05/12/2025
mwakathithi pa page pano zikachitika mumvela Ku
Mabanja oposa 300 akusowa pokhala pomwe anthu ena avulala nyumba zitawagwera kutsatira mvula ya mphamvu ndi ya mphepo yomwe yagwa mmadera ozugurila tauni ya Liwonde m'boma la Machinga.
Izi ndi malinga ndi phungu wakunyumba ya Malamulo kudera la Likwenu ku m'bomali a Tulinje Muluzi ndipo iwo apempha boma komanso mabungwe ndi ena akufuna kwabwino kuti athandize mabanja okhudzidwawa ndi chakudya komanso zina zowayenereza mu nyengoyi
Polankhula pomwe amayendera anthuwa, a Muluzi ati alephera kukakhala nawo ku zokambirana zakunyumba ya malamulo dzulo kaamba kokhudzidwa ndi ngoziyi yomwe yaononga zinthu zambiri.
Mvulayi yagwetsa nyumba zochuluka, kusasula midadada ya sukulu komanso kugwetsa ma polo amagetsi a madera omwe azungurila tauni ya Liwonde monga Kaudzu, Chabwera komanso Saiti omwe ali pansi pa mfumu yaikulu Sitola m'boma la Machinga.
Pakadali pano, mkulu wa zamaphunziro m'bomali a Douglas Namikungulu ati masiku akubwerawa, maphunziro akhala ovuta kukwaniritsa m'bomali maka msukulu zomwe zakhudzidwa pamene nvula ikupitirilabe.
📝NEWS UPDATE