
23/12/2024
Mtsogoleri wakale wa chipani cha UTM Michael Usi, ali pachiopsezo choti atha kuchotsedwa mchipanichi pomwe wayitanidwa kukawonekere ku komiti yosungitsa mwambo.
Malingana ndi kalata yomwe tsamba lino lawona, chipani cha UTM chati a Usi akuganizilidwa kuti adachita zinthu ziwiri zomwe ndizotsutsana ndi malamulo oyendetsera chipanichi.
UTM yati Usi akuganizilidwa kuti adayankhula mau omwe ali ndikuthekera kobweletsa mpungwepungwe m’chipanichi, komaso kuti akhala akutenga mbali m’zochitika za chipani china chomwe sichili pa mgwilizano ndi chipani cha UTM.
Chipanichi chakhazikitsa pa 30 December, 2024 ngati tsiku lomwe chikumane ndi a Usi kuti akafotokoze mbali yawo ndipo chatsindika kuti, “kusapezeka kwanu kutanthauza kuti mulibe chotsutsa ndipo komiti idzapeleka chigamulo popanda kufusaso.”
Izi zikubwera pomwe kumayambiliro a mwezi uno, a Usi anauza anthu m’boma la Mwanza kuti “boma ndi lomweli.”