11/11/2025
BLANTYRE IRI NDI CHOKHUMBA PA MUNTHU YEMWE AKHALE MAYOR.
Aliyense amakhala ndichokhumba ndipo ife ngati anthu timafuna tiri ndi zabwino pa moyo umene tikukhala angakhalenso kawonekedwe ka dziko lathu timafuna kali kabwino.
Chomwe munthu wachikulire amawona atakhala, pena kumakhala kovuta kuti wachichepere achiwone angakhale ali wotalika mu usinkhu.
Nzeru ipambana zonse ndipo chibwana chimalanda nachipweteketsa dziko kamba ka anthu opusa, osawona patali ndi okonda ndalama.
Padakalipano tikamati tikufuna zinthu zabwino timayang'anira kuti anthu akudera apindula bwanji ndi atsogoleri omwe tikuwafuna.
Kwanthawi yaitali mzinda wathu wa Blantyre wakhala usakuyenda bwino kamba kakulephera kwa atsogoleri anthu a mzindawu.
Nthawi yomwe Blantyre imalozeka inali nthawi ya a Noel Chalamanda yemwe anali Mayor wa Mzinda wa Blantyre mbuyomu ndipo atangochoka mzindawu wasanduka wabwinja.
Mayor wa mzindawu kuyambira kuyambira pano akufunika akhale wamaphumziro abwino, okhala ndi ukadaulo wa utsogoleri, oziwa kuchita ziganizo zabwino, oziwa kulemba ndi kuwerenga, oziwa kuyankhula chizungu chomveka bwino, akhale wambiri yabwino ndi zina zotero.
Izi ndizofunikira kwambiri kamba koti kukhala Mayor umayimirira anthu ndipo pamafunika kumalemba makalata olumikizana ndi akuluakulu ochita malonda, makampani, kukumana ndi nthumwi zochokera mayiko akunja ndikulumikizana momveka bwino pa chitukuko cha mzinda komanso dziko.
Eric Mofolo atapimidwa bwinobwino zawonetsa kuti akukwanira kukhala Mayor ndipo akuluakulu ambiri mu mzinda wa Blantyre ali okondwa kwambiri.
Eric Mofolo ndi munthu olimbikira kwambiri, wambiri yabwino, ophunzira bwino, wagwira ntchito ngati owerengesera ndalama m'mawofesi aboma kwa dzaka 10 komanso wakhalapo wapampando ku mabungwe omwe amayang'anira zakawerengeseredwe ka ndalama angakhalenso kutsogolera makampani osiyanasiyana monga wamkulu.
Chiyembekezo cha athu a mzinda wa Blantyre ndichachikulu ndipo yemwe akuyenera kukhala Mayor wa mzindawu akuyeneranso kukhala ndi masomphenya akulu otukula mzindawu osati okonda masewera.
Eric Mofolo sazakukhumudwitsani akakhala Mayor wa Mzinda wa Blantyre.