02/06/2026
AZIBAMBO TABWERANI TIKUTSINENI KHUTU.
Pamene mkazi wayamba kuganiza zopanga cheat Mamuna wake, makhalidwe ake amayamba kusintha pangâono Ndi pangâono mânjira izi:
-Amayamba kuchita zinthu ngati munthu wodziyimira pa yekha mopitirira muyeso.
Sikuti kudziyimira pawokha nâkoipa, koma nthawi zambiri zimasonyeza kuti mtima wake wayamba kuchoka pa banjalo.
-Amakhala munthu womasuka komanso wachikondi kwa anthu ena, koma osati kwa mwamuna wake.
Anthu akunja amalandira msangala wake, pomwe mwamuna wake amalandira ma left overs amsangala .
-Amayamba kusasamala kutaya chikhulupiriro cha mwamuna wake.
Kusintha kumeneku nthawi zambiri kumayamba kusonyeza kuti zinthu zazikulu zikubwera mtsogolo.
-Amayamba kusintha momwe amaonera mbiri ya banja lawo.
Zaka zabwino zimayiwalika, koma zolakwa Zako zakale zimangobwerezedwa nthawi zonse.
-Amayamba kusangalatsidwa kwambiri ndi zinthu zakunja kwa banja.
Koma akakhala ndi mwamuna wake amaoneka ngati munthu wosafuna kuyandikira kapena kulumikizana naye.
-Kuyamikira kwa mwamuna wake kumachepa, koma kudzudzula kumachuluka.
Mkazi akafuna kuku cheater, zimakhala zosavuta kuona zolakwa zokha za mwamuna wake.
-Amayamba kuyerekezera mwamuna wake ndi amuna ena.
Nthawi zina amalankhula poyera, koma nthawi zina zimangokhala mumtima mwake.
-Amasiya chidwi chokonza mavuto a mâbanja.
Mkazi amene akuganiza zochoka nthawi zambiri safunanso kugwiritsa ntchito mphamvu kukonza Banja lake.
-Amasiya kugawana nawe zinthu za tsiku lake.
Kulumikizana kwa mumtima kumayamba kupita kwa munthu wina pangâono ndi pangâono.
-Amakhala munthu woteteza kwambiri zachinsinsi zake/fone Ndiye siungayigwire nkomwe.
Zinthu zimene kale zinkakhala zotseguka zimayamba kukhala âsi nkhani yako/siziku kukhudza .â
-Amayamba kuchotsa mtima wake pa iwe, (emotional distance) asanachite china chilichonse.
Nthawi zambiri cheating imayambira mumaganizo ndi mumtima, zisanasanduke zenizeni.
Azibambo mukakhala omvetsetsa,
Muyamba kuona Ma red flags b4 kuchitika ZENI ZENI zo.