PortHerald Press

  • Home
  • PortHerald Press

PortHerald Press Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from PortHerald Press, Media Agency, Chikwawa, .

Registered Media House
best online publication that provides catchy and tangible breaking news.

provide top-notch media consultancy and advertisements

/Whatsapp +265 889 35 35 57
✉️ [email protected]
#"The Truth Uncovered"

 NDALAMA WAKUMANA NDI BUSHIRI  Bhima Ndalama mtolankhani wakale wa Mibawa Television yemwenso amusankha kukhala khansala...
27/10/2025


NDALAMA WAKUMANA NDI BUSHIRI

Bhima Ndalama mtolankhani wakale wa Mibawa Television yemwenso amusankha kukhala khansala wa Sambagalu Ward m'boma la Thyolo tsopano wakumana ndi mneneri Shepherd Bushiri.

Ndalama wakumana ndi Bushiri ku Lilongwe komwe mwazina akambirana zokhudza chuma komanso kuunikira mmene achinyamata angathe kuzidalira wokha.

Kudzera pa tsamba lake la mchezo ola lapita, Ndalama wati wazindikira lero kuti Bushiri ndiwochezeka komanso wa nzeru zakuya.

Zomwe wapindula kumeneko sadaulure.



ItOffers:
and (color printing printing studio or printing Photo printing
:Sorgin moyandikana ndi Phute Bar mphepete mwa msewu wa M1.
0998712825 Whatsapp on 0882274370.

 Don Marley ndi Harry Chabe ndiomwe ayankha MOLONDOLA ndi mogwira nthawi mu mpikisano wa D-Tech Printers Bundle Ipite Pr...
27/10/2025



Don Marley ndi Harry Chabe ndiomwe ayankha MOLONDOLA ndi mogwira nthawi mu mpikisano wa D-Tech Printers Bundle Ipite Promotion.

Awiriwa atumize ma nambala awo mwansanga kuti alandire bundle yawo ya week.

Yankho: Mpira uli pa B

 NDIPITILIZA POMWE NDINALLEKERA-Ilyas Karim     Phungu wa dera la kumwera m'boma la Chikwawa Ilyias Karim walonjeza kuti...
27/10/2025


NDIPITILIZA POMWE NDINALLEKERA-Ilyas Karim



Phungu wa dera la kumwera m'boma la Chikwawa Ilyias Karim walonjeza kuti apitiliza ntchito za zitukuko zomwe wakhala alikuchita m'derali.

Karim wanena mawuwa Lolemba atangolumbilitsidwa ku Nyumba ya Malamulo mu mzinda wa Lilongwe.

Iye wati ayesetsa kuthana ndi zitukuko zomwe sizisanathe ndipo wati zikhala m'gulu lake loyambilira kugwira.

"Ndikufunitsitsa kuti zitukuko zomwe zinayambidwa zithereti monga chipatala chaching'ono cha Nsangwe," watero phungu.

M'modzi mwa nzika ku derali, Doreen Sauti wati ali wonyadira kwambiri ndi kusankhidwanso kwa Illias Abdul Karim kuti apitilizire ntchito za zitukuko.

Iye wati mu zaka zomwe Karim wakhala phungu wa derali kwavumba zitukuko zam'nanu.

"Tapatsidwa sukulu za sekondale yoyendera pa Nkhwangwa ndi Konzere zomwe mu mbiri ya dera lino panalibe,"watero Sauti.

Iye anapitiliza kunena kuti ndikusankhidwaku akuyembekezera zinthu zambiri mu zaka zisanu zikubwerazi.

Aka kakhala kachitatu Karim akutumikira derali.



ItOffers:
and (color printing printing studio or printing Photo printing
:Sorgin moyandikana ndi Phute Bar mphepete mwa msewu wa M1.
0998712825 Whatsapp on 0882274370.

 CHAGUNDA WAULURA KUTI ANAPHA GOGO WA ZAKA 83  Francis Chagunda (24) akuyembekezereka kukawonekera kubwalo la milandu po...
26/10/2025


CHAGUNDA WAULURA KUTI ANAPHA GOGO WA ZAKA 83

Francis Chagunda (24) akuyembekezereka kukawonekera kubwalo la milandu pomuganizira kuti anapha Violet Nyambale, gogo wa zaka 83 yemwe adakukhala kwa Baluti munzinda wa Blantyre pa 30 August, 2025.

Chagunda waulura yekha kuti adachita izi pomwe apolisi amumanga ku Ndirande pomuganizira milandu yakupha ndi kuba.

Chagunda analowa nyumba ya mayiyu kuti abe ndipo atamuzindikira anaganiza zowapotokola khosi ndikuwapha nyumbamo.

Aubry Kawale, mkulu wa polisi ya Blantyre wati zonsezi oganizilidwayu waulura yekha kotero Malamulo agwira ntchito kwa Chagunda akapezeka olakwa.



ItOffers:
and (color printing printing studio or printing Photo printing
:Sorgin moyandikana ndi Phute Bar mphepete mwa msewu wa M1.
0998712825 Whatsapp on 0882274370.

 ANTHU AWIRI ALANDILA BUNDLE KU D TECH PRINTERS AKAYANKHA MOLONDOLAIfe a DTech Printers timapanga ma service monga awa *...
26/10/2025


ANTHU AWIRI ALANDILA BUNDLE KU D TECH PRINTERS AKAYANKHA MOLONDOLA

Ife a DTech Printers timapanga ma service monga awa
*Photocopy and printing also color printing
*laminating
*Photo printing - passport photo size printing
* t-shirt printing
* binding ndi ma services ena
mukatifuna mutipeza pafupi ndi phute bar moyang'anizana ndi nzikiti wa sorgin ku Nsanje call 0998712825

(MPIRA ULI PATI? anthu awiri ayankhe molondola azalandila bundle ya internet ya week ) ndipo owina azalengezetsedwa mmawa 8pm madzulo, osaiwala kuti ikupangidwa sponsor ndi DTech Printers Visit us today and try DTech simuzakhumudwa. osaiwala kupanga share kuti anzanu awine nawo.

 MAFUPA A MUNTHU APEZEKA MU NKHALANGO   Mafupa a munthu wina yemwe sakudziwika apezeka mu nkhalango ina mudzi wa Phalula...
26/10/2025


MAFUPA A MUNTHU APEZEKA MU NKHALANGO



Mafupa a munthu wina yemwe sakudziwika apezeka mu nkhalango ina mudzi wa Phalula m'boma la Balaka agalu akuwadya.

Mayi wina yemwe anapita ku katola nkhuni ku nkhalango yo ndiyemwe wazindikira pa nthawi yomwe agalu amadya mafupa wa.

"Mayi wina yemwe anapita ku katola nkhuni watitsina khutu pa zankhaniyi ndipo tinapitako ndi achipatala omwe atsikimiza kuti mafupa wa ndi a munthu " watero Gladson M'bumpha, wofalitsa nkhani za apolisi ku Balaka.

M'bumpha wapempha anthu ozungulira dera la Phalula kuti afufuze abale awo ngati akusowa.

Izi zapereka m'thumanzi Kwa anthu okhala kuderalo pa za chitetezo chawo.



ItOffers:
and (color printing printing studio or printing Photo printing
:Sorgin moyandikana ndi Phute Bar mphepete mwa msewu wa M1.
0998712825 Whatsapp on 0882274370.

 JUST IN:   MKAZI WACHIWIRI KWA MKULU WA POLISI AMUPHA    Leonor Inguane, mkazi wa wachiwiri wa mkulu wa polisi mdziko l...
25/10/2025


JUST IN: MKAZI WACHIWIRI KWA MKULU WA POLISI AMUPHA



Leonor Inguane, mkazi wa wachiwiri wa mkulu wa polisi mdziko la Mozambique Bernardino Rafaer waomberedwa usiku watha-wu dera la Marracuene Province ya Cabo Delgado kumene kwatchuka kwambiri ndi nkhondo.

Inguane wakumana nditsokali pomwe amabwelera kunyumba yake kuchokera ku mwambo wokumbukira tsiku lake lobadwa omwe unachitikira dera lomwelo limodzi ndi apolisi anzake.

"Inguane waphedwa ndi achiwembu. Wapezeka mugalimoto atafa pochokera ku birthday" malingana ndi malipoti.

Akuluakulu apolisi mdziko la Mozambique atsikimiziranso malipoti-wa ndipo zapereka mantha aakulu.

Mkazi wachiwiri kwa mkulu wa polisiyu analinso wofalitsa nkhani za apolisi ku Mozambique -ko.

Taika kanema mu bokosi lopereka ndemanga (comment box) yosonyeza kusangalala ku mwambo wake wa tsiku lobadwa.

TheTruthUncovered
ItOffers:
and (color printing printing studio or printing Photo printing
:Sorgin moyandikana ndi Phute Bar mphepete mwa msewu wa M1.
0998712825 Whatsapp on 0882274370.

 ENGLISH AYITHETSA KU GHANA  Ku Ghana, unduna wa zamaphunziro wakhazikitsa ndondomeko yoti msukulu zawo adzigwiritsa ntc...
25/10/2025


ENGLISH AYITHETSA KU GHANA

Ku Ghana, unduna wa zamaphunziro wakhazikitsa ndondomeko yoti msukulu zawo adzigwiritsa ntchito zilankhulo za komko osati chingerezi pofuna kuti ophunzira azimvetsetsa mosavuta.

Ghana ili ndi zilankhula pafupipafupi 80 ndipo mwazina ndi Akan, Ewe, Ga,Dangme, Gonja ndi Nzema.



ItOffers:
and (color printing printing studio or printing Photo printing
:Sorgin moyandikana ndi Phute Bar mphepete mwa msewu wa M1.
0998712825 Whatsapp on 0882274370.

25/10/2025

NEW CURRICULUM: DIPLOMA AND DEGREE A MUST FOR PRIMARY SCHOOL TEACHERS

The Ministry of Education, through the Malawi Institute of Education(MIE), has announced major reforms under a new National Curriculum Framework designed to make education more relevant, inclusive, and skills-driven.

The new curriculum shifts from an Outcome-Based Curriculum (OBC) to a Competency-Based Curriculum (CBC), emphasizing practical, demonstrable skills over rote learning. It also revises the school structure from 8–4–4 to 1–6–6–3, introducing a preparatory class, six years of primary education, six years of secondary school, and three years of tertiary or vocational training.

Secondary education will now follow four distinct pathways: Social Sciences and Humanities, Arts and Sports Science, STEM, and TEVET.

As part of the reform, teacher education is also being upgraded. Primary school teachers will now be required to hold at least a diploma, with degree qualifications encouraged, to ensure they can effectively deliver the revised curriculum.

The curriculum aims to align with Malawi 2063, preparing learners for digital innovation, critical thinking, and 21st-century skills. MIE has already completed needs assessment, a national symposium, and curriculum conceptualisation, with syllabus development and teacher training underway.

Implementation will be phased, beginning with selected grades once all teaching materials and training are ready.

Executive Director of MIE, Dr. Frank Mtemang'ombe, said the reform marks a major step toward building a modern, inclusive, and skills-oriented education system that will "equip learners with the knowledge, skills, and values necessary to build a self-reliant and industrialised Malawi.

Ministry of Education - Malawi
Malawi Government

 NTHENDA YA TB YAGWIRA AKAIDI 10 KU NDENDE YA NSANJE  Nthenda ya chifuwa chachikulu (TB) yagwira akaidi khumi ku ndende ...
25/10/2025


NTHENDA YA TB YAGWIRA AKAIDI 10 KU NDENDE YA NSANJE

Nthenda ya chifuwa chachikulu (TB) yagwira akaidi khumi ku ndende ya Nsanje ndipo akulandira thandizo la mankhwala.

Akaidiwa omwe awasiya pawokha kuopa kupatsira anzawo nthendayi, apitilira kumwa makhwala mwezi wa December chaka chino ndipo akuluakulu a ndendeyi ati pali kusintha kwakukulu.

Chifuniro Mukhuna, wofalitsa nkhani pa ndende ya Nsanje wauza Nyumba yofalitsa nkhani ina mdziko muno (Zodiak) kuti akuchita chotheka kuti akambirane ndi bungwe la Partiners in Hope kuti ayambe ntchito yoyeza akaidi a ndendeyi kuti adziwe mmene zinthu zikuyendera mu mwezi wa December.

Kuthinana ndi vuto lalikulu pa ndende ya Nsanje yomwe ikusunga akaidi 300 mmalo mwa 120.


: ZBS

ItOffers:
and (color printing printing studio or printing
:Sorgin moyandikana ndi Phute Bar mphepete mwa msewu wa M1.
0998712825 Whatsapp on 0882274370.

25/10/2025


BWALO LA MILANDU LAKANA PEMPHO LA KHEMBO

Texious Masoamphambe, woweruza mlandu wa bwalo lalikulu munzinda wa Blantyre wakana pempho la Linda Khembo yemwe adaimira pa mpando wa phungu wa Nyumba ya Malamulo kumpoto kwa boma la Chikwawa pa chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) kuti Geoffrey Onsewa yemwe adapambana ngati wa independent asamulumbilitse ponena kuti padachitika chinyengo pa kuwerengera ma voti ku Mfera pa 16 September, 2025.

Bungwe la MEC lomwe lidali loyankha oyamba pa mulanduwu lati zomwe Khembo adakadandaula kuti woyang'anira ake sadasaine zotsatira za chisankho zidali zabodza.

Naye Onsewa pokhala woyankha wachiwiri wati iye akuyenera kumulumbilitsa chifukwa adapambana ndipo wati chiletso cha Khembo mchosagwira mtima chifukwa bungwe la MEC simalumbilitsa aphungu.

Linda Khembo amulamuranso kupereka chindapusa.

 ANTHU AMAFUNA KUMUOTCHA POMUGANIZIRA UFUTI  Polisi Unit ya Fatima m'boma la Nsanje ikusunga mayi wina yemwe zaka zake z...
25/10/2025


ANTHU AMAFUNA KUMUOTCHA POMUGANIZIRA UFUTI

Polisi Unit ya Fatima m'boma la Nsanje ikusunga mayi wina yemwe zaka zake zobadwa ndiza pakati pa 60 mpaka 70 yemwe sakudziwika kwawo.

Anthu ena osadziwika a m'mudzi wa Chomboto mudera la mfumu yaikulu Mlolo m'boma la m'bomalo amafuna kumuotcha pomuganizira kuti wagwa pa ndege ya ufuti pa 17 October, 2025 ndipo zinatengera apolisi kukamupulumutsa.

Jabulani Ng'oma, wachiwiri kwa wofalitsa nkhani za apolisi m'boma la Nsanje wapempha anthu omwe akudziwa abale a mayi-yu yemwe ali pa chithunzi-pa kuti apite ku polisi ya Fatima kuti akamutenge.

Address

Chikwawa

Telephone

+265990485072

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when PortHerald Press posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

  • Want your business to be the top-listed Media Company?

Share