31/05/2024
Nyimbo yonse ija ndiyabwino, koma!
Kunjaku kwabuka nkhani. Mukudziwa inu paja kuti Big man Namadingo ndi Ofumu Tay Grin, ubale wawo ndiwabwino ndithu.
Koma zomwe ayankhula big man Namadingo kukanema ina yaku Zambia ndizo zikuoneka kuti zautsa mapiri pachigwa. Namadingo anafunsidwa, kuti paja nayeso amakhala ku Area 43, ndekuti aneba ake ndi azungu?
Pamenepo ndipo pabukira nkhaniyo, kamba kakuti Namadingo anati, sakufuna kuti zioneke ngati akufuna kunyozana ndi Tay Grin kapena kuti beef, komabe "nkhani ya aneba anga ndi azungu, ndalama zanga zachizungu", chakhala chinthu chakumtima kwakwe kwa kanthawi.
Iye anapitiliza kuti, nyimbo yonse ija (So Mone) ndiyabwino kwambiri koma idalakwa potamanda azungupo, ndikunyazitsa munthu wakuda. Kutanthauza kuti, kuti munthu wakuda achite bwino, neba wake ayenera kukhala mzungu.
Ofumu, Tay Grin sikuti ayankhapo kwenikweni pa nkhaniyi, koma patsamba lawo la Facebook apereka funso loti: kodi mumamvera nyimbo, kapena mumamvera koma mwacheka?
(by InnocentKumchedwa-Lilongwe:05/30/24)