27/04/2026
Pali ma application ena ndiopanda ntchito Kwenikweni amangozazitsa space mu phone
1. virus scanner ( ma phone ali kale ndi application imene imasakasaka ndi kupedza mavailusi mu phone )
2. Battery Saver ( ma phone ali kale ndi ma settings oti m***a kupangitsa kuti battery lisamangotsetsereka)
3. Wallpaper App
izizi izi ndi zoti mafoni amakhala nazo kale ndipo sikuti zimangozazitsa space mu phone komano zimaopsaso. zimakhala zokaikitsa.
mwachitsanzo akuba kunjaku kumayiko aanzathu amapanga application kenako amaipatsa dzina loti VIRUS-OUT kapena Virus Scanner kenako amaiyikira ma settings oti ikangolowa mu phone izitenga screenshot mwakachetechete panthawi imene munthu akulowetsa password iliyonse kaya ndi pin.
amapanga izi kuti akwanitse kumubera munthu amene akufunayo.
Kwa amene tili ndi ndalama mu phone , munthu kuti waziwa PIN kaya ndi password yathu sangachedwe kutitsatira kunyumba kapena kutitchingira pa msewu chifukwa azitha kutitsatira bwinobwino pogwiritsa ntchito foni yathu imene tikuyenda nayo. akubawa amangofuna kuti mu foni mwanumo mulowe system yawo kenako iwowo azikutsatirani.
ndiye chenjerani ndi ma application okhala ndi mayina omveka ngati ndi othandidzadi komano asali motero.
kulinso ma application oti munthu azisinthasintha ma wallpaper... zimamveka zabwino komano mmmm pamafunika kuchenjerabe