17/09/2026
Katswiri ochita zisuzo zophunzitsa nkhani za Chipembezo za Chisilamu, Shaib Mustafa, yemwe amatchuka ndi dzina loti Mofolo wamwalira lero kutsatira ngozi ya galimoto yomwe yachitika pa Mbulumbuzi m'boma la Chiradzulu.
Kwaswiriyu wamwalilira ku Chipatala cha Zomba Central Hospital komwe adagonekedwa atavulala pa ngoziyo.
Malingana ndi ma report, thupi lake lilowa m'manda la Chisanu m'mudzi mwa Mpama kwa T/A Mpama m'boma lomwelo la Chiradzulu.
Olemba: Oscar Tauzi - 17/09/2026
Angoni Radio Station