
01/07/2025
Yemwe anali mtsogoleri wa bungwe loyimira ophunzira amnzawo ku sukulu yaukanjede ya Malawi bambo Humble SC Bondo, akufuna kuchita chionetsero komanso m'bindikiro ku ma ofesi a utsogoleri wa sukulu ya ukachenjede ya Malawi, Zomba pokwiya (Justice Awaiting Demonstration and Vigil_ JADGIL) ndi kuchedwa kwa chigamulo pa mlandu womwe sukulu inagamula zaka ziwiri zapitazo.
Poyambirira, bwalo lamilandu lalikuru (High Court) linagamula kuti bambo Bondo, sanamalizitse zonse zoyenera pa pempho lawo lofuna kuunikiranso chigamulo chimene anapatsidwa poyamba ndi sukuluyi chomwe chinabwera pomwe amafuna kupanga m'bindikiro.
Bondo wati ngakhale anachita zonse zoyenera koma mpaka pano sikunabwerebe yankho lililonse ngakhale matsiku omwe bwalo lamilandu linalamula adutsa.
"M'bindikirowu udzayamba pa 09 July 2025 ndipo udzatha tsiku lomwe utsogoleri wa sukulu ya ukachenjede ya Malawi udzatulutse chigamulo pa nkhaniyi," atero a Bondo.
Mwazina zomwe bambo Bondo akudzachita mu m'bindikirowu ndi monga; kunyamula bokosi loika maliro lolembedwa "Uwutse mu Mtendere utsogoleri wa zachilungamo wapa sukulu ya ukachenjede ya Malawi" tsiku lilionse, ulaliki, mapemphero komanso kutsala kudya.
Sukulu yaukanjede ya Malawi inayimitsa pa sukulu Bondo kwa zaka zinayi mu chaka cha 2024 pa mlandu omuganizira kuti amkafuna kuchita zinthu zomukopa msungwana wina kuti agone naye.
Wolemba Moses Dyson Supuni.