Mpebros TV

Mpebros TV Mpebros TV is Independent media TV which its aim is to proclaim the gospel of our Lord Jesus Christ.

Mpebros TV is just giving best wishes to all Regional women's camps for Seventh Day Baptist across the Malawi.
26/07/2026

Mpebros TV is just giving best wishes to all Regional women's camps for Seventh Day Baptist across the Malawi.

26/07/2026
25/07/2026

BIWI JOINT SENIOR YOUTH CHOIR

25/07/2026

THE JEWS
BIWI SDB CHURCH

 HERITAGE CARE FOUNDATION YAKHAZIKITSIDWA  KU MANGOCHI Anyamata awiri, Francis Mpezeni ndi Jonathan Khangaiwa, akhazikit...
25/07/2026



HERITAGE CARE FOUNDATION YAKHAZIKITSIDWA KU MANGOCHI

Anyamata awiri, Francis Mpezeni ndi Jonathan Khangaiwa, akhazikitsa bungwe lotchedwa Heritage Care Foundation, lomwe lakhazikitsidwa ndi cholinga chothandiza achikulire pa moyo wawo wa uzimu komanso wa kuthupi.

Poyambitsa ntchito za bungweli lero m'mudzi mwa Bauleni, m'boma la Mangochi, Heritage Care Foundation yathandiza anthu achikulire okwana 20 powapatsa zinthu zofunika pa moyo wawo wa tsiku ndi tsiku monga sopo, mchere komanso machesi.

Mmodzi mwa akuluakuku oyambitsa bungweli, Francis Mpezeni, wati cholinga cha Heritage Care Foundation ndi kuthandiza achikulire omwe nthawi zambiri amakumana ndi mavuto chifukwa chosowa zinthu zofunika pa moyo wawo komanso kuwalimbikitsa pa moyo wa chikhulupiriro.

"Takhazikitsa Heritage Care Foundation kuti likhale chiyambi cha ntchito yothandiza achikulire osati kuwapatsa zinthu zokha, komanso kuwalimbikitsa pa moyo wa uzimu kuti azikhala ndi chiyembekezo," watero Mpezeni.

Mmodzi mwa omwe alandira thandizoli, Sandy Hussein, yemwenso ndi mfumu ya mudzi wa Bauleni, wayamikira kwambiri ntchito yomwe Heritage Care Foundation yayambitsa.

Hussein walimbikitsanso Francis Mpezeni ndi Jonathan Khangaiwa kuti asataye mtima kapena kusiya ntchito yabwinoyi panjira, koma kuti apitirize kuthandiza achikulire chifukwa anthu ambiri okalamba amakumana ndi mavuto a kusowa kwa zinthu zofunikira pa moyo wawo wa tsiku ndi tsiku.

Anthu a m'derali akukhulupirira kuti Heritage Care Foundation ikhala chiyambi cha kusintha miyoyo ya achikulire ambiri m'boma la Mangochi komanso m'madera ena a dziko lino ngati ingathathandizidwe ndi anthu komaso mabungwe osiyanasiyana a mdziko muno ingakhale mayiko ena.

Sabata labwino kwa inu nonse kuchokera ku Mangochi Seventh Day Baptist church Maola asabata tikufunirani mtendere opamba...
24/07/2026

Sabata labwino kwa inu nonse kuchokera ku Mangochi Seventh Day Baptist church

Maola asabata tikufunirani mtendere opambana komaso chisogozo chabwino kwa inu nonse pamene mukupuma pasiku limeneli

Werengani Eksodo 20:8-11
khalani mu mpumulo wa Ambuye kulikonse komwe muli.

17/07/2026

Happy Sabbath from Mbayani SDB Young Chithangato

16/07/2026

CHORAL SABBATH FOR CENTRAL REGION SDB YOUTH
CONDUCTED AT MWATIBU PRIMARY SCHOOL, NANTHENJE, LILONGWE.

5th April, 2026

Achinyamata akuyesesa kukwatira momuno asikana akapezeka wa mu mpingo momuno musamaleni Sabata yathawi kunali maukwati a...
10/07/2026

Achinyamata akuyesesa kukwatira momuno asikana akapezeka wa mu mpingo momuno musamaleni

Sabata yathawi kunali maukwati atatu Achinyamata ampingo wathu omwe uno.

palibe zovuta apa tiyeni tipitilize ndithu

Awa ndi maukwati achitika sabata ino maboma a Ntcheu,Lilongwe, ndi Blantyre.

Address

Mbayani
Blantyre
0996706309

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Mpebros TV posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Business

Send a message to Mpebros TV:

Shortcuts

Share

Category