16/10/2025
Ofesi yowona k*ti pasamakhale kusiyana pakati pa amayi ndi abambo ku Likoma yati amayi akukumana ndi nkhanza zochuluka m'bomali.
Izi ndimalingana ndi mulangizi mu ofesiyi a Emily Newa omwe ati ofesi yawo ikulandira ma ripoti komanso madandaulo kuchokera kwa amayi ochuluka omwe akuchitilidwa nkhanza.
"Madandaulo omwe tikulandira ndi kugonedwa ndicholinga chak*ti amayi agule nsomba kapena Usipa mosavuta, kuletsedwa mpata osonkhana ndi anzawo m'magulu abanki nkhonde komanso kusapatsidwa ndalama panyumba." Atero a Newa.
Iwo ati izi zikupita patsogolo kaamba koti m'boma la Likoma kulibe mabungwe olimbikitsa nkhani zamaufulu omwe amalimbikitsaso k*thana ndi nkhanza.
Poyankhapo m'modzi mwa amayi omwe amamenyelera ufulu wa amayi mdziko muno mayi Barbara Banda ati kukhala mzimayi sichifukwa kotero abambo asazunze amayiwa potengera mpata oti ndi Amayi.
Mayi Banda omwenso ndiwapampando wa amayi omwe amachita malonda mdziko muno wati amayi asamadziwonere pansi ndipo adziwonetsa chilungamo pomwe apatsidwa mpamba wochitira mabizinesi ndicholinga choti amuna awo adziwakhulupirira.
: Oliver Malibisa.