Nkhani Za A Malawi Ku Joni

  • Home
  • Nkhani Za A Malawi Ku Joni

Nkhani Za A Malawi Ku Joni Join our page by clicking the like button!. This page is here to Inform, Educate, Entertain & Unite different pple from different countries together.

Let's keep it rocking 🔥 Nkhani zosiyanasiyana zochitika ku madera osiyanasiya ku Joni muzimvera pano!!.. Invite ur friends to LIKE our page by posting this without the plus (+) sign @+[236219766530164:0]

17/08/2025

Mwadzuka bwanji
Lero sitinena Rate chifukwa akamva akumaigwetsa ndi 50kwacha titagula kale value.

Sitinganene kuti

R1 = MK260.00

01/08/2025

Mwadzuka bwanji

Amai ndi abambo komanso achinyamata. Ino ndi nthawi ya kampeni ku Malawi.

Atsogoleri a zipani zosiyana siyana ali kalikiliki, pembela pembela ku mamidzi, ntown ndi mma social media kuzigulitsa kuti apeze voti.

Onse amatumbwa ali pa udindo aja ali kangalikangali kunyengelera voti yanu ena ndi Maheu, ena ndalama, ena ti ma bonanza, ena chimanga, ena akuyenda ku makomo aanthu osauka, wolumala. Onsewo akufuna voti yanu inuyo.

Pa 16 September iwowo akadzawina basi chikondi kwa inu chathela pompo. Kwa omwe mukukonzekela kavoti yesetsani kukavotela anthu omwe ali ndi mfundo zotukula Malawi.

Taonani pano mafuta akusowa, forex ikusowa, zinthu zikukwera mtengo tsiku ndi tsiku.

26/07/2025

A katswiri pa nkhani za ndale ku Malawi akapereka zikalata zopempha boma kuti liuze boma la South Africa kuti ligwire amalawi onse m'dziko la South Africa kuti abwelere kuno kumudzi adzavote.

Namandwayu wati a Malawi akufunika kuti asamathawe kuvota. Ndi voti yokha yomwe ingasinthe zinthu. Popitiliza ati mzokhumudwitsa poona anthu akumachita kugonela Immigration kufuna passport cholinga athawe asavote.

23/07/2025

Mwadzuka bwanji
Lero sitinena Rate chifukwa akamva akumaigwetsa ndi 50kwacha titagula kale value.

Bola musauze ena kuti ili pa

R1 = MK260.00

22/07/2025

Mwadzuka bwanji

Kodi mumadziwa kuti mau oti MULUNGU satanthauza kuti God monga momwe ife timanthauzilamu.

Omwe muli ku Joni mukudziwa kale musayankhile nawo.

16/07/2025

Mwadzuka bwanji

Lero Rate yakwera

R1 = MK250.00
R4,000 = 1 Million kwacha

Mukhoza kugula Malawi yonse nokha

05/07/2025

Amwene tandibiseni, ine yo ndikufuna mundithandize nzeru. Ndine wopemphera wa katolika.

Monga munthu wopemphela timauzidwa kuti tizikhala mchiyero komanso wangwiro. Akati wangwiro kutanthauza kuti tizichita zonse m***a mtima wosabisa kanthu.

Ndiye ineyo ndikuzunguzika mutu. Ndili ku Joni kuno pamalo pomwe ndimakhala tidayandikana ndi a Malawi azathu. Mwamuna amagwira ntchito ku town pomwe mkazi amagwira kwa mzungu dera lomwe lino.

Anthu wa akhala akukangana kuti mwamuna yu amachita uhule kunja. Alimbana mpaka mkazi adangotopa nkusiya wosalimbana naye so mwamuna wake yo. Mkati mwakusiyaku mkaziyu zazidziwika kuti naye so akumagonana ndi mnyamata wogwira naye ntchito pa lunch pena poweruka amazapangana kunyumba kwaoku.

Izizi sikuti zonamizilanso koma zoti ma umboni aliko koma mwamuna yo sazidziwa.

Ndiye ine monga wopemphela posafuna kukhala wodetsedwa ku mpingo ndimafuna ndi muuze mwamuna yo. Kodi abale kuchita choncho ndilakwitsa. Ganizoli amuna anga sidawauze. Ndikufuna ndimve kunoko.

04/07/2025

Ndidali nditangokhala pakhonde. Panthawiyi ndimaothera dzuwa pakuti stove yomwe ndimaotha mnyumba njodalira kachaso(Ethanol). Kachasoyo watha wofunika ndikagule wina.

Ndatuluka nkukhala pa mpando panja. Ndaika tebulo nkuikapo zakudya. Ndidayamba kudya. Khale khale ndangomva mu ndiwo mo tchabwaa!.. Kuyang'ana kuona zoyera mbeee, ndakweza mutu mmwamba kuona mbalame ili pa TV aerial. Apa ndidangodziwa mbalameyi yazachitila dala, kuchoka uko basi kubwera zangonyera mu ndiwo zanga basi.

Ndisaname ndiwozi mwana wa a landlord adazikazingila bwino kwambiri. Ndabalalika. Ndizomwezi kulibe so zina. Nsima ndangoiyamba kumene.

Kodi pamenepa nditani ndizitaye ndiwo zi kapena ndingodiyabe.

27/06/2025

Musanditchule dzina,
Ineyo ndine mtsikana ndangobwera kumene ku South Africa kuno mwamuna yemwe dadziwana naye kudzela mwa achibale atandiitanitsa.

Kufika ndidafika bwino, adandilandilanso bwino. Koma pali mavuto angapo omwe ndakumana nawo.

Mwamuna yu ndi mlomwe ine ndi mngoni. Ndiye tsiku lina ntagwira foni yake dapeza ma message akulumikizana ndi achibale ake kumudzi za mkazi amene Ali wa kwao afuna amukwatire. Ndi mmene ndazionelamo anthuwo adayamba kuyendetsa dongosolo yo ka nthawi ine sadafike. Izi sidamuuze kuti ndaziona. Ndimangoyang'ana koma omwe adachititsa kuti ndibwere plus kulola munthuyu dawauza.

Vuto lachiwiri ndilakuti mwamuna yu ndikagonana naye ndikumapezeka kuti ine ndikumatsegula mmimba pena kumangomva kupweteka mmimba kukanika kugona.

Zinazo ndilibe nazo ntchito ndizasamuka kupeza malo anga. Komano ndabwera pano kuti mundithandize zimene zimandichitikilazo vuto ndi chani, nanga ndingapeze mankhwala anji kuti ndichile.

26/06/2025

Mwadzuka bwanji
Lero sitinena Rate chifukwa akamva akumaigwetsa ndi 50kwacha titagula kale value

23/06/2025

Mwadzuka bwanji
Lero Rate ili motere kuno
R1 = MK195.00

Mmalo mwa kota million kwacha pa R1000 zinthu zasintha ndithu.
Koma sikuti mitengo itsika ku Malawi ai.

23/06/2025

Mtsikana wa zaka 20 mnyamata wa zaka 20 awawa si ma agemates tikumvana koma

Address


Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Nkhani Za A Malawi Ku Joni posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

  • Address
  • Alerts
  • Claim ownership or report listing
  • Want your business to be the top-listed Media Company?

Share