
06/06/2025
AZIBAMBO OFOOKA AMATHAMANGIRA AZIMAYI AMPHAMVU KOMANSO OLIMBIKIRA
Alipo Azibambo omwe analeredwa mopyorera kapena moonjeza ndi Mai awo. Azibambo achonchi kukula kumawavuta.
Ngakhale awirikize ku gym, limakula ndi thupi koma osati kaganizidwe.
Azibambo ofooka amakhala ndi chikoka ndi Azimai a tough, a rough, olimbikira ma business komanso opata. Izi zimachitika chifukwa analeledwa pachinena. Mavuto sawadziwa. Anazolowera kuyeyekedwa. Zotsatira zake, amamusiya Mkazi k*ti awalerenso ngati momwe amkachitira Mai awo.
Izi ndi zina mwa zizindikiro za Amuna achikazi:
1. Amakanika kumusamala Mkazi ngakhale k*thekera atakhala nako. Iwowo amakhala pa mtambasale basi kudikira k*ti Mkazi alongosola chilichonse malingana ndi momwe amkachitira Amai awo.
2. Amakanika k*tsogolera Mkazi. Chili chonse amadikira afunsire nzeru kwa Mkazi wawo komanso amakanika kupanga chinthu chooneka paokha opanda k*tsogoleredwa ndi Mkazi wawo.
3. Akakhumudwa amadikira Mkazi wawo awanyengerere k*ti ayanjanenso. Iwowa samatha kulongosola komanso kukonza nkhani. Mkazi qawo amamutenga ngati kholo lawo.
4. Amanyanyala pakakhala zakudya zosakhala bwino chonsecho sanasonkhe yandiwo. Amakhumudwa Mkazi akangoyankhula ndi Mamuna wina ngakhale ali waku mpingo. Izi zimachitika chifukwa iwowa ndi ofewa ndipo Mkazi wawo ndi kholo lawo.
5. Ukawauza k*ti mwina mungosiyana, amakuopsyeza k*ti azipha olo amalira ngati mwana kufikira utawamvera chisoni.