Urban Trends

Urban Trends Chimbota Radio: Your hub for arts, culture, entertainment, and sports across Malawi. Tune in now.
(1)

30/05/2026

Koma Bwana awa Ntchito amaigwila eshiiiii🙊🙊

29/05/2026

Simene kunalili ku C U congratulations 🎉 ma Graduate Nonse

  NewsMayi Annie Debre Mumba, omwe anali akazi awo a Professor Peter Mumba, atisiya. Mayi Mumba analamulidwa mbuyonu ndi...
26/05/2026

News
Mayi Annie Debre Mumba, omwe anali akazi awo a Professor Peter Mumba, atisiya.

Mayi Mumba analamulidwa mbuyonu ndi court lalikulu kuti anapha amuna awo, omwe ankaphunzitsa Chemistry ku LUANAR, powamwetsa poison ndipo anawalamula kukakhala kundende zaka zokwana 53.

Koma bwalo lalikulu la Appeal (Supreme Court of Appeal) linawatulutsa pa bail a Mumba kamba kopeza kuti bwalo la High Court silinalinganize umboni wina bwino bwino ndipo pamafunikanso kuwona ngati chigamulo cho chinali cholondola.

Mayi Mumba amwalira bail ili mthumba. Ndipo siwa ikuchitikila ku Area 38 kufupi ndi ku Ntaya komwe Iwo amakhala. Akhala asakumva bwino

Thupi lawo liyikidwa mmanda ku Area 28 ku Lilongwe

25/05/2026

Koma Atsikana amu Sana ya Mulimbe Ali ndi Mwano ngati samapita kwawo eeeeee🙆🙆🙆🙊🙊🙊

25/05/2026

Prophet from Malawi what is it🙊🙊🙊

25/05/2026

Sha 😁 Amfumu nawo ndi Munthu nde Iyishoshatu akuti afumu kwawo komweko🤣🤣🤣iye akufuna zake amupatse ntchito ndi yolemetsa yomwe wagwila😂😂🙌

Sizinayendetu apapa🥹🥹🥹🥹Anthu asanu ndiomwe avulala pangozi yapansewu yomwe yachitika pa Bawi m'boma la Ntcheu.Mneneli wa...
24/05/2026

Sizinayendetu apapa🥹🥹🥹🥹

Anthu asanu ndiomwe avulala pangozi yapansewu yomwe yachitika pa Bawi m'boma la Ntcheu.

Mneneli wa polisi ya Ntcheu a Jacob Khembo ati mwa anthu asanuwa awiri anali mu lorry pomwe atatu mu bus ya SOSOSO.

A Khembo ati anthuwo sadavulale modetsa nkhawa ndipo akhonza kutulutsidwa mchipatala lero lomwe.

Ngoziyi yachitika lero lorry itaombana ndi bus ya SOSOSO.

Tiwapepesele Chabwino kuti Sorry 😔 Chithuzi mukuchionachi ndi bambo wina amene akuti anaakaba mbatata minda yaku Barrack...
24/05/2026

Tiwapepesele Chabwino kuti Sorry 😔

Chithuzi mukuchionachi ndi bambo wina amene akuti anaakaba mbatata minda yaku Barracks dzulo, ndiye thumba limakanika kuchoka paphewa. Anthu anakumana ndi bambowa ku zikomo flowers koma akuoneka ofooka kwambiri chifukwa akuti thumbali anali ataliseza chama mamawa wa dzuloro.

Mwini wa munda wa mbatatawu sakudziwika kuti ndindani ndipo bambowa anali atabalalika chifukwa sankadziwa kuti akapepesa kwandani. Chonde amene mukudziwa kuti mudalima mbatata mimda yaku Barracks ndipo mudatsilika chonde athandizeni abambowa. Akakhala pasi kuti atule akuti thumbali likungokhala ngati lamamatira kumnofu wathupi lawo ndipo akumava kupweteka kwambiri...
*Zinaa ukamva*

Mwaionela kale?Mai Wina waziyanika ku Machinjiri... Nkhani ikumveka kuti alipo yemwe  amamutumizila 🫘 koma mwatsoka zapi...
24/05/2026

Mwaionela kale?
Mai Wina waziyanika ku Machinjiri... Nkhani ikumveka kuti alipo yemwe amamutumizila 🫘 koma mwatsoka zapita ku Gulu🙊🙊🙊

23/05/2026

Nde Chimadziwa kukanyanga Mnsambo🙆🙆🙆Bass gutter ikamuona imamwetulila😎His Name is Chitsanzo Mwana akubwela bwino uyu anyway Happy birthday Mr Bass gutter Man 🤗🤗🤗We wish you well pa ulendo okanyanga Mnsambo mwaluso komaso mopeleka Chikoka😎😎😎

LA40😳😳lilibe wait kayeZigawenga ziwiri zomwe zakhala zikukhapa ndikubera anthu opemphera mu phiri la Soche ku Blantyre, ...
23/05/2026

LA40😳😳lilibe wait kaye

Zigawenga ziwiri zomwe zakhala zikukhapa ndikubera anthu opemphera mu phiri la Soche ku Blantyre, tsopano zagamulidwa kukakhala ku ndende kwa zaka 20 popezeka olakwa pa milandu yakuba.

Opezeka olakwawa ndi Martin Brighton wa zaka 41 ndi Jackson Mahomba wa zaka 31 ochokera m'boma la Thyolo.

Oweruza ku bwalo la mlandu la Blantyre Senior Resident Magistrate Godfrey Mchilima wapereka chilangochi pa 22 May 2026, kutsatira awiriwa kuvomera milandu isanu yokhudza kubera anthu opemphera mu phiri la Soche mwazina.

Padakali pano awiriwa akhale akuyankhanso mlandu wokupha m'busa wina Chisambi wazaka 76 wa utumiki wa The Will of God Ministries, yemwe anamupha pa 6 May 2026, atapita kukapemphera komanso kuthilira maluwa pa gome lake mu phirili.

Bwaloli latumiza mlandu wakuphawu ku bwalo lalikulu, komwe awiriwa azikayankha uku akuseweza ukayidi pa milandu yomwe agamulidwayi.

Address

Machinjiri
Lilongwe

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Urban Trends posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share