24/09/2026
Zotsatira za kuchipatala zapeza kuti mayi Tathokoza Salimu yemwe anali ogwira ntchito ku Bank ya FDH mu msasa wa Dzaleka anamwalira kaamba koomberedwa ndi mfuti pakhosi.
Mneneri wa polisi ya Dowa a Alice Sitima awuza Times 360 Malawi za nkhaniyi ponena kuti lipoti la chipatala lawonetsa kuti malemuyo anawomberedwa
Malemu Salimu anapezeka atafa lolemba mu galimoto yawo pafupi ndi mlatho wa Tatolonga mu msewu wochoka ku Dzaleka kupita ku Dowa Boma.
Malemu mayi Tathokoza Salimu amachokera mmudzi wa muliya mfumu yaikulu Mkanda m'boma la Mulanje.
Wolemba Mphatso M'bang'ombe