29/04/2026
*CHEMWALI PA DEEN AKUFUNA KUDZIWA NGATI PALI DUA YOCHITA AFTER ZINAA, SO THAT UKHULULUKIDWA MKUKHALA NGATI SIUNACHITE ZINAA.* POTENGERA IWO, MU EXPERIENCE YAWO AKUONA KUTI MA SHAYKH AMBIRI SALIOPA TCHIMO LA ZINAA.
*FUNSO*
Kodi pali Dua yomwe akanganya amenewa amadalira? Chonde tiphunzitseni Dua imeneyo.
*YANKHO*
*@* May Allah have mercy! Palibe Dua direct yomwe inakhanzikitsidwa kuti yonena After Zinaa ndikuti munthu akainena adzayeletsedwa ngati sanachite Zinaa, ndipo kulibe zoterozi kumachimo ena posakhala Zinaa whether mu Qur'an or mu Sunnah.
*@* Kuyankhula komati ma Shaykh mngokonda akazi ndikofalikira pakati pa asilamu ndi omwe sali asilamu, izi chifukwa choti Allah analoledza msilamu kukhala ndi nkazi woposa m'modzi pa Qur'an 3:4 ndipo ma Shaykh amachita Practice chilolezo chimenecho kuposa aliyense plus ma shaykh amalimbikitsa kutsatira chilolezochi monga amalimbikitsira Ibaadah Ina.
*@* Zoona zake mzoti palibe mwamuna yemwe amasangalatsidwa ndikukhutitsidwa ndi nkazi m'modzi yekha, ndipo Allah anatsimikizira mu Qur'an kuti awachita amuna kukhala wokonda akazi pa Qur'an 3:14, choncho amuna onse ndiwokonda akazi pachibadwidwe.
*@* Ma shaykh ndi amuna ena omwe amatengera mwai pachilolezochi mmalo mokwatira akazi oposa mmodzi mkumangopanga Zinaa ndikuluza kwawo kwakukulu. Amayenera kugwiritsa mchito chilolezochi kuti afune fune chiyanjo cha Allah. Indee ena mpaka amayankhula kuti mowa wama Shaykh nde zinaaa. Anthu ena ali ndi experience kuti ma shaykh ambiri mngofooka ku tchimo la zinaaa, koti mpaka ena anati kamba koti ma shaykh samamwa mowa, juga, chamba, kuba ndi machimo ena akulu akulu, akuti Zinaa imawaphwekera mwina kaamba koti Zinaa imachitika mdima utakuta Dunia" Wallahul musta'anu nde anasankha Zinaa yoti siimaonekera. *Izi sizili kwama shaykh onse, ndipo 90% yama Shaykh ndiwolungama pomwe 10 or 5% nde omwe samaipeza mitima mpaka akudetsa mbiri zabwino zama shaykh abwino.*
*KODI PALI DUA PAMBUYO PA ZINAA?*
Ayi palibe. Koma Pali njira zotsatidwa kuti munthu akhululukidwe ndikuti asanduke woyera ngati sanachite tchimo la Zinaa or machomo ena ndipo palibe chilango chomwe angalandire akatsatira njirazi.
*IMENEYO NDE TAWBAH*
Machimo anabwelera anthu, ndipo palibe yemwe angatetezeke kumachimo, yemwe wachimwa akumbukire kuthawira kwa Allah mwachangu, kupempha chikhululuko nthawi zonse ndikulapa nthawi zonse.
1. *Musataye mtima poti mwachita Zinaa or tchimo lililonse* pa Qur'an 39:53 Allah akuwaitanira akapolo ake omwe achita Zinaa ndimachimo ena ku chikhululuko Iye mu tanthauzo la Aya akuti: "Tawauze kuti; Oh inu akapolo anga omwe mwazichitira zoipa! {machomo} Musataye mtima zachisoni cha Allah, Ndithu Allah mngokhululuka machimo onse {tchimo lalikulu or laling'ono}; ndipo Iye mngochulukitsa kukhululuka ndiwachisoni.
2. *Kulapa kwanu kukhale koona mtima kusakhale pa lilime pokha, ndipo muzitalikire zomwe zinakugwetserani mu tchimolo. Plus muchilimike pochita Ibaadah, poti ntchito zabwino zimafafaniza machimo.*
3. *Ngati mwalapa kwa Allah m***a mtima si inu wa chiwere werenso. Choncho mulinso ndi mwai wokwatiwa ndi Mwamuna wolungama/nkazi wolungama osati wa Zinaa.*
4. *Munthu wokhulupilira akuyenera kukhala ndi chiyembekedzo chabwino pazabwino zochokera kwa Allah. Ndipo osapempha chitetezo cha Jahannam chokha ayi, koma kupemphanso Jannah chifukwa chakulapa kwake.*
Ladies and Gentlemen! Palinso moyo wokoma pambuyo pa machimo ndipo siinati kukwanira Tawbah ya munthu yemwe walapa koma sanati kusiya tchimolo.
*SHAYKH! INE NDINALAPA KOMA NDACHITANSO TCHIMOLO! ULAPENSO , ULAPENSO , ULAPENSO MPAKA ALLAH AKUPATSE CHITETEZO KUTCHIMOLO, IMENEYO NDE DEEN YANU. SIIMAMUTAYA AMENE WACHIMWA KOMA IMAMUITANA NDIKUMPATSA CHITONTHOZO.*
_Allah atimvere chisoni_