17/07/2025
KIDNEY STONES ( miyala yamu impso)
✓iyi ndi miyala yomwe imatha kupezeka nkati mwa kidney(impso) yanu. Miyalayi ndi michere( salts & minerals) yomwe yaundana pamodzi. Miyalayi imatha kukhala ing'ono ing'ono ngati mchenga pena ngati kabulu kachimanga
✓ miyala yamu impso imapangidwa pamene mu mkodzo wanu muli michere yambiri( eg calcium, oxalate uric acid kuposa madzi omwe angasungunule michereyo
KODI CHIMAYAMBISA MIYALAYI NDICHANI?
✓ kuchepekela Kwa madzi m'thupi; ichi ndichoyambisa chachikulu, ngati simukumwa madzi okwanila ndekuti mikozo yanu ikhala ndi michere yambiri kuposa madzi zomwe zipangise kuti michere ija yiundane pamodzi ndikupanga miyala
✓ madyedwe; kudya zakudya za mchere kwambiri, sugar komaso red meat( nyama ya mbuzi or ya ng'ombe kwambiri)
✓ngati m'banja mwanu alipo kapena Kwa makolo anu aliko anadwalapo, pamakhalaso ka mwayi koti inuso m***a kudwala
✓kunenepa koonjeza kumasoneza mlingo wa uric acid amene atha kuyambisaso miyala yamu impso
✓makhwala ena atha kuyambisaso miyala monga ma diuretics, ma antibiotics ena komaso ma antacid omwe amakhala ndi calcium
ZIZINDIKILO ZA KIDNEY STONES
✓ Kupweteka ku nsana mmusi, pansi pa mimba pamene kupwetekekaku kumazayendelera kufika m'mphechepeche( m'ma groin)
Kumva kupweteka mukamakoza
✓kufuna kukonza pafupipafupi
✓ kukonza mikozo ya magazi
✓mikozo yotulusa fungo
✓kumva nseru komaso kusanza
✓ thupi kutentha/ kumva kuzizizdwa
KODI TINGAPEWE BWANJI MA KIDNEY STONES?
✓ Kumwa madzi pafupipafupi ( 2-3 liters pa tsiku) kuonesesa kuti mikozo yanu ikale ya pale yellow kapena ya clear( yopanda mtundu), dziwani kuti tea komaso coffee atha kuyambisaso ma kidney stones ndikunenawa
NOTE; lemon juice amathandiza kuti michere isapangidwe m'ma ipso athu
✓kuthila mchere wamlingo wabwino
✓kuchepesa kudya nyama tafotokoza( red meat, madzira)
✓ chepesani thupi pamene mukuona kuti weight yanu yakwela
✓chepesani kumwa makhwala musanaonane ndi dokotala
Dziwani kuti pamene miyalayi ili yaying'ono itha kusungunuka ngati mukumwa madzi moyenelera
Mukaona zizindikilo tanenazi ndibwino kupita kuchipatala mwachangu
NGATI MWAPINDULA NAWO UTHENGAWU ITANANI ANZANU APANGE FOLLOW Mupacho