23/06/2026
Hello upendo muli bwanji Ndipagileko post
Ndine mzimayi ndili kuno ku Pretoria ndikufuna anthu ako andidzudzule ngati ndalakwa ineyo ndili pa banja ndi ana awiri amayi angaso ali kuno amankhala onkha nde tinakambirana kuti tiyitanitseko mwana wa abale awo omwe ali anayi anga akulu cholinga aziwanthandizako amayi akewo ku mudzi . zinathekadi tinapangira passport anabwera kuno panopa wangontha miyezi itatu chibwelere.
Ndinamuuza tiponye mapepara kuti apeze ntchito ineso nali sakugwira masiku ena ndipo zinatheka ntchito tonse tinayipeza iyeso akugwira masiku 4 panopa
Poyamba namuuza upagitse card ya mukulu uwadikile amayi akapeza mpata akupelekeze after 2 days anabwera nalo card akuti nyamata wina anandipelekeza kopagitsa zatheka ife kudabwa mzako.wadziwira kuti ati ndimagwira naye koyandikana ine nangoti oky amayiso anangoti oky .
Tsiku lina amayi anandiuza chonde umuyankhuleko ngono wako mwano kwambiri kamuyankhula zinthu sakundivera ayi ndinapita kufunsa vuto ndi chani iweyo anandiyankha kuti andiwuze omwe andibweletsera unthengawo. Ineso kukamwa kakasi munthu sakufotonza nangoti ngati ukuona kuti pa nyumba pano sukusagalala untha kusaka nyumba uzinkhala poti ugwira ntchito.
Ndeno last week Saturday anadya nsima ndi amayi onse awiri za bwino bwino zinja anacheza onse mkumagona usiku ma 11 pm amayi adzizimuke mzawo pa bed 🛌 palibe anangoti iiiii mwina wapita ku toilet 🚻 eeee mpakana 30 minus inatha munthu osabwera kupita ku toilet kulibeko kuyangana 4n yake ili pa charge anadzutsa ma neba onse akuti ayi sitinamuone chodabwitsa room yawo inali yotsegura koma pa bagala yotulukira yotseka . Anandimbira 4n ine ndati ayi sanafike anagona mmawa kunacha ma 6 am analandira new number akuti amayi musadandaule ine ndilipo ndikupezani ma 10 mmawa uno
Amayi anandiuza zomwe wawuza kenako ine ndinapita atabwera kufunsa unali kuti akuti kwa mzaga zako wa kuti opita usiku komaso osatsanzika ati sindidziwako dzina la malowo tiye ukati onetseko akuti sindingalondole nde ndinangoti nde pakila uzipita komweko unali munthu ananyamura zovala zake mkumapitadi or kupepesa ayi ndinawuza amayi ake mene zankhalira nde akulalata kunditukwana akuti mwana wawo ndimamuda ineyo sindifunira za bwino koma chosecho namuyitanitsa ndine abale kodi kulakwa kwanga kuli pati ?apa mukati muone inuyo
゚viralシfypシ゚viralシalシ