22/08/2026
Mighty Wanderers yabwereranso pamwamba pa m'ndandanda wamatimu osewera mu FDH Bank Premiership pomwe itagonjetsa Red Lions 2-1 pa bwalo la Mpira ku Chiwembe mu nzinda wa Blantyre.
Clement Nyondo komanso Mphatso Kamanga anagoletsera Wanderers, ndipo Shukurani M***a anamwetsa chigoli chopukutira misozi kwa anyamata a Red Lions.
Wanderers ikutsogola ndi mapointi 29 pamene kwangotsala masewero amodzi kuti ligiyi ifike kumapeto kwa gawo loyamba.