20/08/2025
Bungwe lophunzitsa anthu zinthu zosiyanasiyana la National Initiative for Civic Education (NICE) lati ndi kofunika kuti omwe akupikisana pa chisankho cha pa 16 September azigwiritsa ntchito mwayi wa mitsutso ngati potambasulira anthu mfundo za chitukuko zomwe azachite akazapambana pa chisankhochi.
Mkulu woyendetsa ntchito za bungweli m'boma la Blantyre a Glory Ngosi Maulidi ayankhula izi lero pa bwalo la sukulu ya pulaimale ya Makhetha mdera la Ndirande Makhetha pa mtsutso wa opikisana pa mipando ya khansala ndi phungu mderalo.
Iye wapemphanso mafumu kuti apereke mwayi wofana kwa omwe akupikisana akafuna kuchitisa misonkhano ku madera awo, zomwe zingathandizire kupewa ziwawa mu nthawi ino yokopa.
Poyankhulapo mlembi wamkulu wa chipani cha United Democratic Front (UDF) yemwenso akupikisana nawo pa mpando wa phungu m'derali, Genarino Lemani wapempha zipani komanso opikisana kuti asunge bata ndi mtendere mu nyengo ino yokopa anthu.
Omwe anatenga nawo mbali pa mtsutsowu ndi monga aphungu a zipani za UDF,DPP, AFORD, MCP ndi ena oyima pawokha komanso makhansala a zipani za UTM, Odya zake alibe Mlandu, ndi enanso oyima pawokha.