23/08/2026
NYENGO M’SABATA IKUBWERAYI 24-30 AUGUST 2026
Kuyambira Lolemba mpaka Lachitatu, tiyembekezere nyengo yofunda, mitambo yapatalipatali, komanso mphepo nthawi
ya masana, koma nyengo yozizira usiku komanso m’mawa. Izi ndi kamba ka mphepo za chinyontho chochepa zochokera ku m’mwera chakumvuma m’nyanja ya mchere ya India
Nyengo ya chiperoni ikuyembekezereka kuyambira Lachitatu usiku kufikira Lachisanu. Choncho, kudzakhala nyengo ya mphepo,yozizira, mitambo yambiri, mvula yowaza komanso chifunga m’madera ena maka a chigawo chakummwera. Izi ndi kamba ka mphepo za chinyontho chochuluka zochokera ku m’mwera chakumvuma m’nyanja ya mchere ya India.
Loweruka ndi Lamulungu, kudzafunda maka nthawi yamasana ndipo kudzakhala kwa mitambo yapatalipatali madera ambiri chifukwa cha mphepo zofunda ndi za chinyontho chochepa kuchokera kumvuma.
Mphepo yamphamvu ya Mwera idziomba pa nyanja ya Malawi ndi nyanja zina. Choncho asodzi ndi ena ogwilitsa ntchito nyanja akhale osamalitsa ndipo apewe kulowa pa Nyanja.
© Department of Climate Change and Meteorological Services