
25/05/2025
Nkhamu la undipondera mwana lasonkhana pa bwalo la za masewero la Dowa boma pomwe pakhale nsonkhano wa chipani cha Malawi Congress (MCP).
Alendo olemekezeka pa nsonkhanowu ndi mlembi wa mkulu wachipanichi yemwenso ndi nduna ya za maboma ang'ono ang'ono ndi chikhalidwe a Richard Chimwendo Banda komanso nduna ya za ulimi a Sam Dalitso Kawale.
Nsonkhanowu wabweletsanso pamodzi anthu odziwika ena monga nduna yoona zakusasiyana pakati pa amayi ndi abambo a Jean Sendeza ndi wachiwiri wake a Halima Daudi, nduna ya za malo a Deus Gumba, Mkulu wa achinyamata Steven Baba Malondera komanso a Patrick Zebron Chilondora yemwe ndi Region Chair wachipanichi.