30/07/2025
NTHANGA ZA MAUNGU NDI ZINC
✓Abambo bwerani ticheze pang'ono sizochititsa manyazi izi.
✓Abambo ambiri akukumana ndi vuto la kuchepa kwa zinc m'thupi komwe kukukhudzanso mbali yawo ya ubereki ndi kulephera kuchipinda.
✓Zinc akachepa chonde nacho chimachepa kamba koti umuna ukhoza kupangika ochepa, opanda mphamvu komanso osakhala bwino.
✓Mbali ina ndiyoti chidwi choti akhale pamodzi mkazi wake chimachepa komanso pena chiwalo cha ubereki sichidzuka bwino. Mphamvu zeni zeni sizioneka.
✓Ngati ndi choncho ayi musavutike abambo. Thanzi labwino ndi lomwe likufunika.
✓Lingalirani za zinc. Lingalirani za nthanga za maungu zomwe ziri ndi mlingo wabwino wa zinc.
✓Pezani nthanga za maungu ndipo muntha kukazinga ndi kupanga powder. Sakanizani ndi moringa ndipo mudziika tiyi supuni imodzi m'phala. Muzidya tsiku ndi tsiku kwa miyezi itatu.
✓Mukhozanso kutsira nthanga za maungu musaladi ndi kudyera limodzi kapena kutafuna tebulo supuni imodzi ya nthanga zimenezi pa tsiku.
✓Nthanga za maungu zirinso ndi amino acid itchedwa kuti "L- Arginine," yemwe amathandiza kuti umuna uzipangika ochuruka bwino komanso wa kolite (quality)
✓Naye zinc amathandiza kuti chilako lako chokhala pamodzi NDI akazi anu chikule.