15/07/2026
|Dedza - Malawi
Anthu asanu ndi atatu afa ndipo ena asanu ndi mmodzi avulala pa ngozi ya galimoto yomwe yachitika mmawa wa lero pa msika wa Bembeke mu msewu wa Dedza - Ntcheu.
Malipoti akuti galimoto lonyamula katundu la mtundu wa Howo, imachokera ku Dedza Roadblock ndipo imafuna kupitilira galimoto ina kutsogolo kwake (overtake) mwatsoka inaombana ndi minbus yomwe imachokera mbali ya Ntcheu.
Olankhulira polisi ya Dedza a Beatrice Jefita atsimikiza za izi ndipo ati anthu asana ndi atatu wa nkuphatikizapo driver wa minibus yo anavulala modetsa nkhawa ndipo pomwe amafika nawo ku chipatala anali atafa kale.
Pomwe anthu ena asanu ndi mmodzi akadali mchipatala pomwe akulandira thandizo.
A Jefita ati polisi sinakwanitse kuzindikira anthu omwe afawa ndipo akawazindikira akhale akuwaziwitsa achibale awo a anthuwa komanso mtundu wa a Malawi.
Precious Wilson Charliey |Ntcheu