NewConnect Malawi

NewConnect Malawi J͚T͚B͚-T͚E͚A͚M͚
-Digital Valid Multi-Malawian-
-News and Broadcaster Media and connector Company-

"Galimoto ya pa mdipiti wa vice president, Lead or Pilot Vehicle yomwe imanyamula achitetezo anga yalandidwa ndikupereke...
13/08/2025

"Galimoto ya pa mdipiti wa vice president, Lead or Pilot Vehicle yomwe imanyamula achitetezo anga yalandidwa ndikuperekedwa kwa munthu oti si vice president. Galimoti yi ndi ya boma osati yachipani. Inetu olo atandiranda ma galimoto onse kuti ndiyende pa wheelbarrow sindingawone vuto chifukwa ndakula ndikuyendetsa chingelengele. Ine ndimadya zanga ndipo ndi libe mulandu. Chomwe ndikudana nacho ine ndi katangale ndi umbava!"
_ Dr Michael Usi

12/08/2025

Nthawi yaife, ana amma 2000 sakuziziwa izi😂

 -06/08/2025 EveningAKAKAMIZIDWA KUKHALA PACHIMPANDO CHAMOTO-APULUMUKIRA MKAMWA MWAMBUZIMnyamata wina wa zauchifwamba ye...
06/08/2025

-06/08/2025 Evening

AKAKAMIZIDWA KUKHALA PACHIMPANDO CHAMOTO-APULUMUKIRA MKAMWA MWAMBUZI
Mnyamata wina wa zauchifwamba yemwe Pakali pano sakudziwika wapulumuka kuzibagera ndi moto olusa omwe chinantindi cha ophunzira apa sukulu ya ukachenjede ya MUBAS mu mzinda wa Blantyre chinamukonzera kutsatira kugwidwa kwake pa zauchifwamba zomwe anachitira mmodzi wa wophunzira wapa sukuluyi.

zachitika usiku wapa 06 August 2025.
Kutsatira kafukufuku, zikuonetsa kuti ophunzira omwe ndi mtsikana ndi mnyamata pa njira yake yaku sukulu mosaganizira ndikuyembekezera kalikonse anakumana ndi anyamata awiri omwe anayamba kuwashisha kuti awalande zipangizo zawo.

Ataona kuti , Mnyamata wophunzirayo analibutsa liwiro kuthawa kumusiya mtsikana akulimbana ndi achifwambawo pomwe amafuna amulande chikwama cha zipangizo.

Mtsikana anakwanitsa kukuwa ndipo anthu oyandikira malowo kuphatikiza ophunzira ena anakhamukira komko pomwe anakwanitsa kugwira chifwamba chimodzi ndipo zifwamba zinazo zinafumuka mkuthawa.

Chifwamba chogwidwacho chinatengedwera kumalo achiweruzo a mtundu wa MUBAS komwe anaphiliphithidwa komaso ndiyatsidwira mpando kuti akhalepo.

Mwamwayi apolisi anafika nsanga kudzapulumutsa chifwambachi.

04/08/2025

Komatu Simukulankhula bwino😭😭
😂😂

28/07/2025

In case you missed it, you always appreciate your presidential candidate.

  MwDon't forget kuti tili mu nyengo ya ma running mate.
27/07/2025

Mw

Don't forget kuti tili mu nyengo ya ma running mate.

zikatere 4 million izikhala yatheka basi,🥳🥳
20/07/2025

zikatere 4 million izikhala yatheka basi,🥳🥳

Happy birthday to APM🎂
18/07/2025

Happy birthday to APM🎂

🎊🎉Lero pa 18 July ndi tsiku lokumbukira kubadwa kwa mtsogoleri wa kale wa dziko lino,Prof. APM.
18/07/2025

🎊🎉
Lero pa 18 July ndi tsiku lokumbukira kubadwa kwa mtsogoleri wa kale wa dziko lino,Prof. APM.

  Anthu anayi afa ndipo ena omwe chiwerengero chake sichikudzuwika  avulala modetsa nkhawa pa ngozi yomwe yachitika mmaw...
17/07/2025



Anthu anayi afa ndipo ena omwe chiwerengero chake sichikudzuwika avulala modetsa nkhawa pa ngozi yomwe yachitika mmawa uno pa malo otchedwa chilanga m'boma la Balaka.

Wofalitsa nkhani za chipatala chachikulu cha Machinga a Wongani Nyirenda atsimikiza za imfa ya anthuwa.

"Pakadali pano talandira anthu ovulala ochulukirapo koma mwatsoka anthu anayi ndiomwe amwalira." atero a Nyirenda.

Malipoti akusonyeza kuti galimoto la lorry lomwe anthuwa anakwera linaombana ndi galimoto lina lomwe limachokera mbali yosemphana ndi Lorry.

Pakadali pano apolisi sanayankhulepo pa nkhaniyi.


ahead

  A devastating fire has swept through Luwinga market in Mzuz, leaving a trail of destruction. The origin of the fire is...
17/07/2025



A devastating fire has swept through Luwinga market in Mzuz, leaving a trail of destruction. The origin of the fire is still unknown as of now.

The preliminary reports suggest that 7 shops have been reduced to ashes. Shop owners and sympathetic bystanders are trying to put more effort to bring the fire under control.

By: Lucinio Patrick

 Kutsatira kumva dandaulo la yemwe amapikisana nawo pa chisankho chachipulura,ku dera lapakati la boma la Mzimba, a Vitu...
16/07/2025


Kutsatira kumva dandaulo la yemwe amapikisana nawo pa chisankho chachipulura,ku dera lapakati la boma la Mzimba, a Vitumbiko Mumbai, bwalo lamilandu lalikulu la Mzuzu lalamula chipani cha Malawi Congress (MCP) kuti lichititsenso chisankhochi.

Popereka chigamulo, woweruza Justus Kishindo wati MCP sinatsate ndondomeko yoyenera poyendetsa zisankhozi. Koma yemwe adapambana pa chisankhochi a Adamson Mkandawire ati sakutekeseka ndi chigamulochi ndipo Ali ndi chiyembekezo kuti ziyenda bwinonso.

A Mumba anakamang'ala ku bwalo lamilandu atalephera kupambana pa chisankhocho ponena kuti panali zachinyengo.

Address

Ntcheu

Website

https://x.com/newconnectmw

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when NewConnect Malawi posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share