02/10/2026
OPPOSITION IKUGONA KWAMBILI - MBEWE
M'modzi mwa akatswiri olankhulapo pa nkhani zosiyanasiyana m'dziko muno a Joshua Mbewe apempha opposition kuti ichangamuke.
M'modzi mwa anthu womwe amalankhulapo pa nkhani zosiyanasiyana zochitika m'dziko muno koma zokhudza a Malawi a Joshua Mbewe adabwa ndi chete wa mkulu wotsogolela zipani zotsutsa boma m'dziko muno a Simplex Chithyola Banda.
Malingana ndi anthu osiyanasiyana m'dziko muno akufusa a Chithyola Banda kuti azilankhula ngati mkulu wotsutsa boma podzudzula zochitika zina ndi zina zomwe zikuoneka kuti sizikuenda bwino .
A Joshua Mbewe alemba kalata yawo potambasula mavuto womwe a Malawi akukumana nawo pakanali pano monga kusowa kwa mafuta a galimoto,mankhwala kusowa ku Chipatala,kusowa kwa ndalama za kunja,kukwela kwa katundu wina wofunika miyoyo ya a Malawi mwa zina.
Choncho a Mbewe apempha m'tsogoleli wa mbali yotsutsa boma m'dziko muno a Chithyola Banda kuti asakhale chete ayi , koma agwile ntchito yawo yoyankhulila a Malawi pa mavuto womwe akuta dziko lino maka pasakuyenda bwino kwa zinthu zina ndi zina.
A Mbewe awonjezela mavuto ena ngati mavuto a ku Blantyre Water Board BWB,kusowekela kwa mwayi wa loan kwa ophunzila ena kuti achite maphunziro awo ku sukulu ya ukachenjede za boma, komanso chipwilitiki pa nkhani ya Constituency Development Fund CDF komanso nkhani zikulu zikulu zokhudzana ndi a Malawi.
A Simplex Chithyola Banda pa ichi apemphedwa kuti azilumikizana ndi a Malawi popangitsa misonkhano ya Atolankhani pafupifupi kuti azitha kutambasula nkhani zomwe zikupsinja anthu m'dziko muno.
Komanso a Joshua Mbewe apempha eni ake a Malawi nao kuti asakhale chete koma kuwunikila ngati ofesi ya leader of Opposition ikukwanitsa ntchito yake kapena ai.
Mu chithuzimo a Simplex Chithyola Banda womwe apemphedwa kuti azilankhulila a Malawi ngati Leader of Opposition.
Anamandwa TV