joyce Chitsulo sopano anthu akumeneko mogwirizana ndi chipani cha MCP asankha mwana wake wa Joyce Chitsulo, Maureen Chitsulo Chirwa kuti ndiyemwe azaimire chipani cha MCP ngati phungu pa zisankho za pa 16 September ku delari

Yemwe akuzaimira ngati phungu wa  chipani Cha DPP dera la Neno East a Mary Maulidi Khembo ayamba ntchito yokonza mijigo ...
27/06/2025

Yemwe akuzaimira ngati phungu wa chipani Cha DPP dera la Neno East a Mary Maulidi Khembo ayamba ntchito yokonza mijigo yowonongeka ku derali ndipo dzulo anali mudzi mwa Makoza mfumu yaikulu Symon ndi a nyamata awo kugwira ntchitoyi

Iwo auza Lipenga la Neno kuti madera ena akhala zaka ziwiri akusowa madzi aukhondo.

Mu chaka cha 2022 ndi 2023 matenda a kolera anavuta kwambiri ku delari ndipo iwo ati aonesetsa kuti iyi ikhale mbiri pobwezeretsa mijigo yonse yomwe inafa

Maulendo apa njinga zamoto afika powawitsa m'boma la Neno chifukwa chakukwera mtengo kwa mafuta a galimoto mu misika yos...
16/06/2025

Maulendo apa njinga zamoto afika powawitsa m'boma la Neno chifukwa chakukwera mtengo kwa mafuta a galimoto mu misika yosavomerezeka (black market) momwe iwo amagula.

Pakadali pano, mtengo wa Petro wafika pa K12,000 pa litre pamene ena akugulitsa mafutawa pa mtengo wa K10,000 pa litre mmisika yo.

Izi zipangitsa kuti mitengo yolipilira njinga zamoto pamaulendo osiyanasiyana ikwere molakwitsa poyenda mmadera osiyanasiyana m'boma la Neno.

Mwachitsanzo kuchoka pa Zalewa kupita paboma la Neno mtengo wanjinga wafika pa K20,000 pamene mmbuyomu ulendowu umalipiridwa K8,000 kupita kokha.

Maulendo ena omwe amalipiridwa K1,000 pano ali pa K3,000 komanso komanso maulendo omwe anali pa K3,000 akwera kufika pa K6,000.

Mmodzi mwa anthu oyendetsa njinga zamotozi pa Zalewa, Everson Mbewe, ati mitengoyi yakula chonchi chifukwa mafuta sakupezeka ndipo anyamata ogulitsa mafuta akumakagula mafutawa ku Ntsakama mdziko la Mozambique zomwe zikupangitsa kuti mafutawa adziwagula pamtengo okwera zedi.

Olemba Joseph Mkango wa MIJ Online

Current weather at Neno BomaKwanuko nyengo ili bwanji?
15/06/2025

Current weather at Neno Boma
Kwanuko nyengo ili bwanji?

Emmie Deebo aimba nyimbo yokhunza moyo wake ali ku Neno
12/06/2025

Emmie Deebo aimba nyimbo yokhunza moyo wake ali ku Neno

Khonsolo ya Neno ndiyo yakhala nambala wani pa ma nkhosolo onse mdziko muno pakayendesedwe ka ntchito za chuma ndi chitu...
22/05/2025

Khonsolo ya Neno ndiyo yakhala nambala wani pa ma nkhosolo onse mdziko muno pakayendesedwe ka ntchito za chuma ndi chitukuko.

Izitu ndi malinga ndi bungwe la MALGA lomwe limayanga'anila ntchito za ma khonsolo ndipo pokhala nambala wani nkhosolo ya Neno yalandira Chikho komanso ndalama

Are you looking for a new opportunity to make a real impact with your IT skills? Partners In Health Malawi is currently ...
22/05/2025

Are you looking for a new opportunity to make a real impact with your IT skills? Partners In Health Malawi is currently seeking a passionate and talented individual to join their team.

Link: https://shorturl.at/XVdKC

Kwa nthawi yoyamba chipatala chachikulu cha Neno, sopona chili ndi chipinda chomwe chizigoneka anthu odwalika kwambiri N...
09/05/2025

Kwa nthawi yoyamba chipatala chachikulu cha Neno, sopona chili ndi chipinda chomwe chizigoneka anthu odwalika kwambiri

Ndipo pali chiyembekezo choti kusegulidwa kwa malowa kuchepetsa chiwerengero cha odwalika omwe amatumizidwa ku chipatala cha Queen Elizabeth Central Hospital kuchokera pa chipatalachi.

Chipindachi chomwe chili ndi zipangizo zapamwamba achimanga ndi thandizo la ndalama kuchokera ku bungwe la Partners In Health Malawi/Abwenzi Pa Za Umoyo

Address


Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Lipenga la Neno posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Business

Send a message to Lipenga la Neno:

Shortcuts

  • Address
  • Telephone
  • Alerts
  • Contact The Business
  • Claim ownership or report listing
  • Want your business to be the top-listed Media Company?

Share