21/04/2026
💔Zochitika kwathu kwa Chafelamthengo 🙌
Awa ndi malo owetele ma virus ndima bacteria. Eya Champs uku uku ndi ku Dowa, pama office a MTL ndi MPC.
Malowa akuti ali kuseli kwa nsika ndipo ma Health Champs kumeneko akudandaula ndi chifungo choipa chomwe chikumatuluka pamalowa.
Komatu akuti nkhani yake ndi yovuta chifukwa kuchotsa zinyalalazi kukufunika makobidi okwana 4.5 million kwacha. Vuto ndi loti Boma nalo lili mmaluzi.
PS
Nkhawa zama Champs ku bawo zoti matenda amayenda mu mpweya. Ndiye apapa zitha bwanji? Kapena tichite limodzi limodzi poti boma lachepekedwa🥱
📷Zodiac Online