08/08/2025
Kwaya ya Balaka yakonzeka ndi DVD
Kwaya ya Balaka CCAP yati zonse zili mchimake kukhazikitsa kanema owonera wa nyimbo (DVD) Lamulungu pa 10 Ogasiti 2025, ku mpingowu nthawi ya 1 koloko masana.
Malingana ndi mkulu woyang'anira kwayayi a Masauko Kapiye, iwo akukhazikitsa DVD kaamba koti atatulutsa CD ya Mwakhristu Tikondane, anthu anayilandira bwino.
"Chimbalechi ndi choyamba ndipo titatulutsa chinapereka chikoka kwambiri zimene zinatilimbikitsa kuti tijambule DVD choncho taona ukulu wa Mulungu chifukwa makonzekeredwe athu akuonetsa kuti anthu achilandira ndi manja awiri," anatero a Kapiye.
Pakadali pano, iwo ati agulitsa kale matiketi olowela pakhomo okwana 500.
"Taitana makwaya ambiri akunja kwa Balaka komanso aku Balaka kuno kuphatikizapo amu mpingo mwathu kuti adzakometse mwambowu," anatero a Kapiye.
Katswiri woimba nyimbo zauzimu Favoured Martha ndi mmodzi mwa oimba omwe adzakhale nawo pa mwambowu. Mlendo wolemekezeka ndi a Simplex Chithyola Banda, nduna yowona zachuma.
Matikiti olowela pa khomo ndi K1000 munthu akakuguliratu pano koma kudzagula pa khomo pa tsikulo ndi K1,500.
Wolemba: Rose Chipumphula CHALIRA