01/08/2025
Grace Fan TV
Bwalo la Bingu ku Lilongwe, limene limatenga anthu 41,000, liri pa mndandanda wa ma bwalo opyola 50, amene bungwe la Confederation of African Football-CAF, lawavomereza kuchititsa masewero a mipikisano ya World Cup, Africa Cup of Nations, Champions League ndi Confederations Cup.
Izi zikutanthauza kuti timu ya Flames idzasewerera pa bwaloli masewero ake a mpikisano wa World Cup ndi Liberia mwezi wa September komanso ma timu a Silver Strikers ndi Mighty Wanderers adzagwiritsa ntchito bwaloli ngati pa khomo mmipikisano ya CAF.
Kukhala momasuka kwa anthu owonera, chitetezo chokhwima, magetsi, madzi komanso posewerera pabwino ndi zina mwa zimene bungwe la CAF limayang'ana kwambiri lisanavomereze ma bwalo
Koma maiko a Namibia, Guinea, Central African Republic, Djibouti, Sao Tome and Principe, Lesotho, Somalia, Sierra Leone ndi Seychelles achita tsoka kuti ma timu awo adzichita kubwereka ma bwalo mmaiko ena kamba koti bungwe la CAF silinavomereze ma bwalo awo.
Ma timu a Namibia ndi Sao Tome and Principe, amene ali mu gulu limodzi ndi timu ya Malawi, mu mpikisano wa World Cup, adzasankha ma bwalo oti adzasewerere ndi timu ya Flames.