Ceyome Media

Ceyome Media We are youthful and fruitful

Places are still available at Mubarak Complex College situated in St Mary's in Zomba City. Programs offered:Computer Eng...
11/04/2025

Places are still available at Mubarak Complex College situated in St Mary's in Zomba City.

Programs offered:
Computer Engineering
Human Resource Management
Business Management
Public Health
Community Development and Social Work
>Plumbing
>Tailoring and fashion Designing
>Project Management
>Information Communication Technology

AND MANY MORE!!!!!!

For more information, please contact: 0994986201

Phungu wadera la pakati m'boma la ntcheu Dr Albert Mbawala ati zomwe wachita president Chakwera mzogometsa.Iwo ati dziko...
17/02/2025

Phungu wadera la pakati m'boma la ntcheu Dr Albert Mbawala ati zomwe wachita president Chakwera mzogometsa.

Iwo ati dziko lino lasintha mu ngodya za mbili kamba ka ulamuliro wa maso mphenya womwe achakwera alinawo.

Mbawala ayankhula izi lolemba masana kunyumba ya malamulo pomwe amayankhapo pa zomwe achekwera anayankhula nthawi yomwe amatsekulira zokambilana zanyumbayi lachisanu sabata Latha

Izi zili chomwechi pomwe anthu ochuluka akulankhulapo zokhudzana ndi zomwe achakwera anayankhula.

08/12/2024
04/12/2024

Phungu wa chipani Cha Democratic Progressive (DPP) ku dera la Machinga likwenu a Bright Msaka ati chipani chawo sichikugwirizana ndi bill yokhudza kagulidwe kamafuta agalimoto kamba koti bill yi siipindulira nzika za dziko lino.

A Msaka ayankhula izi lachiwiri sabata ino pamene anapatsidwa mpata kuti aimilire chipani cha DPP polankhulapo pa bill yi pamene nduna yazamphanvu a Ibrahim Matola anapeleka bill yi m'nyumba yamalamulo.

Iwo ati boma la MCP likufuna kutenga ngongole zambiri pogwilitsa ntchito bill yi pofuna kusiya ngongole zochuluka m'boma,ku utsogoleri omwe udzayambe kulamulira m'dziko lino chaka chamawa.

Iwo ati boma la MCP livomeleze kuti likusowa ntengo ogwila kuti athane ndi vuto lakusowa kwamafuta ndichifukwa akufuna kusintha kwanjira zakagulidwe kamafuta pogwilitsa ntchito njira ya tsopano kuti dziko lino lidzigula mafuta kudziko linzake osati kugula mafutawa kwa ankhala pakati omwe ndi kampani zogulitsa mafuta agalimoto wa m'maiko omwe muli madoko amafuta.

CEYOMENEWS - LILONGWE.
Copied.

02/12/2024

Zinali uku

28/11/2024

Mtsogoleri wa chipani cha UTM Dr Dalitso kabambe auza mtsogoleri wadziko lino Dr Lazarus chakwela kuti achotse mmaudindo a zikhale Ng'oma komaso mkulu wa apolisi a mellin Yolamu kamba kolephera kutumikila amalawi

A Kambambe ayankhula izi pa msokhano wa atopa nkhani womwe unachitikila ku likulu la chipanichi mu mzinda wa Lilongwe

Iwo ati a Malawi atopa ndi ulamuliro wopsyeza boma womwe boma la Malawi congress party motsogozedwa ndi Dr Lazarus Chakwera akuchita

Mwazina adzudzula anthu ena omwe akugwilitsidwa ntchito ndi a Ndale kuchita za Mtopola zomwe ati zikhiza kuyambitsa chiwawa.

Mwazina akhudzanso mbali zingapo zomwe dziko likuphera kutumikila mzika zake, ena mwa mavutiwa ndi monga kusowa kwa mafuta galimoto, njala ngakhaleso kusowa kwa ntchito.

Pomaliza iwo apeleka mawu achilimbikitso kwa mzika za malawi kuti zinthu zisintha Chipanichi chikalowa m'boma pachisankho cha chaka chamawa.

Thomas phiri, Ceyome news Lilongwe.

Anthu ochuluka asonkhana pa malo otchedwa stop ku mchezi mu mzinda wa Lilongwe kuyembekezera mtsogoleri wadziko lino yem...
28/11/2024

Anthu ochuluka asonkhana pa malo otchedwa stop ku mchezi mu mzinda wa Lilongwe kuyembekezera mtsogoleri wadziko lino yemwe akuchititsa misonkhano yoimayima kulimbikitsa anthu kuti akalembetse mkaundula ozaponya voti chaka cha mawa.

Thomas phiri

26/11/2024

Nduna yoona za mtenga tenga ndi zomanga manga a Jecob Hara

Ati boma kludzera muundunawu liyesetsa kuti limalize ina mwa misewu yomwe inayambidwa kale nyengo ya mzula isanafike pamponda chimera

iwo ayankhula izi lolemba ku nyumba ya malamulo pomwe amayankha mafuso kwa ena mwa aphungu omwe ali ndivuto lamisewu kudera kwawo.

nyumba ya malamulo aitskulila lolemba pa 25 november ndipo idzatha pa 20 December 2024.

Thomas phiri-Lilongwe

16/11/2024

Mtsogoleri wa kale wa dziko lino yemweso ndi mtsogoleri wachipani chotsutsa boma cha Dpp peter mutharika ati iwo azabwezeletsa zinthu zomwe zinasamutsidwa ndi boma kuchoka mu mzinda wa Blantyre kupita ku Lilongwe.

A mutharika ayankhula izi ku Blantyre pa mwambo womwe unakozedwa ngati njira yopezera ndalama zogwilitsila ntchito zisiyanasiyana zachipani ku malo ogona alendo a golden peacock ku Blantyre.

Ceyomenews Blantyre.

Anthu okhala mmidzi yosiyana siyana monga Mnyaka, mwangata, Naliwa ndi ina yambili pansi pa gulupu village wagata kuchin...
22/10/2024

Anthu okhala mmidzi yosiyana siyana monga Mnyaka, mwangata, Naliwa ndi ina yambili pansi pa gulupu village wagata kuchingale m'boma la zomba akadali kakasi kusowa pogwila kutsatila kuonongeka kwa nyumba ndi mvula ya mphepo yomwe inagwa mmwezi wa October chaka chino.

Atayendera midziyi phungu wa dera la zomba chingale a Lonnie phiri apeza kuti maanja ochuluka ali pamavuto adzaoneni kutsatila ngoziyi.

Iwo ati izi zikupereka mafuso kamba ka nyengo ya mvula yomwe ikudzayi, mwazina apempha boma, mabungwe ndi anthu akuna kwabwino kuti akumbukile kuchereza anthu omwe akukumana ndi mavuto angozi zogwa mwadzidzi ndipo alangizaso anthuwa kuti apewe mchitidwe okolezera ngozizi monga kudula mitengo mosasamala

Boma la zomba ndi limodzi mwa maboma omwe amakumana ndi mavuto adzaoneni maka njala ngakhaleso ngozi zonga izi.

By Thomas phiri- Zomba.

06/10/2024

Big shout out to my newest top fans! Felister Banda

Address

Zomba

Telephone

+265994986201

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Ceyome Media posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Business

Send a message to Ceyome Media:

Share