Mabungwe Akuchitanji News Online

  • Home
  • Mabungwe Akuchitanji News Online

Mabungwe Akuchitanji News Online MA NewsOnline//The Real Voice of Organizations, Companies and Individuals
(1)

01/11/2025
 Mwambo wolumbilitsa nduna, otsatira kwa ndunazi komanso akuluakulu a nthambi zina uchitika lero pa 2 November ku BICC m...
01/11/2025


Mwambo wolumbilitsa nduna, otsatira kwa ndunazi komanso akuluakulu a nthambi zina uchitika lero pa 2 November ku BICC mu mzinda wa Lilongwe.

Mwambowu umayenera kuchitika loweluka pa 1 November koma panali kusintha kwina kaamba ka zifukwa zina.

Malingana ndi kalata yomwe mtsogoleri wa dziko lino Professor Arthur Peter Mutharika watulutsa mwambowu uyamba nthawi ya 2 koloko masana ndipo mtsogoleri wa dziko linoyu ndiye atsogolere mwambowu.

NewsOnline Kukupatsirani Nkhani Zamabungwe/Kampani/Ndi Anthu ena

 Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Dr.Jane Ansah wati boma lipitilira kuthandiza achinyamata kuti apitilire kukhala...
01/11/2025


Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Dr.Jane Ansah wati boma lipitilira kuthandiza achinyamata kuti apitilire kukhala patsogolo pothandiza kupititsa patsogolo ntchito za chitukuko cha dziko lino.

Dr.Ansah anena izi kudzera mu kalata yawo yomwe atulutsa loweluka pomwe dziko lino mogwilizana ndi maiko ena limakumbukira tsiku la wachinyamata wamu Africa.

NewsOnline Kukupatsirani Nkhani Zamabungwe/Kampani/Ndi Anthu ena

 Iyi ndi kabinenti yonse ya mtsogoleri wa dziko lino Professor Arthur Peter Mutharika.Kabinentiyi yatuluka lachinayi lap...
01/11/2025


Iyi ndi kabinenti yonse ya mtsogoleri wa dziko lino Professor Arthur Peter Mutharika.

Kabinentiyi yatuluka lachinayi lapitali ndipo onse alipo anthu 24 womwe ndi kuphatikidzaponso mtsogoleriyu.

NewsOnline Kukupatsirani Nkhani Zamabungwe/Kampani/Ndi Anthu ena

 Here is President Professor Arthur Peter Mutharika's Full Cabinet.The Full Cabinet which was released on last Thursday ...
01/11/2025


Here is President Professor Arthur Peter Mutharika's Full Cabinet.

The Full Cabinet which was released on last Thursday comprises of 24 Officials including the President him self.

NewsOnline The Real Voice of Organizations/Companies/Individuals

 "MASIPIKALA INU,GWIRANI NTCHITO MOKOMERA IFE AMALAWI"-Mbadwa ZokhudzidwaGulu lina lomwe likudzicha Mbadwa Zokhudzidwa l...
01/11/2025


"MASIPIKALA INU,GWIRANI NTCHITO MOKOMERA IFE AMALAWI"-Mbadwa Zokhudzidwa
Gulu lina lomwe likudzicha Mbadwa Zokhudzidwa lapempha anthu omwe asankhidwa kukhala sipikala wa nyumba yamalamulo komanso achiwiri kwa sipikalayu kuti agwire ntchito yawo moyenera pothandiza kupititsa patsogolo ntchito zanyumbayi.

Wapampando wa gululi Billy Malata ndiye wapereka pempholi lachisanu lapitali mu m'zinda wa Lilongwe pa msonkhano wa atolankhani womwe anakonza pofuna kufokozera zokhudza izi.

Iwo ati a Sameer Suleman omwe tsopano ndi sipikala wa nyumbayi akuyenera kugwirana manja ndi aphungu onse akunyumbayi powonesetsa kuti zokambirana zawo zikulunjika kwambi pa nkhani yopititsa patsogolo aMalawi komanso chitukuko cha dziko lino.

A Malata ayamikiranso mtsogoleri wa dziko lino Professor Arthur Peter Mutharika kaamba kosankha achinyamata maudindo akuluakulu pofuna kuti anthuwa akhale akhale patsogolo pa ntchito yothandiza kutukula dziko lino.

Pakadali pano gululi lati likuyembekeza kuti yemwe chipani chotsutsa boma cha MCP chamusankha kukhala mtsogoleri wa zipani zotsutsa boma kunyumba yamalamulo a Simplex Chithyola Banda athandiza kuti boma likonze mavuto omwe anthu mdziko muno akukumana nawo.

NewsOnline Kukupatsirani Nkhani Zamabungwe/Kampani/Ndi Anthu ena

 "INU KU TANZANIA-KO TAKHUMUDWA NANU KWAMBIRI"-SADCBungwe la SADC lati lakonzeka pofuna  kukhazikitsa  bata ndi mtendere...
01/11/2025


"INU KU TANZANIA-KO TAKHUMUDWA NANU KWAMBIRI"-SADC
Bungwe la SADC lati lakonzeka pofuna kukhazikitsa bata ndi mtendere mdziko la Tanzania.

Mu kalata yomwe wasainira ndi wapampando wa nthambi yowona za chisankho ku bungweli yemwenso ndi mtsogoleri wa dziko lino Professor Arthur Peter Mutharika bungweli ladandaula ndi chiwerengero cha anthu omwe afa komanso kuvulala kaamba ka ziwonetsero zomwe zakhala zikuchitika mdzikolo kuchokera pomwe anthu anaponya voti.

Mu kalatayi bungweli lapempha atsogoleri a zipani zandale m'dzikolo komanso magulu ena okhudzidwa kuti aganinizire za moyo wa anthu ndi kukambirana njira zoyenera zothanirana ndi vutoli.

Pakadali pano bungweli lapempha apolisi kuti agwire ntchito yawo moyenera pomwe akubweretsa bata ndi mtendere.

NewsOnline Kukupatsirani Nkhani Zamabungwe/Kampani/Ndi Anthu ena

 "A BUSHIRI ASAPITE KU JONI KUKAYANKHA MILANDU'-KhotiBwalo lamilandu lalikulu ku Lilongwe lachisanu lagamula kuti mnenel...
01/11/2025


"A BUSHIRI ASAPITE KU JONI KUKAYANKHA MILANDU'-Khoti
Bwalo lamilandu lalikulu ku Lilongwe lachisanu lagamula kuti mneneli Shepherd Bushiri ndi mkazi wawo Mary asatumizidwe mdziko la South Africa kuti akayankhe milandu yomwe akuganizilidwa kuti anapalamula.

Popereka chigamulo chake oweluza milandu ku bwaloli Justice Mzondi Mvula anati bwalo lamilandu la Chief Resident Magistrate lomwe linagamula kuti awiriwa atumizidwe m'dzikolo linalakwitsa.

A Mvula anatinso a Bushiri sanapatsidwe mpata kuti afokotozera bwino kumbali yawo pomwenso bwaloli linalephera kupereka chigamulo chake moyenera kaamba ka zifukwa zina.

NewsOnline Kukupatsirani Nkhani Zamabungwe/Kampani/Ndi Anthu ena

Address

Street 5

MANEWSONLINE

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Mabungwe Akuchitanji News Online posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

  • Want your business to be the top-listed Media Company?

Share