New Muslim Family

New Muslim Family ๐ŸŽค NMS TV
An Islamic media platform supporting New Muslims in Malawi
๐Ÿ“บ Daโ€™wah โ€ข Interviews โ€ข Outreach
๐Ÿ“ž +265 986 691 40

14/08/2026
14/08/2026

โœจ NEW MUSLIM STORY | PHALOMBE โ€“ T/A NAZOMBE ๐Ÿ•Œ๐Ÿค

๐Ÿ’” โ€œNdawona kusintha kwakukulu pamoyo wanga pamene ndinalowa Chisilamuโ€ฆโ€

Uyu ndi m'bale wathu wochokera ku Phalombe, T/A Nazombe, amene adagawana nkhani yake yosangalatsa komanso yokhudza mtima. ๐Ÿคฒ

Asanalowe Chisilamu, akunena kuti sanali kudziwa bwino njira yolondola yopembedzera ndipo anakhala zaka zambiri osazindikira zambiri zokhudza chipembedzo. ๐Ÿ˜ข

Koma Alhamdulillah ๐Ÿค, anthu ophunzitsa Chisilamu anafika kumudzi kwawo ndipo adamulalikira za Chisilamu. Kudzera mu maphunzirowo, iye anapeza chowonadi ndipo anayamba kudziwa njira yolondola yopembedzera Allah. ๐Ÿ•Œโœจ

Masiku ano akuti wadziwa mmene Msilamu ayenera kukhalira, kuphatikizapo kapempheredwe koyenera komanso kavalidwe ka munthu wokhulupirira. ๐Ÿคฒ๐ŸŒ™

โ€œNgakhale Allah wandipatsa chisomo cholowa Chisilamu, mtima wanga umalira chifukwa cha abale anga amene ali m'zipembedzo zina. Ndikufuna adziwe chowonadi chimene ndaphunzira.โ€ ๐Ÿ’”

Akunena kuti ena amamunyoza nโ€™kumuuza kuti walowa chipembedzo choipa, koma iye akuyesetsa kuwafotokozera moleza mtima kuti Chisilamu chimaphunzitsa kupembedza Mulungu mmodzi yekha komanso kuti Yesu (Isa) ndi Mtumiki wa Mulungu. ๐Ÿค

๐ŸŒ™ Khumbo lake lalikulu ndi kuona abale ake komanso anthu ambiri akudziwa chowonadi ndi kutsatira njira ya Chisilamu. ๐Ÿคฒ

Allah awatsogolere onse ku njira yolondola. ๐Ÿค

๐Ÿ“บ NMS TV โ€“ New Muslim Story
๐ŸŽฅ Tikubweretsa nkhani za anthu amene apeza chikhulupiriro chatsopano.

14/08/2026

๐Ÿ”ฅ EPISODE 1 YATULUKA! ๐Ÿ”ฅ

NEW MUSLIM STORY โ€“ CHILINGA, PHALOMBE ๐Ÿ•Œ๐Ÿคฒ๐Ÿฝ

Alhamdulillah! Tidapita ku Chilinga, Boma la Phalombe, kukakumana ndi ma New Muslim ndi kumva nkhani za moyo wawo komanso ulendo wawo wolowa mu Chisilamu.

๐ŸŽฅ Athu onse, mukawone Episode 1 pa YouTube. MUSAPHONYE! โค๏ธ

๐Ÿ‘‰๐Ÿฝ ONANI APA: https://youtu.be/qaYNi6I5XxA?si=Oy0wHDnMihfP134g

๐Ÿ‘ Like | ๐Ÿ’ฌ Comment | ๐Ÿ”” Subscribe ku NMS TV

13/06/2026

Zivute zitani, koma nyama ya khumba Allah adaletsa. Siyani kudya khumba, bwerani ku Chisilamu ndipo mudziwe choonadi."

ASSALAMU ALAYKUM WA RAHMATULLAHI WA BARAKATUHDear brothers and sisters in Islam,One of our responsibilities as Muslims i...
13/06/2026

ASSALAMU ALAYKUM WA RAHMATULLAHI WA BARAKATUH

Dear brothers and sisters in Islam,
One of our responsibilities as Muslims is to welcome, support, and care for those who have recently embraced Islam. New Muslims often face many challenges and need encouragement, guidance, and a strong Muslim community around them.

At NMS TV, we started this platform with the vision of ensuring that New Muslims never feel alone. We strive to walk alongside them, support them in their Islamic journey, and help them become strong and confident Muslims.

Through our work, we have met many New Muslims who are in need of:
Islamic education and mentorship
Qurโ€™ans and Islamic learning materials
Hijabs and Islamic clothing
Basic necessities and welfare support
Emotional and spiritual encouragement
However, NMS TV cannot accomplish this mission alone. We believe that if we unite as one Ummah, we can make a real difference in the lives of New Muslims across Malawi and, by the will of Allah, throughout Africa.

We kindly invite everyone who understands the importance of supporting New Muslims to join us in this noble cause. Whether through donations, ideas, volunteering, or sharing our mission, your contribution can help transform lives.

If you have suggestions on how NMS TV can improve and reach more people, please do not hesitate to contact us.

๐Ÿ“ž Contact: +265 986 691 403
๐Ÿ‘ค Ishmael John Sankhani
๐Ÿ“ Phalombe, Malawi

Together, let us support New Muslims and help them grow in faith. United, we can achieve more.

NMS TV โ€“ Supporting New Muslims, Building Stronger Communities. ๐Ÿ•Œ๐Ÿค๐Ÿ“บ

ASSALAMU ALAYKUM WA RAHMATULLAHI WA BARAKATUH

Abale ndi alongo athu a Chisilamu, pali udindo waukulu umene tili nawo wothandiza ndi kulandira bwino anthu amene angolowa kumene mu Chisilamu (New Muslims). Anthu amenewa amasiya zambiri pa moyo wawo chifukwa cha kusankha choona, choncho amafunikira chikondi, chithandizo, ndi kulimbikitsidwa kuchokera kwa ife.

Ife a NMS TV tinayambitsa ntchito imeneyi ndi cholinga choti ma New Muslim asamadzimve okha kapena kusiyidwa. Tikufuna tiziyenda nawo limodzi, kuwathandiza kuphunzira Chisilamu, ndi kuwathandiza pa zosowa zina zimene amakumana nazo.

Pa ntchito yathu, takumana ndi ma New Muslim ambiri omwe akusowa zinthu zosiyanasiyana monga:
Maphunziro a Chisilamu
Ma Qur'an
Mikanjo ndi ma Hijab
Thandizo la moyo wa tsiku ndi tsiku
Kulimbikitsidwa ndi upangiri
Koma ife a NMS TV sitingathe kuchita zonse patokha. Choncho tikupempha abale ndi alongo onse kuti tigwirane manja pothandiza ma New Muslim ku Malawi komanso mtsogolo kufikira m'madera osiyanasiyana a Africa.

Ngati mukudziwa kufunika kothandiza ma New Muslim, kapena muli ndi malingaliro omwe angathandize kukulitsa ntchito ya NMS TV, musazengereze kulankhula nafe. Malingaliro anu ndi chithandizo chanu zingathandize kusintha moyo wa anthu ambiri.

๐Ÿ“ž Contact: +265 986 691 403
๐Ÿ‘ค Ishmael John Sankhani
๐Ÿ“ Phalombe, Malawi
Tiyeni tigwirane manja pothandiza ma New Muslim. Pamodzi tingathe zambiri.
โ€œWothandiza m'bale wake, Allah amamuthandizanso.โ€
NMS TV โ€“ Walking Together with New Muslims. ๐Ÿ•Œ๐Ÿค๐Ÿ“บ@

12/06/2026

Kodi Munthu Akalowa Chisilamu Ndiye Kuti Wamusiya Yesu? Yankho Lingakudabwitseni!

10/06/2026

Inshaallah Yunus James Becks Ibrahim Malawian Arabic Teacher Joyson Kev Agogo Amuna Elias M. Pemba Abdullah Moyo William Jazeel
Abdul Rasheed Hassan

Alhamdulillah! ๐ŸคฒZikomo kwa onse amene athandiza kuti Page ya NMS TV ibwerere. Ngakhale panali mavuto ndi zosokoneza, ler...
10/06/2026

Alhamdulillah! ๐Ÿคฒ

Zikomo kwa onse amene athandiza kuti Page ya NMS TV ibwerere. Ngakhale panali mavuto ndi zosokoneza, lero tikuthokoza Allah chifukwa cha kupambana kumeneku.

Kwa amene anachita zimenezo, sindili nawo mangawa. Ndikukhulupirira kuti Allah ndiye Woweruza wabwino koposa.
Tiyeni tipitilize kusatira NMS TV, kugawana mauthenga abwino, ndi kufalitsa uthenga wa Chisilamu.

Ine ndili wokondwa kwambiri. Alhamdulillah! ๐ŸŒ™๐Ÿ“–

10/06/2026

Jazakumullahu Khayran. ๐ŸŒน
Page iyi yabwelela ndithu Alihamdullah

07/06/2026

Malawi Muslim motivate speech and Tidziwe chisilamu chikutinji Elias M. Pemba NMS TV Idris Habeeb Becks Ibrahim Yunus James Agogo Amuna Abdullah Moyo William Jazeel Malawian Arabic Teacher Abdul Rasheed Hassan Abbas Damson Amini Maliro Abudllah Karimmu Khadija inussah

Address

Zomba

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when New Muslim Family posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share

Category