07/13/2026
Bungwe la Beauty Malawi pamodzi ndi mtsogoleli wa dziko Professor Arthur Peter Mutharika komanso mai wa fuko madame Getrude Mutharika apeleka katundu osiyanasiyana kwa anthu amene afika kuchoka ku South Africa kuthawa Xenophobia.
Katunduyu wapelekedwa pa Joice Chitsulo stadium m'boma la Mwanza komwe anthuwa akumafikila.
Mmau ake mkhalapampando wa bungweli a Dingswayo Jele anati mtsogoleli wadziko lino komanso mayi wa fuko ndi okhudzika kwambiri ndi mavuto amene a Malawi akumana nao m'dziko la South Africa.
Katundu amene wapekedwa ndi wa ndalama pafupifupi 100 million kwacha. Mwa zina pali zofunda, ufa, soap ndi sugar.