04/05/2026
Zatsimikizika tsopano kuti timu ya Manchester United isewelanawo mu mpikisano wa UEFA Champions League itagonjesa timu ya Liverpool masana a lamulungu pa 3 May 2026 pa bwalo la Old Trafford Ku Mangalande.
Izi zadza pamene timuyi yakhala zaka zochuluka chiseweleleni mu mpikisanowu potsatila kusachita bwino.
Pakadali pano timuyi ili pa nambala yachitatu ndi mapoints okwana 64, kutsatira kugonjesa Liverpool yi ndizigoli zitatu kwa ziwiri m'masewera omwe anali opatsa chidwi.
Masewerowa asanachitike mphuzitsi wakale watimuyi Sir Alex Ferguson anagwa koma atawapima ku kuchipatala madotolo atsimikiza kuti akupeza bwino.
Date: 03/05/2026
Wolemba: Promise Peter