Patricia 2 Frakeza

Patricia 2  Frakeza Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from Patricia 2 Frakeza, Digital creator, 5 buzzard Road Pelican park, Pelican Park.
(8)

Story teller
Entertainer
Comedian

Pano pamakhala nkhani zophunzitsa, zolangiza komanso zodziwitsa, kalikonse mukamva pano😋😋😋

I can do all things through christ who strengthens me🙏🙏🙏🙏

Mayi Woyamba -Episode 2Chipinda chochezera cha nyumbayi chinali chokongola kwambiri komanso chapamwamba. Pansi pake pana...
23/06/2026

Mayi Woyamba -Episode 2

Chipinda chochezera cha nyumbayi chinali chokongola kwambiri komanso chapamwamba. Pansi pake panali kapeti wofiira wokongola, ndipo makoma ake anali opakidwa utoto woyera wonyezimira. Makomawo anali oyera kwambiri moti Brian ankatha kuona chithunzi chake chikuwonekera pa iwo ngati galasi. Atangolowa m’chipindamo, anatenga mpweya wakuya ndipo mpweya wozizira wa makina oziziritsira mpweya unamupangitsa kumva bwino. Nyumba yonseyo inasonyeza chuma ndi mphamvu. Mayi Woyamba anasankha yekha nyumbayi, ndipo anthu ena sankaloledwa kulowamo. Inali nyumba yobisika yomwe inali m’dera lapamwamba la nyumba za m’likulu la boma.

Brian anaikonda kwambiri nyumba imeneyi, koma anadabwa kwambiri ndi zimene Mayi Woyambayu anamuuza atamulowetsa m’chipinda china cha nyumbayo.

“Brian , ndinakuitana kuno chifukwa ndakusowa kwa zaka zambiri. Chifukwa chimene ndinakusiyira nthawi imeneija n’chakuti sunali wokonzeka kukwatira ndipo sunali ndi ndalama zokwanira. Tsopano ndili ndi mphamvu ndi chuma, ndipo ndikufuna kuti tikhalenso pafupi ngati kale,” adatero Mayi Woyamba.

Brian anangokhala chete chifukwa anali wosokonezeka komanso wodabwa.

“Koma munandiuza kuti ndidzakhale mthandizi wanu wapadera. Munati ndidzagwira ntchito ku nyumba ya boma. Nanga bwanji mwandibweretsa kuno? Ntchito yomwe ndinabwera kudzagwira ili kuti?” anafunsa Brian.

“Brian usandikhumudwitse. Ndikufuna ukhale munthu amene ndingamudalire komanso kumamuyandikira nthawi zonse. Udzudzalandira ndalama zambiri, nyumba yabwino, galimoto komanso maubwino ena ambiri. Sindikufuna kuti udzavutike moyo wako wonse,” anayankha Mayi Woyamba.

“Musaiwale kuti ndine munthu wokwatira. Ndili ndi mkazi komanso mwana. Sindikufuna chilichonse chomwe chingabweretse mavuto m’banja langa kapena m’banja lanu,” adatero Brian.

Koma Mayi Woyamba sanasinthe maganizo ake.

“Sindikukupempha kuti usiye mkazi wako. Ndikungofuna kuti tizikhala pafupi. Mwamuna wanga amakhala wotanganidwa kwambiri ndi ntchito za boma ndipo nthawi zambiri samakhala ndi nthawi yokwanira. Ndikufuna munthu amene ndingamukhulupirire,” adatero.

Brian anamuyang’ana Mayi Woyambayu ndipo anaona kuti akadali wokongola monga momwe analili kale. Komabe, anadziwa kuti zimene ankafunazo zikanabweretsa mavuto ambiri.

“Ayi. Sindingachite zimenezo. Chonde, ndiwonetseni ntchito yeniyeni yomwe munandiyitanira. Sindinabwere kudzachita zimene mukunenazi,” adatero Brian.

Mayi Woyamba anaoneka kukwiya.

“Ndakuuza kale ntchito yomwe ndikufuna uzigwira. Ngati sukufuna kugwira , basi ndifufuza munthu wina amene angandithandize.”

“Ngati ndi choncho, ndiye pangani momwe mwaonera. Sindingachite zinthu zosagwirizana ndi zomwe ndimakhulupirira. Ndine wokwatira ndipo ndikufuna kukhala wokhulupirika ku banja langa,” anayankha .

Atayankhula zimenezo, anatuluka m’nyumbamo ndikubwerera kunyumba kwake. Mayi Woyamba anakhumudwa kwambiri ndipo anachoka pamalopo ali wokwiya.

Brian atafika kunyumba kuja , anauza mkazi wake zomwe zinachitika.

“Mayi Woyamba akunena kuti andichotsa ntchito,” adatero.

“Chani? Koma tangofika kumene! Nchifukwa chani akufuna kukuchotsa?” anafunsa Amina modabwa.

“Sindinakonde zimene akufuna kuti ndizichita.Ndi zosiyana kwambiri ndi ntchito yomwe anandilonjeza poyamba ija,” anayankha Brian.

“Koma Nchifukwa chani wakana? Ife takhala tikuvutika kwa nthawi yayitali. Kodi sungaganizireko za tsogolo la banja lathu? Ndalama zimenezi zitha kusintha moyo wathu. Mwana wathu athanso kubwerera kusukulu ndipo moyo wathu ungakhalenso wabwino,” adatero Amina mokwiya.

“Ndikumva zimene ukunena, koma sindingapange chilichonse chomwe chingawononge ulemu wanga kapena banja lathu,” anayankha Brian

Amina anakhala chete kwa kanthawi, koma ankawonekabe kuti sankakhutira ndi yankho la mwamuna wakelo.

Ikupitrira....

Kodi Brian apitirizabe kukana zomwe Mayi Woyamba akufuna? Kapena mavuto atsopano ayamba m’banja lakeli chifukwa cha chisankho chimene wapanga??

Like share and comment komanso follow Patricia 2 Frakeza

23/06/2026

Mkazi wanga anakanika kundiberekera mwana

Part 2

Salah zikuvutabetu nzipatala ndee akuyesetsa kuyenda mzathuyi kaya zimuthera bwanji ....komanao mwina vuto siiywyu Isaah 🙄🙄🙄🙄

Masana anu akuyenda bwanji mbali imeneyo??Part 2 ya mkazi wanga anakanika kundipatsa mwana Loading......
23/06/2026

Masana anu akuyenda bwanji mbali imeneyo??

Part 2 ya mkazi wanga anakanika kundipatsa mwana Loading......

Mayi Woyamba -Episode 1Brian  anali kunyumba madzulo amenewo akuwerenga nyuzipepala. Koma kwenikweni sanali kuwerenga nk...
23/06/2026

Mayi Woyamba -Episode 1

Brian anali kunyumba madzulo amenewo akuwerenga nyuzipepala. Koma kwenikweni sanali kuwerenga nkhani zake; amangoyang'ana masamba osiyanasiyana kuti aone ngati angapeze ntchito yogwirizana ndi maphunziro ake. Anali ali pa ulova kwa miyezi yoposa isanu ndi umodzi ndipo banja lake linali likuvutika kwambiri. Anafufuza nyuzipepala yonse kuyambira patsamba loyamba mpaka lomaliza, koma sanapeze ntchito iliyonse yoti alembere.

“Ndatopa kufunafuna ntchito. Mwina ndibwerere kumudzi ndikayambe ulimi. Kumeneko nditha kumakapeza chakudya chokwanira kusamalira banja langa. Tauniyi sikundiyanjanso ai ,” adadandaula Brian uku akuponya nyuzipepala patebulo.

Nthawi yomweyo, foni yake inalira. Anatenga ndikuyankha.

“Waswera bwanji, Brian . Kodi ukumudziwa amene akuyankhula? Ungakwanitse kuwakumbukirabe mawu anga?” mkazi amene anayimba foni uja anafunsa.

Brian anayesetsa kukumbukira koma sanathe kuzindikira mawuwo. Ngakhale kuti ankawaoneka ngati owadziwa, sanakumbukire mwiniwake.

“Pepani, sindikukumbukira. Chonde undikumbutse kuti ndiwe ndani,” anayankha mofatsa.

“Ndine Jessica, bwenzi lako lakale. Kuteroku wandiwala? N’chifukwa chani sukukumbukira mawu anga? Sizabwino zimenezo,” adatero Jessica mwachisangalalo ngakhale ankachita ngati wakwiya.

“Eya! Jessicah! Ndine wokondwa kumva mau ako . Sindinaganizirekonso kuti ungadzandiyimbirenso kuchokera pamene tinasiyana. Lero ndi tsiku lapadera kwa ine. Kuyimba kwako kuli ngati mvula yogwa pa nthawi ya chilala. Uli bwanji, Jessica? Ndikudziwa kuti zinthu zikukuyendera bwino chifukwa unandisiya ine n’kukwatiwa ndi munthu wolemera,” adatero Brian

“Sunayenera kundiimba mlandu. Umadziwa kuti ife akazi nthawi yathu imayenda mofulumira. nthawi imeneyija unali usanakonzeke kukwatira ndipo unalibe ndalama zosamalira banja. N’chifukwa chake ndinasankha munthu amene anali wokonzeka. Komabe, ndiwe amene ndinkankonda kwambiri, koma chikondi chokha sichingabweretse chakudya patebulo,” adatero Jessica moseka.

“Ndinakumvetsa. Kale ndinavomera zimene zinachitika zija ndipo ndinapitirira ndi moyo wanga. Tsopano ndine wokwatira pano ndipo ndili ndi mwana mmodzi. Moyo sukuphweka, komabe tikuyesetsa kuphusha,” anayankha Brian mwachisoni.

“Ndichifukwa chake ndakuyimbira. Choyamba, ndine wokondwa kumva kuti tsopano uli ndi banja lako. Ndikudziwa kuti ukusowa ndalama ndipo ndikudziwa mavuto amene ukukumana nawo. Ndikufuna ndikupatse ntchito. Mwamuna amene ndinakwatira nae uja tsopano wasankhidwa kukhala Bwanamkubwa(Gavanala) wa boma lathu, ndipo ine ndakhala Mayi Woyamba(first lady). Ndikufuna ubwere kuno udzidzagwira ntchito ngati mthandizi wanga wapadera. Udzalandira ndalama zambiri. Malipiro ake ndi K2 miliyoni pamwezi. Kuphatikiza apo, udzapatsidwa nyumba yaulere komanso galimoto yatsopano kwa iwe ndi banja lako. Ndikuthandizanso kupeza ma kontrakiti a ndalama zambiri. Ngati ungakonde, ndikutumizira ndalama za ndege kuti iwe ndi banja lako musamukire kuno ndikudzakhala m’bomali lino” adatero Jessica.

Mawu amenewo anamudabwitsa kwambiri Brian.

“Ndine wokondwa kumva kuti tsopano ndiwe Mayi Woyamba, mkazi wa Bwanamkubwa. Zikomo kwambiri ndipo ndathokoza kwambiri. Za ntchitoyi, ndilankhule kaye ndi mkazi wanga usiku uno kenako ndikudziwitsa mwamsanga,” adatero.

“Chabwino. Ndiyembekezera yankho lako, koma ndikufuna uyankhe mwachangu tisanafike mawa m'mawa. Ukapanda kundiyankha pofika m'mawa, ndidzadziwiratu kuti sukufuna ndipo ndidzapatsa munthu wina,” adatero Jessica asanadule foniyo.

Usiku womwewo, Brian anakambirana ndi mkazi wake, Amina, za mwayi wa ntchitowo.

“Kodi ukuona kuti ndiivomere ntchitoyi? Ndi ntchito yabwino kwambiri ndipo ndi mwayi kugwira ntchito ndi mkazi wa Bwanamkubwa. Malipiro akenso ndi abwino komanso pali maubwino ambiri. Koma ndikuda nkhawa. Ndikufuna ndikuuze zoona, sindikufuna chilichonse chomwe chingabweretse mavuto mmbanja lathu,” adatero Brian. Iwo anali atagona kale m’chipinda chawo.

“Kodi ukukayikira chani? Kodi sitinavutike mokwanira? Ukuyenera kuivomera ntchitoyi pompano. Kodi ukufuna kuti munthu wina atenge mwayi umenewu? Mawa m'mawa ndiyamba kulongedza katundu wathu kuti tidzipita kumeneko. Palibe chimene chingatilepheretse kupeza mwayi umenewu womwe ungasinthe moyo wathu,” anayankha Amina mosazengereza.

“Kodi ukutsimikiza zimene ukukambazi? Ukukumbukira kuti Mayi Woyamba ameneyu ndi bwenzi langa lakale. Ndimangowopa kuti zingabweretse mavuto patsogolo. Ndikuganiza kuti ndibwino iye apeze munthu wina,” adatero Brian.

“Ayi! Uyenera kuivomera basi ntchitoyi. Ngati sukufuna, ndiye kuti sukuganizira za banja lathu. Sindingapitirize kukhala mu umphawi moyo wonse. Ntchitoyi isintha moyo wathu. Mwana wathu sakupitanso kusukulu chifukwa chosowa ndalama za ku sukulu, ndipo zovala zathu zambiri nzokutha. Choncho usaganizurenso kawiri,” adatero Amina mwamphamvu.

“Chabwino, ndivomera. Koma ngati pangakhale mavuto mtsogolomu, musadzati sindinakuchenjezeni,” adatero Brian asanagone.

Tsiku lotsatira, Brian ndi banja lake anasamukira ku boma limene Jessica ankakhala. Atafika ku likulu la bomalo, anatengedwa kupita ku nyumba yatsopano yomwe Jessica anawagulira. Anapatsidwanso galimoto ndi zinthu zina zambiri zabwino zomwe zinawapangitsa kukhala osangalala komanso omasuka.

Atangokhazikika, Brian analandira foni kuchokera kwa Mayi Woyamba.

“Dalaivala wanga akubwera kudzakutenga,” adatero.

Posakhalitsa, galimoto inalowa pa nyumba yawo ndipo Brian anatengedwa kupita ku nyumba ina yapamwamba komwe kunali nyumba za anthua mmboma olemera kwambiri.

Atalowa m’chipinda chochezera, Jessica anayamba kulankhula naye.

“Iyi ndi nyumba yanga yobisika. Ndagula kuti tizikumanirana kuno tikafuna kukambirana zinthu zathu mwakachetechete. Ndakusowa kwambiri kuyambira kale lomwe. Mwamuna wanga amakhala wotanganidwa kwambiri ndi ndale moti samandipatsa nthawi yokwanira. Ndakhala ndikufuna kukhala pafupi nawe kachikenanso . Chonde, ndifuna kuti ubwererenso m'moyo mwanga, ndipo ndikulonjeza kuti sudzasowa chilichonse,” adatero Jessica

Brian anadabwa kwambiri ndi zimene anamvazi ndipo sanadziwe choti angayankhe.

Ikupitrira

Kodi Brian avomera zomwe Jessica akufuna? Kapena akhalabe wokhulupirika kwa mkazi wake ndi banja lake?

Amina mistake......azimai mwaiona Blandah ya Amina?????

Like share and comment osaiwala kupanga follow Patricia 2 Frakeza

23/06/2026

Zigumu tazipeza apa bola kkkkk

New story alert 💃  📢 👀 😍 "Mayi woyamba(the first lady)"Umu tione za mayi mzathu Amina amene anali nd mamuna wake Brian ....
22/06/2026

New story alert 💃 📢 👀 😍

"Mayi woyamba(the first lady)"

Umu tione za mayi mzathu Amina amene anali nd mamuna wake Brian ...koma Brian yu anali paulova wadzaoneni ..ndee mwadzidzidzi tsiku lina analandira foni kuchokera kwa bwenzi lake lakale Jessica amene anamuuza kuti waimba foniyo kamba kodzwa zoti amavutika ndeee akuyenera kupita kudera lomwe amakhala iyeyo poti amupatsa ntchto yabwno ..komanso nyumba nd galimoto ...koma Brian atamva nkhaniyi kumuuza mkazi wake mkaxiyu anakondwa kwambiri kuti umphawi watha ..koma mamunayu sanakondwe podzwa kuti uyuyu nd bwenzi lakale... madzi saaiwala nkhwawa amaopa kukachimwa ...komatu Amina ndeee anaumilira ali mgati suvomera ntchtoyi ndikusiyaaa....mamuna anazikakamizabe nkovomera koma anamuuziratu chobwera mmawa osadzandiimba Mlandu...ndee muone atakafika ukokwa Jessica ..Mai bwanankubwa mai Gavanala kunali zotani........

Tikuiyamba mmawa!!!! 💃💃💃💃💃

I hope smundisiya ndekha anthu abwino inu....mundibereka muja muchitiramu😋😋😋😋😋...

#

Mimba ya Amapasa Episode 20Ukwati wa Lindah ndi Michael  unatchuka kwambiri m’dziko lonse. Mawayilesi a pa radio, manyuz...
22/06/2026

Mimba ya Amapasa Episode 20

Ukwati wa Lindah ndi Michael unatchuka kwambiri m’dziko lonse. Mawayilesi a pa radio, manyuzipepala komanso ma TV ankangolankhula za ukwatiwo kwa sabata yonse. Tsiku la ukwatiwo linali ngati chikondwerero chachikulu chifukwa anthu ambiri otchuka ndi olemekezeka anapezekapo. Lindah anali mkazi wosangalala kwambiri padziko lonse lapansi pa tsikulo.

Lindah ankawoneka bwino kwambiri mu diresi lake laukwati ndipo Michael anali wokondwa kwambiri kuti anapeza mkazi ngati Lindah ndipo anamukakamiza kuti avomereze kukhala mkazi wake. Ukwatiwo unachitikira ku bwalo la boma ndipo sunatenge nthawi yaitali. Chofunika kwambiri chinali phwando la ukwati. Malo amene phwandolo linachitikira anali okongola kwambiri moti Lindah sanakhulupirire maso ake pamene iye ndi mwamuna wake anafika. Atakhala pansi, mwambo unayamba bwino kwambiri.

Panali kudya ndi kumwerera kochuluka, nyimbo komanso kuvina. Linali tsiku lachisangalalo chachikulu kwa Lindah ndi Michael.

“Pomaliza, tsopano ndife mwamuna ndi mkazi. Ndine wokondwa kwambiri kuti izi zakwaniritsidwa. Ndine mwamuna wosangalala kwambiri padziko lapansi. Tsopano ndine mwamuna wokwatira komanso mwamuna wa mkazi wokongola. Osati wokongola kokha, komanso wolimba mtima. Lodala tsiku limene ndinakumana nawe. Ndikupemphera kuti ukwati wathu udalitsidwe ndipo utibweretsere madalitso ambiri,” Michael anamuuza Lindah.

“Akanakhala nd munthu anandiuza kuti ndidzakwatiwa ndi mwana wa Purezidenti, ndikanati munthu ameneyo wapenga. Chaka chapitacho ndinali ndi pakati ndipo ndinali ndekha. Sindinali ndi mwamuna wondithandiza. Ndimangoganiza mmene ndingapulumukire mmoyou ndekha. Koma taonani lero. Ndakhala mkazi wa munthu. Osati wa munthu wamba koma wa mwana wa Purezidenti. Ndikuganiza kuti ndine mkazi wodalitsika kwambiri padziko lapansi,” Lindah anayankha ndi mmwetulo pankhope pake.

“Kupatula kukhala wodalitsika, ndiwe wolimbikira ntchito. Ndikuganiza kuti uyenera kulandira zabwino zonse chifukwa ngakhale dziko lonse litakusiya, iwe sunadzisiye wekha. Anthu atakuseka chifukwa chokhala ndi pakati uli kusukulu ya sekondale, iwe sunadziseke wekha. Atsikana ena akangokhala choncho amakhala opanda ntchito koma iwe unasankha kugwira ntchito molimbika. Ndine wamwayi kwambiri kukhala ndi mkazi ngati iwe,” anatero Michael.

“Ayi Michael, sukumvetsa. Ine ndine munthu wamwayi kwambiri. Ndinachita zolakwa zambiri paunyamata. Moyo wanga ukanawonongeka chifukwa cha zolakwikazo. Ndinachokera ku banja losauka koma tsopano ndatchuka chifukwa cha ana anga komanso chifukwa cha iwe. Ndikufuna kukuthokoza chifukwa chondipatsa mwayi wokhala mkazi wako. Ndikulonjeza kuti ndidzakhala mkazi wabwino, wodzichepetsa, waulemu komanso wolimbikira ntchito kuti titukule banja lathu limodzi,” anatero Lindah.

Anakumbatirana mwachikondi pansi pa kuwala kwa phwandolo. Patangopita nthawi pang’ono, inafika nthawi yodula keke ya ukwati ndipo anaitanidwa kutsogolo.

Keke ya ukwatiyo inali yayikulu kwambiri moti inali yayitali kuposa Lindah ndi Michael. Atayima kumbuyo kwake limodzi ndi anthu owafunira zabwino, anatenga mpeni ndipo ankafuna kuyamba kudula kekeyo.

Mwadzidzidzi, mfuti zinamveka.

Anali Dawood amene anawomba mfutizo mumlengalenga. Posakhalitsa anthu anamuwona ali mmalo a phwandowa atanyamula mfuti n’kuwaloza Lindah ndi Michael. Anthu ambiri anayamba kuthawa chifukwa cha mantha. Dawood anali atavala yunifolomu ya asilikali ndipo zimenezi zinamuthandiza kulowa m’malowo popanda kuletsedwa ndi alonda.

“Imani pomwepo! Mumaganiza kuti sindibwera? Mukuganiza kuti mukwatirana n’kumakasangalala pamene ine ndikuvutika? Ayi! Lero ndikuwonetsani mphamvu zanga!” Dawood anafuula.

Anawombanso mfuti mumlengalenga ndipo anthu ambiri anathawa.

“Unandilanda ana anga. Ndinakupatsa pakati ndipo wandikaniza kuti ndisamaone ana anga. Ndikufuna ana anga. Koma ngati ukufuna kuti ana anga akhala amwamuna wina, sudzakhala ndi mtendere. Ndidzakuonetsa pola mpaka kale” Dawood anatero mwaukali.

“Ndiwe munthu wolephera Dawood. Unandipatsa pakati kenako unandisiya. Sunasamale za ine kapena ana athu. Tsopano ukunamizira kuti ukuwafuna chifukwa wamva kuti ndinabereka,” Lindah anayankha molimba mtima.

Kenako Lindah anamuyandikira Dawood mopanda mantha.

“Anthu nonse, taonani munthu uyu. Ndi wamantha. Anandipatsa pakati ali mphunzitsi wanga kusukulu ya sekondale. M’malo mondisamalira ndi kundiphunzitsa, anangondipatsa pakati. Ndi munthu wopanda manyazi komanso wopanda udindo.”

Anthu onse anadabwa ndi kulimba mtima kwake.

“Samala pakamwa pako Lindah, apo ayi ndikuwonetsa kuti ndine mwamuna weniweni,” Dawood anatero.

“Khala chete Dawood. Mamuna weniweni sasiyira mkazi wake ndi ana ake mavuto. Wamuna weniweni amatenga udindo. Tsopano tandipatse mfutiyo!”

Chodabwitsa n’chakuti Dawood anamvera ndipo anapereka mfutiyo. Nene anatembenukira kwa achitetezo ndipo anawauza kuti amumange.

“mmoyo wako winawo, uzizaniza kawiri usanayesenso kundilepheretsa znthu zanga. Ndidzakhala ndikukugonjetsa nthawi zonse. Ine sindili ngati akazi ena. Ine ndine Lindah ndipo ndine wapaderadera,” anatero.

Anthu amene anatsala anayamba kumuwombera m’manja. Dawood anangoyima ngati mtengo pamene ankamangidwa.

“Kulimba mtima kotereku ndi chifukwa chake ndinakukwatira. Ndine wonyadira kwambiri chifukwa cha iwe, Lindah,” anatero Michael uku akukumbatirana.

Ndipo iwo anakhala osangalala mpaka kalekale.

KAPHULENI MBATATA

Osamaseweretsana ..munthu mukumuseweretsa leroyo simukudzwa mmawa tsogolo lake ndlotani ..izi ziimire mbali zonse relationship or friendship ..mmakoma nonsee...

Pangani follow Patricia 2 Frakeza

Kodi yakupezani kale ya "mkazi wanga anakanika kundipatsa mimba "? Ngati ndi ai ndilankhuleni ndithamanga ndi link ku in...
22/06/2026

Kodi yakupezani kale ya "mkazi wanga anakanika kundipatsa mimba "? Ngati ndi ai ndilankhuleni ndithamanga ndi link ku inbox kwanuko...

Komanso ndiika mu comment section 🥰🥰🥰

22/06/2026

Mkaziwangq anakanika kundiberekera mwana

Part 1🥳🥳🥳🥳

Mukuona ngati Salah akukonzekera kuti mmawali ?.....Steve apezadi mkaziwina ???

Khalani pompo pomwe drama yi Ikupitrira.....

Video ija tiiyamba lero!!!!🥳🥳🥳🥳Mwakonzeka ????"Mkazi wanga anakanika kundiberekera mwana "Ndione omwe ali ready kukwera ...
22/06/2026

Video ija tiiyamba lero!!!!🥳🥳🥳🥳

Mwakonzeka ????

"Mkazi wanga anakanika kundiberekera mwana "

Ndione omwe ali ready kukwera nane ngalawa🖐🖐🖐

Address

5 Buzzard Road Pelican Park
Pelican Park

Telephone

+27725816358

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Patricia 2 Frakeza posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share