18/08/2026
"MUNDISAMALIRE PICTURE-YO" 💔
___________________________________
PART 9
Written by Fukiz mw
_____________________
Izi zinayamba kundipatsa mantha kufikila tsiku la 5 lomwe ndimamva kupweteka ndikamakodza. Mikodzo ikandipola ndimachita kudela nkhawa kuti ndikakodzenso. Maganizo amandipeza kuti ndiwauze Agogo anga koma pena ndimazibweza . Izi zinandipangitsa kucheza masiku ochepa kenako ndinaganiza zobwerera ku Blantyre .
Ndinauyamba ulendo obwera kunyumba . Ndili bus ndinayamba kulingalira . " Ndakhala ndilipachibwazi ndi Sosten kwadzaka 8 . Kuchoka form 1 mpaka kukafika ku university koma sanandipatse matenda aliwonse . Uyu ndadziwananaye kumene miyezi itatu sinathe koma wandipatsakale matenda , tidziti palitsogolo apa?" Ndinapumila m'mwamba uku ndikuomba m'manja modzidandaulira . Kenako ndinayamba kudzifusa ndekhandekha .
"Laika ndye utanino pamenepa?"
Ndinatero ndikungolumaluma chalachanga . Kenako ndinati .
"Laika ukuyenera kuzemba ukwati umenewu."
Bus inayenda kufikila ndinakafika ku Blantyre chama 3 koloko masana . Nditafika pa gate yakwathu , ndinagogoda ndipo Achisale ananditsekulira . Atatsekula gate ndinaona Mamie ndi dad akuvina kusonyeza kuti alimchisangalalaro. Atandiona anandithanangira ndikuzandikumbatira. Kenako anandigwira mkono uku akuvinabe . Titalowa mnyumba anandionetsa malowolo omwe Uncle a Fukiz anabwera kuzasiya. Atatha kundionetsa amayi anayankhula alindichimwemwe ndipo anati:
"Sizokhazitu ayi, galimoto ya Ng'ombe 6 yanyamukakale kukasiya Ng'ombe-zo kwawo kwa Bambo ako."
Ndinazikakamiza kumwetulira, kenako ndinawatsamzika kuti ndikupita ku chipinda changa ndikapume . Ndinatenga handbag yanga ndikupita kuchipinda kukakhala pa bed langa chete uku ndikulingalira zothana ndi nthenda ija, chifukwa imandichititsa mantha. Ndilimkati molingalira ndinaona chitseko cha chipinda changa chikutsekuka uku mkulu wanga akuyankhula .
"Lai, osandiyimbila phone kuti......."
Anadukiza mau atandiona kuti ndikupukuta misozi kuti asayione. Nthawi yomweyo anabwera pa bed langa paja ndikuzakhala pambali uku akundifusa .
"Chavuta ndichani Laika?"
Ndinangokhala chete sindinamuyankhe koma misozi imatuluka. Kenako anandifusanso.
"Mphwanga tatena , kapena misoziyi ndiyachisangalaro kuti Fukiz ali serious zokukwatira eti?"
Ndinagwedeza mutu kusonyeza kukana . Nthawi yomweyo anandifusanso .
"Nanga ndichani tanenatu."
Anatero akutenga mutuwanga kugoneka pantima pake. Kenako ndinati.
"Flora,(Ma Peace) ndavulala."
"Wavulala pati? Bus yomwe munakwera munachita ngozi?😳"
Anandifusa mafuso awiri uku akundiyang'ana modabwa. Ndye pokuti kubisa matenda kuja ndi mtendere , ndinayimilira ndikuvula zovala zanga ndikumuonetsa. Atandiona zinamuopsa of course koma anapanga ngati munthu wamkulu kuti asandiopseze . Kenako anati:
"Siiwe oyamba dear , koma unamufotokozera doctor wa adad uja?"
"Ayi sindinamuyimbire chifukwa sindikufuna adad ndi Mamie adziwe."
"Usandiuze kuti ndi fukiz-tu"
"Ndyemweyo"
Anapumilamwamba kenako anati :
"Basi siyani kulirako, pukutani misoziyi tidzipita kuchipatala."
Tonse tinayimilira ndikuzikomzabwinobwino ndikutuluka kukatenga galimoto wakuchipatala. Titafika ndikumufotokozera Namwino , anandipatsa mankhwala okumwa komanso anasakaniza mankhwala ake muchijekison chachikulu chomwe anandibaya (Jenta). Ndinayamba ndakhalakaye pansi kufikila ululu utachepa. Kenako tinakwera galimoto kumabwerera kunyumba uku ndikumuuza Flora kuti :
"Ukwati uwu ndiuzemba"
Ngakhale ndinayankhula izi Flora sanandiyankhe amangoyendetsa galimoto. Sindikudziwa kuti m'mutu mwake mumkayenda chani panthawi imeneyi.
---
Masiku anapanga sabata ndipo masabata anapanga miyezi itatu. Pa miyezi itatu imeneyi, ubwezi wa ine ndi Fukiz unalibwinobe chifukwa ine ndimafuna nditathetsa ubweziwu kamba kokuti amandikana kuti sanandipatsire chizonono koma makolo anga amamuyikila kumbuyo Fukiz ngati ndimwana wawo weniweni kusiya ine . Zokamba zaine samamva koma amakhulupulira za Fukiz basi . Pa miyezi itatu yomweyo ndinali nditamisa period yanga zomwe zimatanthauza kuti ndiine oyembekezera. Thupi langa linayamba kufooka chifukwa chakudwaladwala. Week ino ndinatsekula m'mimba , week yamawa chimakhala chifuwa. Ndikachoka pa chifukwa ma rashes thupi langa lonse. Ngakhale izi zimandichitikila , makolo anga diso lawo amayang'ana zaukwati wanga basi omwe umafuna kuchitika mwezi otsatilawo. Ndye pokuti masiku anayandikila , analumikizana ndi designer waku South Africa kuti atipangire zovala ine ndi Fukiz zokuti tizavale pa ukwati . Kotero tsiku limenero tinanyamuka kuwapelekeza mamie ndi a Dad ku Bakili Muluzi international airport (Chileka) kuti azikapita kukakumana ndi Designer.
Titafika ku Airport tinatsika galimoto ndikuwapelekeza makolo athu mkati kuti akadinditse passport. Kumeneko tinapeza mzere ndithu wa Amwenye , amzungu ndi anthu okudafe. Titalowa mkati muja ndinaona Ma Peace akundikodola pa phewa.
"Lai, Laika wamuona Sosten?"
Anayankhula motsitsa mau. Ndinamwazamwaza maso koma sindimamuona. Kenako nanenso ndinamufusa motsitsa mau.
"Alikutiko?"
"Uyo mkatimo."
Nditaponya maso ndinamuona Sosten alibusy kudinda ma passport uku atavala Uniform ya immigration . Ntima wanga unagunda mwakamodzi ndikamodzi uku ndikudzifusa. "Zakhala bwanji Sosten kuyamba ntchito kuno? Ma connection amenewo wamupatsa ndani popeza kwawo ngati kuli ophunzira ndiyeyo?" Ndye pokuti Flora anabadwa mojijilikilako pang'ono kusiyana ndiine , ananyamuka kukakhala pamzeke ngati akukadinditsa passport uku atamutenga mwana wanga. Atafika iye anati:
"Mlamu, Clara akufuna Ice cream 🍦 "
Sosten anawayangana akumwetulira kenako anati:
"Ice cream apezeka koma andidikile pang'ono panjapo pokuti lunch time yafikakale."
Pomwe Sosten anayankha izi , Mamie anamuyitana Flora. Flora atapita , Mamie anati:
"Ma Peace, muzizipatsa ulemu , mlamu wanu monga simukumudziwa?"
"Ine ndi Sosten chilamu sichidzatha chifukwa tilindimagazi ake awa."
Anatero akumuloza Clara. Kenako amayi anayankhula mokwiya .
"Basi mwatipelekeza dzipitani kunyumba pompano."
Anatero akupita kukakwera Ndege. Ifenso tinanyamuka kupita pomwe tinayimitsa galimoto . Titafika ine ndinakwera galimoto koma Flora sanakwere analipanja ndi mwana wanga. Mosataya nthawi ndinaliza galimoto kuti mwina akamva kuti yalira abwera akwera , koma ndinadabwa akubwera pawindo ndikundifusa modabwa.
"Ukuliza galimoto ukupita kuti?"
"Kunyumba , bwanji?"
"Ayi dikilani mwana awonane ndi bambo ake."
Kenako ndinazimitsa galimoto ija ndikugejemula mpando ndikugona kumaseweretsa phone yanga. Lunch time itakwana ndinamuona Sosten akutuluka ndikubwera komwe kunali ife kuja . Anamunyamula Clara ndikubwera komwe kunali ine kuja uku phone yake akulira nyimbo ya Quaso(mbali yakuno the grass is greener). Anayenda kufika pa window kuzandipatsa moni wapamanja . Mwamanyazi ndinalandira chifukwa iye sanasunge mangawa kuti ndinamuthamangitsa kunyumba kwathu. Nditalandira moni wapadzanja uja, anabwerera kumakacheza ndi Flora uku akumulumphitsa mwana wake m'mwamba komanso kutoletsa ma photo. Mosatenga nthawi onse anayamba kudinadina pa phone kenako ndinamva akufusana ndi Flora.
"Yafika?"
"Eya yafika."
Pomwe amayankhula mau awa , ndinadziwa kuti akutumizilana ndalama. Zonse zitatheka , Flora ananyamuka kubwera komwe kunali galimoto kuja koma Clara akuwalilira bambo ake. Atakwera tinanyamuka kumabwerera kunyumba . Kenako anati:
"Mlamu wanditumizira K100 thousand akuti ya Ice cream. "
Sindinamuyankhe , ndimangoyendetsa galimoto zangaphe. Ndye chifukwa chokuti amangokamba nkhani ekhaekha koma ine sindimamuyankha , anadabwanazo ndipo anandifusa.
"Laika , phee ameneyu ukuganiza zichani?
Ndinapumila m'mwamba Kenako ndinati:
"Ukwati wangawu, ndiuzemba."
"Laika , aka ndikachiwiri ukundiuza kuti ukwati umenewu uwuzemba. Ukutanthauza chani ndipo uwuzemba motani?"
"Inenso sindikudziwayi koma ndiuzemba."
"Ukufuna uthawire kunja ? Ndye uthawira dziko lake litiro?"
"Sindikudziwa Darling."
Kenako tinayenda mpaka kukafika kunyumba komwe ndinapeza Fukiz wafika. Ndinapita pampando omwe anakhalawo ndikumakacheza uku tikukambirana nkhani za mimba yomwe ndinalinayo . Kenako Ma Peace pomwe amadutsa anayima ndipo anati:
"Komatu muziuzananso tsiku linayamba scale osamangokhala. Amakukalipiratu ukayamba scale mochedwa wekha ukudziwanso Laika."
"Eya ndikudziwa ndikayamba scale week yamawa. "
Tinacheza ndi Fukiz kufikila anatsamzika kumapita.
----
Week imodzi inadutsa . Ndipo week imeneyo, kunsana kwanga kunatuluka matuza ang'ono ang'ono koma ootcha ndiopweteka kwambiri . Ndye pokuti linali tsiku lomwe ndimafuna kukayamba scale , ndinaganiza kuti komko ndikamuonetse Doctor . Nditafika kuchipatala , ndinamufotokozera Namwino ndipo iye anandiuza kuti zomwe zanditulukazo ndimashingozi. Kenako anandipatsa mankhwala opaka komanso okumwa.
Nditatuluka kumeneko ndinapita kukapanga za Scale , koma Namwino wakumeneko anati sindingayambe scale ndisanayezetse . Izi zinandikakamiza kupita room yomwe amayezera magazi, ndipo atandiyeza, anandipeza kuti ndili ndikachirombo kuyambitsa AIDS.............
Tikumanenso mu part 10.
Ma Truck driver omwe akukambidwa munkhaniyi , ndi akumayiko akunja osati kwathu kuno kumalawi . Izi zilichonchi chifukwa ma truck driver akwathu kuno ndiodziletsa kwambiri komanso sapanganawo kusaweluzikaku . Inu amene muli ma Truck driver komanso azikazi ama truck driver, nkhaniyi musayitengere ayi ndimacheza chabe komanso ndinkhani zongopeka chabe izi. 🤸🤸
Ikupitilira.........
FUKIZ MW
Subscribe to get exclusive benefits:
https://www.facebook.com/100087613834930/subscribenow