20/08/2026
Kuchipatala Tinakumana… Lero Walowa Chisilamu 🤲🏽❤️
Alhamdulillah! 🤲🏽
Lero takhala ndi mwayi wolandira M’bale wathu watsopano mu Chisilamu, Tiyamike Mapanga, kuchokera ku Mauzi Village, Phalombe, pafupi ndi malire a Mozambique.
Nkhani yake inayambira kuchipatala, pamene adamva ine ndikuyankha Salam pa phone. Anandifunsa kuti:
"Kodi ndinu Muslim?"
Ndinamuyankha kuti, "Eya." Kenako anayamba kundifunsa mafunso osiyanasiyana okhudza Chisilamu. Alhamdulillah, ndinamufotokozera zomwe Chisilamu chimaphunzitsa ndipo adamvetsera mwachidwi.
Komabe, nthawi imeneyo sanatenge Shahada, chifukwa anali ndi mantha komanso ankafuna kaye kuganizira bwino ndi kufufuza, makamaka chifukwa cha zomwe angakumane nazo kuchokera kwa anthu a kwawo.
Tidamupatsa mpata kuti afufuze komanso kuganizira.
Koma lero, watiyimbira foni n’kunena kuti akubwera chifukwa wafika pa chisankho cholowa Chisilamu. ❤️☝🏽
Alhamdulillah, lero tamulandira ngati M’bale wathu watsopano mu Chisilamu. 🤲🏽
📍 Name: Tiyamike Mapanga
📍 Village: Mauzi
📍 District: Phalombe
📍 Area: Pafupi ndi malire a Mozambique
Allahu Akbar! 🤲🏽❤️
Tiyeni timupempherere kuti Allah amukhazikitse pa Chisilamu, amupatse mphamvu komanso amuthandize kupirira pa ulendo wake watsopano wa Imaan. Aamiin. 🤲🏽